Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Koma ukalabadiradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanena,+ pamenepo ndidzalusira adani ako ndi kuvutitsa okuvutitsa.+

  • Yesaya 33:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Tsoka iwe amene ukulanda zinthu koma iweyo osalandidwa. Tsoka kwa iwe amene ukuchita zachinyengo pamene ena sanakuchitire zachinyengo.+ Ukadzangomaliza kulanda, nawenso udzalandidwa.+ Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwonso adzakuchitira zachinyengo.+

  • Yesaya 41:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Taona! Onse okupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+ Anthu amene akukangana nawe sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.+

  • Yeremiya 10:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu+ amene akunyalanyazani,+ ndi pa mafuko amene sakuitana padzina lanu.+ Pakuti iwo adya Yakobo.+ Amudya ndipo akupitirizabe kumuwononga.+ Malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+

  • Yeremiya 25:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova.

  • Yeremiya 50:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 “Babulo muitanireni oponya mivi ndi uta, onse okunga uta.+ Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa.+ Mubwezereni zimene anachita.+ Muchitireni zonse zimene iye anachita.+ Iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova, pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena