15 Chotero iye anatengera Yehoyakini+ ku Babulo.+ Anatenga ku Yerusalemu mayi a mfumuyo,+ akazi ake, nduna za panyumba yake,+ ndi akuluakulu a m’dzikolo, n’kuwapititsa ku Babulo.
7 ‘Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna za panyumba+ ya mfumu ya ku Babulo.’”+
13 Ine ndidzamutambasulira ukonde wanga. Chotero iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira+ ndipo ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi.+ Koma iye sadzaliona ndipo adzafera komweko.+
3 Ndiyeno mfumu inauza Asipenazi, mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu+ kuti abweretse ena mwa ana a Isiraeli, ana a m’banja lachifumu, ndi ana a anthu olemekezeka,+