4 Iwo adzachita mantha chifukwa cha tsiku limene likubwera. Tsikuli ndi lofunkha zinthu za Afilisiti+ onse ndi kupha wopulumuka aliyense wothandiza+ Turo+ ndi Sidoni.+ Pakuti Yehova adzafunkha zinthu za Afilisiti+ amene atsala ochokera pachilumba cha Kafitori.+
8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa ana a Yuda.+ Ana a Yudawo adzawagulitsa kwa amuna a ku Sheba,+ mtundu wa anthu akutali.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.