Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 21:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+

  • 2 Mafumu 24:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 komanso chifukwa cha magazi osalakwa+ amene iye anakhetsa, moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa, ndipo Yehova sanalole kukhululuka.+

  • Yeremiya 2:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Komanso, pazovala zako papezeka madontho a magazi a anthu+ osauka osalakwa.+ Madontho a magaziwo sindinawapeze panyumba, ngati kuti anali kuthyola nyumbayo, koma ndawapeza pazovala zako zonse.+

  • Yeremiya 22:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’

  • Ezekieli 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+

  • Ezekieli 11:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Inuyo mwapha anthu ambiri mumzindawu komanso mwadzaza misewu yake ndi anthu ophedwa.”’”+

  • Hoseya 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kutembererana,+ kuchita zachinyengo,+ kuphana,+ kuba,+ ndi chigololo+ zafala m’dzikoli, ndipo kukhetsa magazi kukuchitika motsatizanatsatizana.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena