Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+

  • Nehemiya 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+

  • Salimo 65:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Zolakwa zanga zandikulira.+

      Inu mudzatikhululukira* machimo athu.+

  • Salimo 86:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+

      Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.+

  • Yesaya 1:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.

  • Yesaya 44:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndidzafafaniza zolakwa zako ngati kuti ndaziphimba ndi mtambo,+ ndi machimo ako ngati kuti ndawaphimba ndi mitambo yambiri. Bwerera kwa ine,+ ndipo ine ndikuwombola.+

  • Yeremiya 50:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+

  • Danieli 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo+ ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena