Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndidzaika+ chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ ndi pakati pa mbewu yako+ ndi mbewu yake.+ Mbewu ya mkaziyo+ idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe+ udzaivulaza chidendene.”+

  • Salimo 22:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Koma ine ndine nyongolotsi+ osati munthu.

      Anthu amanditonza ndipo ndine wonyozeka kwa anthu.+

  • Yesaya 50:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+

  • Yesaya 53:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+

  • Danieli 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+

      “Gulu lankhondo la mtsogoleri amene akubwera lidzawononga+ mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyera amenewo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira, ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mulungu wagamula kuti padzakhale chiwonongeko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena