Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 29:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 ine ndidzachitanso zodabwitsa ndi anthu awa.+ Ndidzazichita m’njira yodabwitsa, pogwiritsira ntchito chinthu chodabwitsa. Nzeru za anthu awo anzeru zidzatha, ndipo kumvetsetsa zinthu kwa anthu awo ozindikira kudzabisika.”+

  • Mateyu 11:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+

  • Mateyu 13:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake.+

  • Yohane 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano maziko operekera chiweruzo ndi awa, kuwala+ kwafika m’dziko+ koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala,+ pakuti ntchito zawo n’zoipa.

  • Machitidwe 28:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma osazindikira ngakhale pang’ono. Kupenya mudzapenya ndithu, koma osaona ngakhale pang’ono.+

  • Aroma 1:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ndiponso monga mmene iwo sanafunire kumudziwa Mulungu molondola,+ iye anawasiya ndi maganizo awo oipa,+ kuti azichita zinthu zosayenerazo,+

  • 2 Petulo 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Munthu amene alibe zinthu zimenezi ndi wakhungu, wotseka maso ake kuti asaone kuwala,+ ndipo waiwala+ kuti anayeretsedwa+ ku machimo ake akale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena