Masalimo
Nyimbo ya Davide.
141 Inu Yehova, ine ndakuitanani.+
Bwerani kwa ine mofulumira.+
Tcherani khutu pamene ndikukuitanani.+
2 Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza+ pamaso panu,+
Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+
4 Musachititse mtima wanga kukonda choipa chilichonse,+
Kuti ndisamachite zinthu zoipa zonditchukitsa,+
Pamodzi ndi amene amachita zinthu zopweteka anzawo,+
Kuti ndisadye chakudya chawo chapamwamba.+
5 Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+
Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+
Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+
Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+
6 Oweruza awo awagwetsera pansi m’mphepete mwa thanthwe,+
Koma anthu awo amva zonena zanga ndipo aona kuti ndi zabwino.+
7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,
Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+
8 Koma ine maso anga ali pa inu+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+
Ndathawira kwa inu.+
Musalole kuti moyo wanga uwonongeke.+