Deuteronomo
26 “Ndiyeno ukakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa chako, n’kulitenga kukhala lako ndi kukhalamo,+ 2 ukatenge zina mwa zipatso zoyambirira+ pa zipatso zonse za m’munda mwako zimene udzakolola m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. Ukaziike m’dengu ndi kupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuika dzina lake.+ 3 Uzikapita kwa wansembe+ amene azidzatumikira masiku amenewo ndi kumuuza kuti, ‘Ndikuvomereza lero pamaso pa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowadi m’dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa.’+
4 “Wansembeyo azikalandira dengulo m’manja mwako ndi kuliika pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wako. 5 Pamenepo uzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Bambo anga anali Msiriya+ wotsala pang’ono kufa. Anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa chabe+ a m’banja lake kukakhala kumeneko monga mlendo, koma anakhaladi mtundu waukulu ndi wamphamvu kumeneko.+ 6 Ndipo Aiguputo anayamba kutichitira zoipa, kutizunza ndi kutigwiritsa ntchito yowawa yaukapolo.+ 7 Pamenepo tinayamba kufuulira Yehova Mulungu wa makolo athu,+ ndipo Yehova anamva mawu athu+ ndi kuona nsautso yathu, mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu.+ 8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula,+ zoopsa zazikulu,+ zizindikiro ndi zozizwitsa.+ 9 Ndiyeno anatibweretsa kumalo ano ndi kutipatsa dziko ili, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za m’dziko limene Yehova anandipatsa.’+
“Pamenepo uzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kugwada pamaso pa Yehova Mulungu wako.+ 11 Uzikasangalala+ chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wako wapatsa iwe ndi nyumba yako, zimene wapatsa iweyo komanso Mlevi ndi mlendo wokhala pakati panu.+
12 “Ukamaliza kusonkhanitsa chakhumi chonse+ cha zokolola zako m’chaka chachitatu,+ chaka chopereka chakhumi, uzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye. Amenewa azidzadya ndi kukhuta chakhumicho m’mizinda yanu.+ 13 Ukatero uzidzanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Ndachotsa chinthu chopatulika m’nyumba mwanga ndi kuchipereka kwa Mlevi, mlendo wokhala pakati pathu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Ndachita zimenezi mogwirizana ndi malamulo onse amene munandipatsa. Sindinaphwanye malamulo anu kapena kuwaiwala.+ 14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nyengo yanga yakulira, kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka gawo lake chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga. Ndachita mogwirizana ndi zonse zimene munandilamula. 15 Yang’anani pansi kuchokera kumwamba, kumalo anu oyera okhalako,+ ndipo mudalitse anthu anu Aisiraeli+ ndi dziko limene mwatipatsa, dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ monga mmene munalumbirira makolo athu.’+
16 “Lero Yehova Mulungu wanu akukulamulani kutsatira malangizo ndi zigamulo+ zimenezi. Motero muzisunga ndi kutsatira zimenezi ndi mtima wanu+ wonse ndi moyo wanu wonse.+ 17 Inu lero mwachititsa Yehova kunena kuti adzakhala Mulungu wanu mukamayenda m’njira zake ndi kusunga malangizo,+ malamulo+ ndi zigamulo zake+ ndiponso kumvera mawu ake.+ 18 Ndipo lero Yehova wakuchititsani kunena kuti mudzakhala anthu ake, chuma chapadera,+ monga mmene anakulonjezerani,+ ndiponso kuti mudzasunga malamulo ake onse, 19 ndi kuti adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga.+ Zimenezi zidzakudzetserani chitamando, mbiri yabwino ndi kukongola, mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu,+ monga mmene anakulonjezerani.”