Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 17
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Machitidwe

      • Paulo ndi Sila ku Tesalonika (1-9)

      • Paulo ndi Sila ku Bereya (10-15)

      • Paulo ku Atene (16-22a)

      • Zimene Paulo analankhula kubwalo la Areopagi (22b-34)

Machitidwe 17:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 2:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 133

Machitidwe 17:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 9:19, 20; 13:13, 14; 14:1; 18:4
  • +Mac 18:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 134-135

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 19

    12/1/2008, tsa. 30

    3/1/1986, tsa. 29

    Sukulu ya Utumiki, ptsa. 251-252

Machitidwe 17:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 22:7; 34:20; 69:21; 118:22; Yes 50:6; 53:3, 5
  • +Sl 16:10; Lu 24:45, 46

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 134-135

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 19

    12/1/2008, tsa. 30

    6/15/1990, ptsa. 17-18

    Galamukani!,

    4/8/1993, tsa. 21

Machitidwe 17:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 15:22, 40

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 135

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 19

    11/1/1997, tsa. 11

Machitidwe 17:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 13:45

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 135-136, 139

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 19

Machitidwe 17:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 16:19-21

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 135-136

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, ptsa. 19-20

    6/1/1993, tsa. 3

Machitidwe 17:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Lu 23:1, 2; Yoh 19:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 135-136

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 20

Machitidwe 17:9

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “ndalama za belo.”

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 136

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 20

Machitidwe 17:10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 136-137

Machitidwe 17:11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 137-138

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 2

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/2011, tsa. 25

    4/15/2007, ptsa. 14-15

    10/15/1998, tsa. 6

    5/15/1996, ptsa. 16-17

    8/15/1990, tsa. 29

    6/15/1990, tsa. 18

    8/1/1989, tsa. 6

    1/15/1989, tsa. 6

    Galamukani!,

    3/2008, ptsa. 8-9

    8/2007, ptsa. 10-11

    10/8/1991, ptsa. 12-13

Machitidwe 17:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 14:2, 19

Machitidwe 17:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 10:23

Machitidwe 17:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 16:1, 2; 1At 3:2

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/2004, tsa. 19

    6/15/1990, tsa. 18

Machitidwe 17:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 140

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/1998, ptsa. 26-27

    2/15/1989, tsa. 5

Machitidwe 17:17

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 140-141

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 18

Machitidwe 17:18

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 5:28, 29; 11:25; 1Ak 15:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 141-142

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2003, tsa. 22

    8/1/2001, tsa. 8

    7/15/1998, ptsa. 25, 27

    6/15/1990, tsa. 18

    6/15/1989, tsa. 4

    2/15/1989, ptsa. 5-6

Machitidwe 17:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Baibulo la Dziko Latsopano (nwt), tsa. 2137

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 18

    2/15/1989, ptsa. 5-6

Machitidwe 17:21

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Galamukani!,

    3/2011, tsa. 18

Machitidwe 17:22

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “ndinu opembedza kwambiri.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 17:33, 34
  • +Mac 17:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Muzikonda Anthu, lesson 5

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 142-143

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 30

    9/1/2007, tsa. 14

    2/15/1989, ptsa. 6-7

    3/1/1986, tsa. 30

    Sukulu ya Utumiki, tsa. 252

Machitidwe 17:23

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Muzikonda Anthu, lesson 5

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 143

    Nsanja ya Olonda,

    3/1/2012, tsa. 18

    7/15/2010, tsa. 30

    7/15/2002, tsa. 32

    2/15/1989, ptsa. 6-7

    Galamukani!,

    3/2011, tsa. 18

    Mawu a Mulungu, tsa. 64

Machitidwe 17:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Mf 8:27
  • +Sl 146:6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 144

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 30

    7/1/2008, tsa. 10

    2/15/1989, ptsa. 7-8

Machitidwe 17:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 50:12
  • +Yes 42:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 144

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 38

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 30

    7/1/2008, tsa. 10

    2/15/1989, ptsa. 7-8

Machitidwe 17:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ge 5:2
  • +Ge 1:28
  • +De 2:5, 19; 32:8; Sl 74:17

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri, article 64

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 144-145

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 30

    7/1/2008, tsa. 10

    9/15/1998, ptsa. 11-12

    6/15/1990, tsa. 18

    2/15/1989, ptsa. 8-9

    5/15/1988, tsa. 10

    Buku la Onse, ptsa. 24-25

    Galamukani!,

    9/8/1993, tsa. 9

Machitidwe 17:27

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +De 4:29; Sl 145:18; Aro 1:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 145

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 30

    7/1/2008, tsa. 10

    2/15/1989, tsa. 9

Machitidwe 17:28

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “mbadwa zake.”

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 146

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 38

    Galamukani!,

    3/2011, tsa. 18

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, ptsa. 30-31

    6/15/2004, tsa. 14

    2/15/1989, ptsa. 9-10

    3/1/1986, tsa. 30

Machitidwe 17:29

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ge 1:27
  • +De 5:8; Yes 37:19; 40:18-20; 46:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 146

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, ptsa. 30-31

    1/15/2004, tsa. 32

Machitidwe 17:30

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aef 4:17, 18

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 146-147

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 31

    7/1/1992, tsa. 32

    2/15/1989, ptsa. 10-11

Machitidwe 17:31

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 96:13; 98:9; Yoh 5:22; Mac 10:42
  • +Yoh 11:25; Mac 2:24; 13:32, 33

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 147

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 31

    1/15/2008, tsa. 20

    7/1/1992, tsa. 32

    6/15/1990, tsa. 18

    6/15/1989, tsa. 7

    2/15/1989, ptsa. 11-15

    3/1/1987, tsa. 32

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 296

    Kukhala ndi Moyo Kosatha, tsa. 175

Machitidwe 17:32

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 1:23

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 147

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 31

    7/1/1998, tsa. 12

Machitidwe 17:34

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2010, tsa. 31

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Mac. 17:11At 2:1
Mac. 17:2Mac 9:19, 20; 13:13, 14; 14:1; 18:4
Mac. 17:2Mac 18:19
Mac. 17:3Sl 22:7; 34:20; 69:21; 118:22; Yes 50:6; 53:3, 5
Mac. 17:3Sl 16:10; Lu 24:45, 46
Mac. 17:4Mac 15:22, 40
Mac. 17:5Mac 13:45
Mac. 17:6Mac 16:19-21
Mac. 17:7Lu 23:1, 2; Yoh 19:12
Mac. 17:13Mac 14:2, 19
Mac. 17:14Mt 10:23
Mac. 17:15Mac 16:1, 2; 1At 3:2
Mac. 17:18Yoh 5:28, 29; 11:25; 1Ak 15:12
Mac. 17:22Mac 17:33, 34
Mac. 17:22Mac 17:16
Mac. 17:241Mf 8:27
Mac. 17:24Sl 146:6
Mac. 17:25Sl 50:12
Mac. 17:25Yes 42:5
Mac. 17:26Ge 5:2
Mac. 17:26Ge 1:28
Mac. 17:26De 2:5, 19; 32:8; Sl 74:17
Mac. 17:27De 4:29; Sl 145:18; Aro 1:20
Mac. 17:29Ge 1:27
Mac. 17:29De 5:8; Yes 37:19; 40:18-20; 46:5
Mac. 17:30Aef 4:17, 18
Mac. 17:31Sl 96:13; 98:9; Yoh 5:22; Mac 10:42
Mac. 17:31Yoh 11:25; Mac 2:24; 13:32, 33
Mac. 17:321Ak 1:23
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
  • 30
  • 31
  • 32
  • 33
  • 34
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe 17:1-34

Machitidwe a Atumwi

17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa mʼsunagogemo ndipo kwa milungu itatu anakambirana nawo mfundo za mʼMalemba.+ 3 Iye ankafotokoza ndiponso kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti zinali zoyenera kuti Khristu avutike,+ kenako auke.+ Ankanena kuti: “Yesu amene ndikumulalikira kwa inu, ndiye Khristu.” 4 Pamapeto pake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Agiriki ambiri opembedza Mulungu komanso azimayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.

5 Koma Ayuda anachita nsanje+ ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa nʼkuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse nʼkuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo. 6 Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa, amene ayambitsa mavuto kwina konseku, tsopano akupezekanso kuno.+ 7 Ndipo Yasoni wawalandira ngati alendo ake. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Eti akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.”+ 8 Atanena mawu amenewa, gulu la anthu lija komanso olamulira a mzindawo anakwiya kwambiri. 9 Olamulira a mzindawo analipiritsa Yasoni ndi enawo ndalama,* kenako anawamasula.

10 Kutangoda, abale anatulutsa Paulo ndi Sila nʼkuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko, analowa mʼsunagoge wa Ayuda. 11 Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona. 12 Ambiri mwa anthu amenewa anakhala okhulupirira, chimodzimodzinso akazi ndi amuna ena otchuka a Chigiriki. 13 Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atamva kuti Paulo akufalitsanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko kukachititsa anthu kuti akwiyire atumwiwo nʼkuyambitsa chipolowe.+ 14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo kuti apite kunyanja.+ Koma Sila ndi Timoteyo anatsala komweko. 15 Ndipo anthu amene anaperekeza Paulo anakamufikitsa ku Atene. Koma anabwerera atatumidwa kuti akauze Sila ndi Timoteyo+ kuti atsatire Pauloyo mwamsanga.

16 Pamene Paulo ankawayembekezera ku Atene, mtima unamuwawa kwambiri poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano. 17 Atalowa mʼsunagoge anayamba kukambirana ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirananso ndi anthu amene ankawapeza pamsika. 18 Koma anthu ena anzeru za Epikureya ndi Sitoiki anayamba kutsutsana naye. Ena ankanena kuti: “Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?” Pomwe ena ankanena kuti: “Akuoneka kuti akulalikira za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa chakuti Paulo ankalengeza uthenga wabwino wa Yesu ndi za kuuka kwa akufa.+ 19 Choncho anamugwira nʼkupita naye kubwalo la Areopagi nʼkumuuza kuti: “Kodi tingadziweko za chiphunzitso chatsopano chimene ukuphunzitsachi? 20 Chifukwatu zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo mʼmakutu mwathu. Ndiye tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21 Ndipotu anthu onse a ku Atene ndi alendo ogonera kumeneko, ankathera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani zatsopano. 22 Tsopano Paulo anaima pakati pa bwalo la Areopagi+ nʼkunena kuti:

“Inu anthu a ku Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambiri milungu* kuposa mmene ena amachitira.+ 23 Mwachitsanzo, pamene ndimadutsa nʼkumayangʼanitsitsa zinthu zimene mumalambira, ndapezanso guwa lansembe lolembedwa kuti, ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Choncho ine ndikulalikira kwa inu za Mulungu wosadziwika amene mukumulambirayo. 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 25 Komanso satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu,+ chifukwa ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya+ ndi zinthu zonse. 26 Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anaika nthawi yoti zinthu zina zizichitika komanso anaika malire a malo oti anthu azikhala.+ 27 Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze nʼkumupezadi,+ ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 Paja chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo, ngati mmene andakatulo anu ena ananenera kuti, ‘Paja ndife ana ake.’*

29 Choncho, popeza ndife ana a Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa ndi anthu aluso.+ 30 Nʼzoona kuti Mulungu analekerera nthawi yomwe anthu sankadziwa zinthu,+ koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape. 31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ mwachilungamo dziko lonse lapansi, kudzera mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”+

32 Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka mwachipongwe,+ pomwe ena anati: “Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.” 33 Choncho Paulo anawasiya. 34 Koma anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza mʼbwalo la Areopagi, mayi wina dzina lake Damarisi komanso anthu ena.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena