Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Chotero ana a Isiraeli anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anayamba kutumikira Abaala+ ndi mizati yopatulika.+

  • Oweruza 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Zitatero, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ zifaniziro za Asitoreti,+ milungu ya ku Siriya,+ milungu ya ku Sidoni,+ milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya ana a Amoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Motero iwo anasiya Yehova ndipo sanam’tumikire.+

  • 1 Mafumu 18:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Eliya anayankha kuti: “Ine sindinachititse kuti Isiraeli anyanyalidwe,+ koma inu ndi nyumba ya bambo anu ndi amene mwachititsa kuti anyanyalidwe,+ chifukwa anthu inu munasiya kutsatira malamulo a Yehova+ n’kuyamba kutsatira Abaala.+

  • 2 Mbiri 28:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma anayenda m’njira za mafumu a Isiraeli,+ ndipo anafika mpaka popangira Abaala+ zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.+

  • Yeremiya 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Unganene bwanji kuti, ‘Sindinadziipitse.+ Sindinatsatire mafano a Baala’?+ Ganizira bwinobwino njira yako m’chigwa.+ Onetsetsa zimene wachita. Wakhala ngati ngamila yaing’ono yaikazi imene ikungothamangira uku ndi uku.

  • Hoseya 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete* yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena