-
Nehemiya 9:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho Yesuwa, Kadimiyeli, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya, omwe anali Alevi, anati: “Dzukani, tamandani+ Yehova Mulungu wanu kuyambira kalekale mpaka kalekale.*+ Inu Mulungu wathu, anthuwa atamande dzina lanu laulemerero,+ lokwezeka kuposa dalitso ndi chitamando chilichonse.
-
-
Danieli 4:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
-