17 Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya anathandiza+ Davide ndipo anakantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti: “Simudzapitanso ndi ife kunkhondo,+ chifukwa mungazimitse+ nyale+ ya Isiraeli!”
18 Koma Abisai,+ m’bale wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu 30 amenewo. Iye ananyamula mkondo ndi kupha nawo anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+