7Tsopano m’masiku a Ahazi mwana wa Yotamu mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda, Rezini+ mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anabwera ku Yerusalemu kudzachita nkhondo koma analephera kulanda mzindawo.+
1Yehova analankhula+ ndi Hoseya+ mwana wa Beeri m’masiku+ a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya+ mafumu a Yuda, ndiponso m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi+ mfumu ya Isiraeli.
1M’masiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda,+ Yehova analankhula ndi Mika+ wa ku Moreseti kudzera m’masomphenya. M’masomphenyawo anamuuza zokhudza Samariya+ ndi Yerusalemu+ kuti: