-
Oweruza 1:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Manase+ sanatenge mzinda wa Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, ndipo sanapitikitse anthu okhala mumzinda wa Dori+ ndi midzi yake yozungulira, anthu a mumzinda wa Ibuleamu+ ndi midzi yake yozungulira, ndi anthu okhala mumzinda wa Megido+ ndi midzi yake yozungulira. Akananiwo anakakamirabe kukhala m’dziko limeneli.+
-
-
2 Mafumu 9:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ahaziya+ mfumu ya Yuda, anaona zonsezo moti anayamba kuthawa kudzera njira ya kumunda.*+ (Pambuyo pake Yehu anayamba kum’tsatira, ndipo anati: “Ameneyonso m’kantheni!” Choncho anam’kanthadi ali m’galeta lake pamene anali kuthawira ku Guru, kufupi ndi ku Ibuleamu.+ Iye anapitirizabe kuthawa mpaka ku Megido+ kumene anakafera.+
-