Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+

      Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+

      Iwo sanaitane pa Yehova.+

  • Miyambo 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Amene amabera mwachinyengo munthu wonyozeka kuti apeze zinthu zambiri,+ komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera, ndithu adzasauka.+

  • Yesaya 32:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu wakhalidwe loipayo, njira zake n’zoipa.+ Iye amakonza zochita khalidwe lotayirira,+ n’cholinga choti apweteke anthu ozunzika pogwiritsa ntchito mawu abodza,+ ngakhale pamene munthu wosauka akunena zoona.

  • Mika 3:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mwadya mnofu wa anthu anga+ ndipo mwasenda khungu lawo. Mwaswa mafupa awo kukhala zidutswazidutswa. Mwawaphwanyaphwanya ngati mafupa ndi mnofu zimene zili mumphika wakukamwa kwakukulu komanso ngati nyama imene ili mumphika.+

  • Habakuku 3:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Munabaya*+ mitu ya asilikali ake ndi zida zake zomwe, pamene iwo anali kubwera ngati mphepo yamkuntho kuti adzandimwaze.+ Kukondwera kwawo chifukwa cha tsoka langa kunali ngati kwa anthu amene akonzeka kuti ameze munthu wosautsidwa m’malo obisalamo.+

  • Maliko 12:40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 Iwo ndi amene amadyerera nyumba+ za akazi amasiye, ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+

  • Yakobo 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena