Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma Zerubabele, Yesuwa,+ ndi atsogoleri ena onse+ a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Mulibe ufulu womanga nafe limodzi nyumba ya Mulungu wathu,+ pakuti ifeyo patokha timangira limodzi nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga momwe Mfumu Koresi+ ya Perisiya yatilamulira.”

  • Ezara 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza.

  • Yesaya 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+ ndipo akalonga+ adzalamuliranso mwachilungamo.

  • Yesaya 51:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwako+ ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa.+ Ndidzachita zimenezi n’cholinga choti ndikhazikitse kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi,+ ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+

  • Luka 12:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 “Musaope,+ kagulu ka nkhosa+ inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.+

  • Aroma 8:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo+

  • Chivumbulutso 14:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa+ ataimirira paphiri la Ziyoni.+ Limodzi naye panali enanso 144,000+ olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate+ wake pamphumi pawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena