13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera.
13 Zipilala+ zamkuwa zimene zinali m’nyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wake kupita nawo ku Babulo.+