Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Yehova adzakutumizira matemberero,+ chisokonezo+ ndi chilango+ pa ntchito zako zonse zimene ukuyesa kugwira. Adzakuchitira zimenezi kufikira utafafanizidwa ndi kutha mofulumira, chifukwa cha kuipa kwa zochita zako popeza kuti wandisiya.+

  • 2 Mbiri 36:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.

  • Yeremiya 6:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova. Ndatopa ndi kukhala chete.”+

      “Tsanulira mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu+ ndipo nthawi yomweyo uutsanulirenso pa kagulu ka anyamata okondana. Mwamuna pamodzi ndi mkazi wake, munthu wachikulire pamodzi ndi munthu wokalamba, onsewo adzagwidwa.+

  • Yeremiya 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+

  • Ezekieli 22:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Choncho ndidzawadzudzula mwamphamvu.+ Ndidzawafafaniza ndi moto wa mkwiyo wanga.+ Ndidzawalanga malinga ndi zochita zawo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

  • Danieli 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu munachitadi zimene munachenjeza kuti mudzatichitira,+ ifeyo ndi atsogoleri athu.+ Munatigwetsera tsoka lalikulu ndipo tsoka limene lagwera Yerusalemu silinachitikeponso padziko lonse lapansi.+

  • Zekariya 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena