Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Titus 1:1-3:15
  • Tito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tito
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Tito

KALATA YOPITA KWA TITO

1 Ine Paulo, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa ndi Mulungu. Komanso ndikudziwa molondola choonadi chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu. 2 Zinthu zimenezi timakhala nazo chifukwa cha chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chimene Mulungu amene sanganame+ analonjeza kalekale. 3 Koma pa nthawi yake, anachititsa kuti mawu ake adziwike kudzera mu ntchito yolalikira imene ndinapatsidwa+ mogwirizana ndi lamulo la Mpulumutsi wathu, Mulungu. 4 Ndikukulembera iwe Tito, mwana wanga weniweni amene uli ndi chikhulupiriro chofanana ndi changa:

Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu, zikhale nawe.

5 Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zolakwika komanso uike akulu mumzinda uliwonse, mogwirizana ndi malangizo amene ndinakupatsa. 6 Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wa ana okhulupirira ndiponso osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.+ 7 Popeza ndi mtumiki* wa Mulungu, woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera. Asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa, wankhanza* kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo. 8 Koma akhale wochereza alendo,+ wokonda zabwino, woganiza bwino,+ wolungama, wokhulupirika+ komanso wodziletsa.+ 9 Akhalenso wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi mfundo zolondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.

10 Chifukwa pali anthu ambiri osalamulirika, olankhula zosathandiza ndiponso opusitsa ena, ndipo pakati pa anthu amenewa palinso amene akulimbikitsabe mdulidwe.+ 11 Anthu amenewa ndi ofunika kuwatseka pakamwa, chifukwa pofuna kupeza phindu mwachinyengo, akuwonongabe mabanja pophunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa. 12 Mmodzi wa iwo, amenenso ndi mneneri wawo, ananena kuti: “Akerete ndi anthu abodza nthawi zonse, zilombo zolusa zakutchire ndiponso alesi osusuka.”

13 Umboni umenewu ndi woona. Chifukwa cha zimenezi, pitiriza kuwadzudzula mwamphamvu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. 14 Asamamvetsere nthano zachiyuda ndiponso kutsatira malamulo a anthu amene asiya choonadi. 15 Zinthu zonse nʼzoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera, chifukwa maganizo awo ndi chikumbumtima chawo nʼzoipitsidwa.+ 16 Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amamukana ndi zochita zawo+ chifukwa ndi onyansa, osamvera ndiponso osayenerera ntchito iliyonse yabwino.

2 Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi mfundo zolondola.+ 2 Amuna achikulire akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana, oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba, achikondi chachikulu ndi opirira kwambiri. 3 Nawonso akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino, 4 nʼcholinga choti azilangiza* akazi achitsikana kuti azikonda amuna awo, azikonda ana awo, 5 azikhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo,* abwino ndiponso ogonjera amuna awo,+ kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.

6 Komanso upitirize kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+ 7 Ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino mʼnjira iliyonse. Uziphunzitsa zolondola* ndipo uzisonyeza kuti ndiwe wopanda chibwana.+ 8 Mawu ako azikhala oyenera, omwe sangatsutsidwe,+ kuti otsutsa achite manyazi ndipo asapeze chifukwa chotinenera.+ 9 Akapolo azigonjera ambuye awo pa zinthu zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10 kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse, kuti azikometsera zimene Mpulumutsi wathu Mulungu amatiphunzitsa.+

11 Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale otani.+ 12 Zimenezi zimatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu. Zimatiphunzitsanso kuti tisamalakelake zinthu zoipa zamʼdzikoli,+ koma kuti tikhale oganiza bwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu mʼdzikoli*+ 13 pamene tikuyembekezera zinthu zosangalatsa+ ndiponso kuonekera kwaulemerero kwa Mulungu wamkulu komanso kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, 14 amene anadzipereka mʼmalo mwa ife+ kuti atilanditse*+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu ake apadera, odzipereka pa ntchito zabwino.+

15 Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu pogwiritsa ntchito ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Usalole kuti munthu aliyense akuderere.

3 Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndiponso kumvera maboma ndi olamulira.+ Akhalenso okonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. 2 Asamanenere zoipa munthu aliyense ndiponso asamakonde kukangana. Koma akhale ololera+ ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.+ 3 Paja nafenso poyamba tinali opanda nzeru, osamvera, osocheretsedwa, akapolo a zilakolako zosiyanasiyana ndiponso a zinthu zosangalatsa, ochita zoipa, akaduka, onyansa komanso tinkadana.

4 Koma Mpulumutsi wathu Mulungu+ atasonyeza kukoma mtima ndi kukonda anthu, 5 (osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene tinachita,+ koma chifukwa cha chifundo chake),+ anatipulumutsa potisambitsa kuti tifike ku moyo watsopano.+ Komanso anatipulumutsa potithandiza ndi mzimu woyera kuti tikhale atsopano.+ 6 Iye anatikhuthulira mzimu umenewu kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,+ 7 kuti titayesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu,+ tingakhale olandira cholowa+ mogwirizana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.+

8 Mawu amenewa ndi oona, ndipo ndikufuna kuti upitirize kutsindika zinthu zimenezi, kuti amene akhulupirira Mulungu aziganizira kwambiri mmene angapitirizire kuchita ntchito zabwino. Zimenezi nʼzabwino ndiponso zothandiza kwa anthu.

9 Koma iwe uzipewa kutsutsana pa zinthu zopusa komanso zokhudza mibadwo ya makolo. Uzipewanso kukangana ndi kulimbana ndi anthu pa nkhani zokhudza Chilamulo, chifukwa zimenezi nʼzosathandiza ndiponso zopanda phindu.+ 10 Munthu wolimbikitsa mpatuko,+ ukamudzudzula* koyamba ndi kachiwiri,+ usagwirizane nayenso+ 11 podziwa kuti munthu woteroyo wasochera, akuchimwa ndipo akudziimba mlandu.

12 Ndikadzatuma Atema kapena Tukiko+ kwa iwe, udzayesetse kuti udzandipeze ku Nikopoli, chifukwa ndaganiza zokakhala kumeneko nyengo yozizirayi. 13 Zena, wodziwa Chilamulo uja, komanso Apolo, uwapatse zinthu zofunika pa ulendo zokwanira, kuti asasowe kanthu.+ 14 Koma abale athu aphunzire kugwira ntchito zabwino kuti azitha kuthandiza pakafunika kutero,+ kuti asakhale opanda phindu.+

15 Onse amene ndili nawo kuno akupereka moni. Undiperekere moni kwa anthu amene amatikonda chifukwa tili ndi chikhulupiriro chofanana.

Kukoma mtima kwakukulu kukhale ndi nonsenu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtumiki woyangʼanira nyumba.”

Kapena kuti, “wandewu; wachiwawa.”

Kapena kuti, “azikumbutsa; aziphunzitsa.”

Kapena kuti, “osamalira nyumba zawo.”

Kapena kuti, “zoyera.”

Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “atiperekere dipo; atiwombole.”

Kapena kuti, “ukamuchenjeza.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena