Misonkhano Yautumiki ya January
Mlungu Woyambira January 1
Mph. 7: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 13: “Lalikirani Mwaluntha.” Fotokozani mfundo zazikulu, ndipo khalani ndi chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za maulalikiwo. Dziŵitsani mpingo za mabuku akale omwe ali m’sitoko pakali pano.
Mph. 15: Pendani mfundo zazikulu za kuchezetsa kwaposachedwapa kwa woyang’anira dera; tchulani kupita patsogolo kumene mpingo ukupanga. Yamikirani abale ndipo perekani malingaliro oyenera opitirabe patsogolo.
Mph. 10: Gwiritsirani ntchito nkhani ya mu Utumiki Wathu Waufumu imene munaphonya pamene munali kumsonkhano wachigawo.
Mlungu Woyambira January 8
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Perekani chiyamikiro choyenera kaamba ka thandizo la ndalama pantchito yakumaloko ndi yapadziko lonse yolalikira uthenga wabwino.
Mph. 15: Phindu Lotetezera la Advance Medical Directive/Release Card. Mkulu akambitsirana ndi mpingo za kufunika kwa aliyense kulemba bwino khadi la Advance Medical Directive/Release ndi kulinyamula nthaŵi zonse ndi kufunika kwa ana kukhala ndi Identity Card nthaŵi zonse. Malinga ndi dzina la khadilo, limadziŵikitsa pasadakhale za chisamaliro cha mankhwala chimene chikufunika (kapena chimene sichikufunika). Kodi nchifukwa ninji zimenezi zimachitika chaka ndi chaka? Khadi latsopano limakhala ndi mphamvu kwambiri kuposa lija limene lingayesedwe lakale kapena losasonyezanso umboni wa zikhulupiriro zanu. Khadilo limakulankhulirani ngati inu sumukhoza kulankhula. Makadiwa adzaperekedwa lero. Muyenera kukawalemba bwinobwino kunyumba, koma osawasaina. Monga momwe tachitira zaka ziŵiri zapitazi, kusaina ndi kukhalira mboni zidzachitikira pamalo a Phunziro la Buku la Mpingo, moyang’aniridwa ndi ochititsa phunziro la buku. Aja amene adzasaina monga mboni ayeneradi kumuona mwini khadilo akusaina. Izi zidzachitika pambuyo pa phunziro la buku mkati mwa mlungu wa January 15. (Onani tsatanetsatane wa njira imeneyi mu Utumiki Wathu Waufumu wa January 1994 patsamba 2. Onaninso kalata ya October 15, 1991.) Ofalitsa onse obatizidwa ayenera kulemba khadi la Advance Medical Directive/Release. Ofalitsa osabatizidwa, mwa kusintha mawu a khadi limeneli malinga ndi mikhalidwe yawo ndi zikhulupiriro zawo, angafune kukonza khadi lawolawo. Makolo ayenera kuthandiza ana awo osabatizidwa kulemba Identity Card.
Mph. 20: “Khalani Akuchita—Osati Akumva Okha.” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, fotokozani za kufunika kwake kwa kumvera, kuchokera m’buku la Insight, tsamba 521, ndime 1 ndi 2.
Nyimbo Na. 70 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 15
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani mwachidule vuto lomakula la kusapeza anthu panyumba. Limbikitsani ofalitsa kuombola nthaŵi mwa kuyamba iwo kulankhula ndi anthu omwe akudutsa, oimirira m’mbali mwa njira, kapena amene akhala m’galimoto.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. (Kapena nkhani yakuti “Samalirani Changu Chanu,” yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya October 1, 1995, masamba 25-8.)
Mph. 18: “Bwererani Kuti Mukapulumutse Ena.” Fotokozani maulaliki osonyezedwa. Limbikitsani kukhala ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro m’buku latsopano lakuti, Knowledge That Leads to Everlasting Life.
Nyimbo Na. 156 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 22
Mph. 5: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 20: “Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 1.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Fotokozani zitsogozo zoperekedwa pankhani za ophunzira m’malangizo a Sukulu Yautumiki Wateokratiki, amene anatuluka mu Utumiki Wathu Waufumu wa October 1995.
Mph. 20: “Lankhulani Molimba Mtima.” Nkhani ndi kukambitsirana, yokambidwa ndi mkulu. Pendani makonzedwe akwanuko a utumiki wa pa Sande. Ayamikireni pachichirikizo chawo chabwino, ndipo tchulani pamene afunikira kuwongolera.
Nyimbo Na. 92 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 29
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Kambani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Ziletso Zimakulefulani?” yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1994, masamba 27-8.
Mph. 20: Gaŵirani Buku la Moyo wa Banja m’February. Fotokozani mmene bukulo limakwaniritsira chofunika chachikulu m’mabanja lerolino. Zikhale zenizeni ndi zopindulitsa. Sonyezani nzeru ya Mawu a Mulungu, ndipo ikambeni mosonkhezera maganizo ndiponso mokondweretsa. Perekani malingaliro otsimikizirika othandiza kuthetsa mavuto ndi kuchititsa ukwati kukhala wosangalatsa monga Mlengi anafunira. Tchulani nkhani zimene likufotokoza. [Sonyezani mpambo wa zamkatimu.] Tchulani kuti bukulo limasonyezanso mankhwala achikhalire a mavuto a anthu. Athandizeni kuona phindu la uthenga wa Ufumu kuti akalandire pamodzi madalitso amtsogolo. Kumbutsani onse kuombola makope okagwiritsira ntchito mu utumiki pakutha kwa mlungu uno.
Nyimbo Na. 143 ndi pemphero lomaliza.