Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 30:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamenepo Yakobo anamupsera mtima kwambiri Rakele n’kumuyankha kuti:+ “Kodi ine ndine Mulungu amene akukulepheretsa kuberekayo?”+

  • Genesis 41:52
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 52 Wachiwiriyo anamutcha Efuraimu,*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana m’dziko la masautso anga.”+

  • Levitiko 26:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘Pamenepo ndidzakucheukirani,+ kukuchititsani kubereka ana ambiri ndi kukuchulukitsani.+ Ndipo ndidzasunga pangano langa ndi inu.+

  • Deuteronomo 28:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Chidzadalitsika chipatso cha mimba yako,+ chipatso cha m’dziko lanu, chipatso cha ziweto zako,+ ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.+

  • Yoswa 24:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “‘Patapita nthawi, ndinatenga Abulahamu+ tate wanu, kuchokera kutsidya lina la Mtsinje,+ ndipo ndinamuyendetsa m’dziko lonse la Kanani, ndi kuchulukitsa mbewu yake.+ Chotero ndinam’dalitsa ndipo anabereka Isaki,+

  • Yoswa 24:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Isaki anabereka Yakobo ndi Esau.+ Pambuyo pake Esau ndinam’patsa phiri la Seiri kuti likhale lake.+ Kenako, Yakobo ndi ana ake anapita ku Iguputo.+

  • Salimo 128:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobala zipatso+

      Mkati mwa nyumba yako.

      Ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya maolivi+ kuzungulira tebulo lako.

  • Yesaya 8:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa+ tili ngati zizindikiro+ ndiponso ngati zozizwitsa mu Isiraeli, zochokera kwa Yehova wa makamu amene amakhala m’phiri la Ziyoni.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena