Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo atumiki ake atauzungulira.+

  • 2 Mafumu 24:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mfumu ya Babulo inatengera ku Babulo amuna onse olimba mtima okwana 7,000, amisiri ndi anthu omanga makoma achitetezo okwana 1,000, ndi amuna onse amphamvu omenya nkhondo.+

  • Ezara 5:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa+ Mulungu wakumwamba, iye anawapereka+ m’manja mwa Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo Mkasidi,+ yemwe anagwetsa nyumbayi+ n’kutengera anthuwo ku ukapolo ku Babulo.+

  • Miyambo 10:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Chinthu choopsa kwa woipa n’chimene chidzamubwerere,+ koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+

  • Yeremiya 24:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndiyeno Yehova anandisonyeza madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandisonyeza zimenezi Nebukadirezara mfumu ya Babulo atatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri+ ndi omanga makoma achitetezo kuchokera ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+

  • Yeremiya 27:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasiya pamene anatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+

  • Yeremiya 29:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamene analemba kalata imeneyi, mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna za panyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu,+ amisiri ndi omanga makoma achitetezo+ anali atatengedwa kupita ku ukapolo kuchokera ku Yerusalemu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena