Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 12:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma ngati simudzamvera mawu a Yehova,+ moti n’kupandukiradi malamulo a Yehova,+ dzanja la Yehova lidzatsutsana ndi inu ndi abambo anu.+

  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • 2 Mbiri 36:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona+ ndi kugwetsa mpanda+ wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino,+ mpaka zonse zinawonongedwa.+

  • Yeremiya 17:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “‘“Koma ngati simudzamvera mawu anga akuti muziona tsiku la sabata kukhala lopatulika ndi kuti musamanyamule katundu+ kulowa naye pazipata za Yerusalemu pa tsiku la sabata, ine ndidzatentha ndi moto zipata za mzindawu.+ Motowo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Yerusalemu+ ndipo sudzazimitsidwa.”’”+

  • Yeremiya 37:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndipo Akasidi adzabweranso ndithu kudzamenyana ndi mzinda uno, kuulanda ndi kuutentha ndi moto.”+

  • Yeremiya 52:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ Anatenthanso nyumba iliyonse ya munthu wotchuka.+

  • Hoseya 8:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Isiraeli anaiwala amene anamupanga+ ndipo anayamba kumanga akachisi.+ Yuda nayenso anachulukitsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma ine ndidzatumiza moto m’mizinda yake ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za mumzinda uliwonse.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena