RUTE
1 Tsopano, pa nthawi imene oweruza+ ankatsogolera* ku Isiraeli, mʼdzikomo munagwa njala. Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda nʼkukakhala ngati mlendo ku Mowabu.+ Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna. 2 Munthuyu dzina lake anali Elimeleki,* ndipo mkazi wake anali Naomi.* Mayina a ana akewo anali Maloni* ndi Kiliyoni.* Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata wa ku Yuda. Ndipo anafika ku Mowabu nʼkumakhala kumeneko.
3 Patapita nthawi, Elimeleki mwamuna wa Naomi anamwalira ndipo Naomi anatsala ndi ana ake aja. 4 Kenako anawo anakwatira akazi a Chimowabu. Wina dzina lake anali Olipa ndipo wina anali Rute.+ Iwo anakhalabe kumeneko zaka pafupifupi 10. 5 Patapita nthawi, ana awiriwo, Maloni ndi Kiliyoni, nawonso anamwalira, ndipo Naomi anatsala yekha wopanda ana komanso mwamuna. 6 Choncho iye ndi apongozi ake anayamba ulendo wochoka ku Mowabu kubwerera kwawo, chifukwa anamva kuti Yehova wakumbukira anthu ake powapatsa chakudya.
7 Choncho Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kumene ankakhala. Ali mʼnjira pa ulendo wobwerera ku Yuda, 8 Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni chikondi chokhulupirika+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera chikondichi kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine. 9 Yehova akudalitseni ndipo aliyense akapeze chitetezo* mʼnyumba ya mwamuna wake.”+ Kenako anawakisa ndipo iwo anayamba kulira mokweza. 10 Iwo ankanena kuti: “Ayi sitibwerera, ife tipita nanu kwanu.” 11 Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathe kuberekanso ana amene angadzakhale amuna anu?+ 12 Bwererani ana anga, pitani, chifukwa ndakalamba kwambiri moti sindingakwatiwenso. Ngakhale nditapeza mwamuna pofika usiku wa lero nʼkubereka ana aamuna, 13 kodi mungawadikire mpaka atakula? Kodi mungadzisungebe osakwatiwanso kuti mudzakwatiwe ndi iwowo? Ayi ndithu ana anga, zimene zinakuchitikirani zimandiwawa kwambiri, chifukwa dzanja la Yehova landiukira.”+
14 Atatero iwo analiranso mokweza. Kenako Olipa anakisa apongozi akewo nʼkubwerera. Koma Rute sanalole kusiyana nawo. 15 Choncho Naomi anati: “Taona mchemwali wako wamasiye wabwerera kwa anthu a kwawo komanso kwa milungu yake. Iwenso bwerera.”
16 Koma Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, chifukwa kumene inu mupite inenso ndipita komweko ndipo kumene mugone inenso ndigona komweko. Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+ 17 Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri ngati chinachake kupatulapo imfa chingandisiyanitse ndi inu.”
18 Naomi ataona kuti Rute walimbikira zoti apite naye, anasiya kumuuza kuti abwerere. 19 Ndipo anapitiriza ulendo wawo mpaka anafika ku Betelehemu.+ Atangofika ku Betelehemu, mumzinda wonsewo anthu anayamba kulankhula za iwo. Azimayi ankafunsa kuti: “Kodi si Naomi uyu?” 20 Koma Naomi ankawayankha kuti: “Musanditchulenso kuti Naomi,* muzinditchula kuti Mara,* chifukwa Wamphamvuyonse wachititsa kuti moyo wanga ukhale wowawa kwambiri.+ 21 Ndinali ndi zonse pochoka kuno, koma Yehova wandibweza wopanda kanthu. Munditchula bwanji kuti Naomi, popeza Yehova ndi amene wandiukira ndipo Wamphamvuyonseyo ndi amene wandigwetsera tsokali?”+
22 Izi ndi zomwe zinachitika pamene Naomi ankabwerera kwawo kuchokera ku Mowabu.+ Iye anabwerera ndi mpongozi wake Rute wa ku Mowabu. Iwo anafika ku Betelehemu kumayambiriro kwa nthawi yokolola balere.+
2 Panali munthu wina wolemera kwambiri yemwe anali wachibale wa mwamuna wake wa Naomi. Dzina lake anali Boazi+ ndipo anali wa kubanja la Elimeleki.
2 Rute mkazi wa ku Mowabu uja anauza Naomi kuti: “Bwanji ndipite ndikakunkhe+ balere mʼmunda wa aliyense amene angandikomere mtima?” Ndipo Naomi anamuyankha kuti: “Pita mwana wanga.” 3 Zitatero Rute ananyamuka nʼkupita ndipo anakalowa mʼmunda wina nʼkuyamba kukunkha pambuyo pa anthu okolola. Ndiye zinangochitika kuti mundawo unali wa Boazi,+ wa kubanja la Elimeleki.+ 4 Pasanapite nthawi, Boazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo analonjera okololawo kuti: “Yehova akhale nanu.” Iwo anayankha kuti: “Yehova akudalitseni.”
5 Kenako Boazi anafunsa mnyamata amene ankayangʼanira okololawo kuti: “Kodi mtsikanayu ndi wakubanja liti?” 6 Mnyamatayo anayankha kuti: “Mtsikanayu ndi Mmowabu,+ anabwera limodzi ndi Naomi kuchokera ku Mowabu.+ 7 Atafika anapempha kuti, ‘Ndimati ndikunkhe nawo.+ Ndizitola balere* wotsala pambuyo pa anthu amene akukololawa.’ Ndipo wakhala akukunkha kuyambira mʼmawa mpaka posachedwapa pamene anakhala pamthunzi kuti apume pangʼono.”
8 Kenako Boazi anauza Rute kuti: “Tamvera mwana wanga, usapitenso kumunda wina kukakunkha. Usachoke kupita kwina, uzikhala pafupi ndi atsikana anga antchitowa.+ 9 Uzingoyangʼana mbali imene akukolola ndipo uziwatsatira. Anyamatawa ndawalamula kuti asakuvutitse.* Ukamva ludzu, uzipita kukamwa madzi amene ali mʼmitsukoyo, omwe anyamatawa atunga.”
10 Atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, nʼkunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mundiganizire ndi kundikomera mtima chonchi, ine wokhala mlendo?”+ 11 Boazi anamuyankha kuti: “Ndamva zonse zimene wachitira apongozi ako kuchokera pamene mwamuna wako anamwalira. Ndamvanso kuti unasiya bambo ako ndi mayi ako komanso dziko lakwanu, nʼkubwera kuno kwa anthu osawadziwa.+ 12 Yehova akupatse mphoto chifukwa cha zimene wachita,+ ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akulipire mokwanira* popeza wathawira mʼmapiko mwake kuti upeze chitetezo.”+ 13 Rute atamva zimenezi anati: “Mwandikomera mtima mbuyanga. Mwandilimbikitsa komanso mwalankhula mondilimbitsa mtima ngakhale kuti si ine mmodzi wa antchito anu.”
14 Pa nthawi ya chakudya Boazi anauza Rute kuti: “Bwera kuno udzadye mkate. Ukhozanso kumasunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anapita nʼkukakhala pansi limodzi ndi okololawo. Ndiyeno Boazi ankamupatsa balere wokazinga ndipo iye anadya nʼkukhuta mpaka wina kutsala. 15 Atatha kudya ananyamuka nʼkukayambanso kukunkha.+ Boazi analamula anyamata ake kuti: “Muzimulola kukunkha barele* ndipo musamʼvutitse.+ 16 Komanso, muzisolola balere wina pamitolopo nʼkumamusiya pansi kuti iye akunkhe ndipo musamuletse kukunkha.”
17 Choncho Rute anapitiriza kukunkha mʼmundamo mpaka madzulo.+ Atamaliza kumenya balere amene anakunkhayo anakwana pafupifupi muyezo umodzi wa efa.* 18 Atatero ananyamula balereyo nʼkubwerera kunyumba, ndipo apongozi ake anaona balere amene anakunkhayo. Kenako Rute anatenga chakudya chimene chinatsala+ chija nʼkuwapatsa apongozi akewo.
19 Tsopano apongozi ake anamʼfunsa kuti: “Kodi lero unakakunkha kuti? Adalitsike amene wakuganizirayo.”+ Ndiyeno iye anauza apongozi akewo za munda umene anakakunkhamo. Anawauza kuti: “Munda umene ndakunkhamo lero, eniake ndi a Boazi.” 20 Atatero Naomi anauza mpongozi wakeyo kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa amoyo ndi akufa, amudalitse munthu ameneyu.”+ Ndipo Naomi anapitiriza kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu.+ Ndi mmodzi wa otiwombola.”+ 21 Ndiyeno Rute mkazi wa Chimowabuyo anati: “Moti anandiuzanso kuti, ‘Usachoke, uzikhala pafupi ndi antchito angawa mpaka adzamalize kukolola.’”+ 22 Naomi anauza Rute mpongozi wakeyo kuti: “Zingakhale bwinodi mwana wanga, uzipita limodzi ndi atsikana akewo, kusiyana nʼkuti akakuchite chipongwe kumunda wina.”
23 Choncho Rute anapitiriza kukhala pafupi ndi atsikana antchito a Boazi, mpaka pamene anamaliza kukolola balere+ ndi tirigu. Ndipo ankakhalabe ndi apongozi ake.+
3 Tsopano Naomi, apongozi ake a Rute, anamuuza kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera nyumba,*+ kuti zikuyendere bwino? 2 Pajatu Boazi ndi wachibale wathu.+ Ndipo atsikana ake antchito wakhala ukugwira nawo ntchito. Usiku walero iye akhala akupeta balere pamalo ake opunthira. 3 Choncho samba nʼkudzola mafuta komanso utchene ndipo upite kumalo opunthirawo. Koma ukaonetsetse kuti iye asakadziwe kuti wafika mpaka atamaliza kudya ndi kumwa. 4 Ndiyeno akamakagona, ukaone kuti wagona pati. Kenako ukapite pamene wagonapo ndipo ukamuvundukule mapazi nʼkugona pomwepo. Iye akakuuza zochita.”
5 Rute anayankha kuti: “Ndikachita zonse zimene mwanena.” 6 Choncho anapita kopunthirako nʼkuchita zonse zimene apongozi ake anamuuza. 7 Boazi anadya ndi kumwa ndipo anali wosangalala kwambiri. Kenako anapita kukagona kumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndipo anavundukula mapazi a Boazi nʼkugona. 8 Pakati pa usiku Boazi anayamba kunjenjemera ndipo anadzuka nʼkukhala tsonga. Koma anadabwa kuona kuti mkazi wagona kumapazi ake. 9 Choncho anafunsa kuti: “Ndiwe ndani?” Rute anayankha kuti: “Ndine Rute kapolo wanu. Ndifunditseni chovala chanu ine kapolo wanu, chifukwa ndinu wotiwombola.”+ 10 Atatero, Boazi anati: “Yehova akudalitse mwana wanga. Chikondi chokhulupirika chimene wasonyeza panopa chikuposa choyamba chija,+ chifukwa sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. 11 Ndiye tamvera mwana wanga, usachite mantha. Ndikuchitira zonse zimene wanena,+ chifukwa aliyense mumzindawu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri. 12 Ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ koma pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine amene angakuwombole.+ 13 Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole mawa, zili bwino akuwombole.+ Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndikuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo, ndikuwombola. Gona mpaka mʼmawa.”
14 Choncho anagonabe kumapazi a Boazi mpaka mʼmamawa. Kenako anadzuka kudakali mdima chifukwa Boazi sanafune kuti anthu adziwe kuti kopunthira mbewuko kunabwera mkazi. 15 Ndiyeno anamuuza kuti: “Bweretsa nsalu wafundayo ndipo uitambasule.” Iye anaitambasuladi ndipo Boazi anathirapo miyezo 6* ya balere nʼkumusenza pamutu. Kenako Boazi analowa mumzinda.
16 Tsopano Rute anabwerera kwa apongozi ake, ndipo iwo anamufunsa kuti: “Wayendako bwanji* mwana wanga?” Iye anawafotokozera zonse zimene Boazi anamuchitira. 17 Anafotokozanso kuti: “Wandipatsa balere uyu wokwana miyezo 6 nʼkundiuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’” 18 Atatero, Naomi anayankha kuti: “Tiye tingodikira mwana wanga, mpaka utadziwa mmene nkhaniyi ithere. Chifukwa iye sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi lero.”
4 Zitatero, Boazi anapita kugeti la mzinda+ nʼkukhala pansi. Ali kumeneko anaona wowombola anamutchula uja+ akudutsa. Ndiyeno Boazi anati: “Iwe uje, tabwera udzakhale apa.” Choncho anapita nʼkukakhala pansi. 2 Kenako Boazi anaitana akulu ena a mzindawo okwana 10+ nʼkuwauza kuti: “Takhalani apa.” Ndipo iwo anakhaladi.
3 Ndiyeno Boazi anauza wowombola uja+ kuti: “Naomi amene wabwerera kuchokera kudziko la Mowabu+ ayenera kugulitsa malo amene anali a mchimwene wathu Elimeleki.+ 4 Ndiye ine ndaganiza zoti ndikuuze kuti, ‘Ugule malowo pamaso pa anthu ndiponso pamaso pa akulu a mzindawu.+ Ngati ukufuna kuwawombola, awombole. Koma ngati sukufuna undiuze, chifukwa iweyo ndiye woyenera kuwombola malowo ndipo pambuyo pako pali ineyo.’” Iye anayankha kuti: “Ndiwombola ineyo.”+ 5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula malowo kwa Naomi, ndiye kuti wagulanso kwa Rute wa ku Mowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+ 6 Wowombolayo atamva zimenezi anati: “Sinditha kuwombola, chifukwa ndingawononge cholowa changa. Inuyo wombolani mʼmalo mwa ine, chifukwa ine sinditha kuwombola.”
7 Kalelo mu Isiraeli munali mwambo wokhudza ufulu wowombola ndiponso wokhudza kusinthana ufuluwo, kuti chilichonse chimene chachitika chitsimikizirike. Mwambo wake unali woti munthu ankavula nsapato yake+ nʼkuipereka kwa mnzake. Umenewu unali umboni woti agwirizana kuti zikhale choncho. 8 Choncho pamene wowombola uja anauza Boazi kuti: “Mugule inuyo,” wowombolayo anavula nsapato yake. 9 Kenako Boazi anauza akulu ndi anthu onse kuti: “Inu ndinu mboni+ lero kuti ndikugula kwa Naomi zinthu zonse zimene zinali za Elimeleki ndiponso zonse zimene zinali za Kiliyoni ndi Maloni. 10 Komanso ndikutenga Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni, kukhala mkazi wanga kuti dzina la mwamuna wake amene anamwalira libwerere pacholowa chake+ komanso kuti lisafafanizidwe pakati pa abale ake ndiponso mumzindawu. Inu ndinu mboni lero.”+
11 Zitatero, anthu onse ndi akulu amene anali pageti la mzindawo ananena kuti: “Ndife mboni! Yehova adalitse mkazi amene akulowa mʼnyumba mwako kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, akazi amene anamanga nyumba ya Isiraeli.+ Zinthu zikuyendere bwino mu Efurata+ ndipo ukhale ndi dzina labwino mu Betelehemu.+ 12 Ndipo kudzera mwa ana amene Yehova adzakupatsa kwa mtsikanayu,+ nyumba yako ikhale ngati nyumba ya Perezi,+ amene Tamara anaberekera Yuda.”
13 Choncho Boazi anatenga Rute kukhala mkazi wake ndipo anagona naye. Yehova anamudalitsa ndipo anatenga pakati nʼkubereka mwana wamwamuna. 14 Zitatero azimayi anayamba kuuza Naomi kuti: “Atamandike Yehova, amene wachititsa kuti upeze wokuwombola lero. Dzina lake lifalitsidwe mu Isiraeli. 15 Mwanayu watsitsimutsa moyo wako ndipo adzakusamalira mu ukalamba wako, chifukwa yemwe wamubereka ndi mpongozi wako amene amakukonda,+ amenenso ndi woposa ana aamuna 7.” 16 Naomi ananyamula mwanayo ndipo ankamulera. 17 Azimayi okhala naye pafupi anamupatsa mwanayo dzina lakuti Obedi. Ndipo iwo anati: “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Obedi+ anali bambo ake a Jese,+ yemwe anabereka Davide.
18 Mzere wa ana a Perezi+ unayenda chonchi: Perezi anabereka Hezironi,+ 19 Hezironi anabereka Ramu, Ramu anabereka Aminadabu,+ 20 Aminadabu+ anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni, 21 Salimoni anabereka Boazi, Boazi anabereka Obedi, 22 Obedi anabereka Jese ndipo Jese+ anabereka Davide.+
Mʼchilankhulo choyambirira, “ankaweruza.”
Kutanthauza “Mulungu Wanga Ndi Mfumu.”
Kutanthauza “Wosangalatsa.”
Nʼkutheka kuti linachokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “kufooka kapena kudwala.”
Kutanthauza “Wolephera; Wotsirizika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mpumulo.”
Kutanthauza “Wosangalatsa.”
Kutanthauza “Kuwawa.”
Mabaibulo ena amati, “mitolo ya balere.”
Kapena kuti, “asakusokoneze.”
Kapena kuti, “akupatse mphoto yokwanira.”
Mabaibulo ena amati, “mitolo ya balere.”
Pafupifupi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mpumulo.”
Nʼkutheka kuti inali miyezo 6 ya seya kapena malita pafupifupi 44. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwe ndani?”