Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Apatuka mofulumira panjira imene ndawalamula kuyendamo.+ Iwo adzipangira fano la mwana wa ng’ombe lopangidwa ndi golide wosungunula. Akuligwadira ndi kupereka nsembe kwa fanolo, ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka m’dziko la Iguputo.’”+

  • 1 Samueli 12:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Pamenepo Samueli anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Inuyo mwachita choipa chachikulu chimenechi. Ngakhale kuti zili choncho, musapatuke n’kusiya kutsatira Yehova,+ koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse.+

  • Salimo 97:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+

      Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+

      Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+

  • Salimo 119:128
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 128 Choncho ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.+

      Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+

  • Miyambo 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+

  • Miyambo 13:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Wolungama amadana ndi lilime lonama,+ koma anthu oipa amachita zinthu zochititsa manyazi ndipo amadzibweretsera manyazi.+

  • Zefaniya 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndidzafafaniza amene akusiya kutsatira Yehova,+ amene sanayesetse kuyandikira Yehova ndi amene sanafunsire kwa iye.”+

  • Aroma 12:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Chikondi+ chanu chisakhale cha chiphamaso.+ Nyansidwani ndi choipa,+ gwiritsitsani chabwino.+

  • Aheberi 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu kuposa cha mafumu ena.”+

  • Aheberi 10:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati wabwerera m’mbuyo, ine sindikondwera naye.”+

  • 2 Petulo 2:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njira ya chilungamo,+ kusiyana n’kuidziwa bwinobwino kenako n’kupatuka pa lamulo loyera lomwe anapatsidwa.+

  • Yuda 23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Apulumutseni+ mwa kuwakwatula pamoto.+ Pitirizaninso kuchitira chifundo ena onse, koma ndi mantha. Iwo aipitsa zovala zawo zamkati ndi ntchito za thupi. Choncho pamene mukuwachitira chifundo, mutalikirane kwambiri ndi zovala zawo zoipitsidwazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena