Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+

  • Yeremiya 13:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndipo ndidzawombanitsa munthu ndi mnzake, abambo ndi ana awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Sindidzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni. Ndithu sindidzakhala ndi chifundo choti ndisawawononge.”’+

  • Maliro 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Yehova wameza malo okhala a Yakobo. Sanamvere chisoni malo ake alionse.+

      Mu ukali wake, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri+ ya mwana wamkazi wa Yuda.

      Waipitsa ufumu+ ndi akalonga+ ake ndipo wawagwetsera pansi.+

  • Maliro 3:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni+ ndipo mukupitiriza kutithamangitsa.+ Mwapha anthu mopanda chisoni.+

  • Ezekieli 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+

  • Ezekieli 7:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena