Aroma
4 Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za Abulahamu kholo lathu?+ 2 Mwachitsanzo, chikhala kuti Abulahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito,+ akanakhala ndi chifukwa chodzitamandira, koma osati kwa Mulungu. 3 Kodi lemba limati chiyani paja? Limati: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”+ 4 Chifukwa munthu amene wagwira ntchito+ saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu,+ koma ngati ngongole.+ 5 Munthu amene sadalira ntchito zake koma amakhulupirira+ Mulungu, amayesedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake,+ pakuti Mulungu amatha kuona munthu wosatsatira malamulo ake kukhala wolungama. 6 Davide ananena kuti munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kuchita ntchito ndi wodala. Iye anati: 7 “Odala ndi amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo+ ndipo machimo awo aphimbidwa.+ 8 Wodala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.”+
9 Chotero, kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala odala choncho? Kapena kodi osadulidwa nawonso amakhala odala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa ngati wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 10 Koma kodi iye anali wotani pamene anayesedwa wotero? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa?+ Sanali wodulidwa, koma wosadulidwa. 11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe monga chizindikiro.+ Chizindikiro chimenechi chinali chosonyeza kuti, chifukwa cha chikhulupiriro, Mulungu anamuyesa wolungama asanadulidwe, kuti adzakhale tate+ wa onse osadulidwa okhala ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12 Kutinso adzakhale tate wa ana odulidwa, osati wa okhawo ochita mdulidwe, komanso wa amene amayenda moyenerera m’mapazi a chikhulupiriro chimene bambo wathu+ Abulahamu anali nacho asanadulidwe.
13 Pakuti Abulahamu kapena mbewu yake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti anali wolungama mwa chikhulupiriro.+ 14 Chifukwa ngati anthu oumirira kusunga chilamulo ndiwo adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa.+ 15 Kwenikweni, Chilamulo chimabala mkwiyo,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+
16 Chotero iye anapatsidwa lonjezolo+ chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale mwa kukoma mtima kwakukulu,+ ndiponso kuti likhale lotsimikizika kwa mbewu yake yonse,+ osati yotsatira Chilamulo yokha ayi, komanso yotsatira chikhulupiriro cha Abulahamu. (Iye ndiye tate+ wa ife tonse, 17 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndakuika kuti ukhale tate wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Uyo amene Abulahamu anam’khulupirira, inde pamaso pa Mulungu, amene amapereka moyo kwa akufa+ ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.+ 18 Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro+ chakuti adzakhala tate wa mitundu yambiri,+ ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ 19 Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, anaganizira za thupi lake, limene linali lakufa tsopano,+ popeza anali ndi zaka pafupifupi 100.+ Anaganiziranso zakuti Sara anali wosabereka.+ 20 Koma chifukwa cha lonjezo+ la Mulungu, iye sanagwedezeke pa chikhulupiriro chake+ ndipo chikhulupiriro chakecho chinamulimbitsa.+ Mwa kutero, anapereka ulemerero kwa Mulungu 21 ndipo anali wotsimikiza kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+ 22 Ndiye chifukwa chake “anaonedwa ngati wolungama.”+
23 Komabe, zonena kuti “anayesedwa+ wolungama” sizinalembedwere iye yekha,+ 24 komanso ife amene tidzayesedwa otero, chifukwa chakuti timakhulupirira iye amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu kwa akufa.+ 25 Iye anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tiyesedwe olungama.+