2 Akorinto
6 Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+ 2 Pakuti iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo m’tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa.+ Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.+
3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa,+ kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.+ 4 Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta,+ 5 kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende,+ kukumana ndi zipolowe, kugwira ntchito mwakhama, kusagona tulo, ndi kukhala osadya.+ 6 Tikusonyezanso zimenezi mwa kukhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ okhala ndi mzimu woyera, osonyeza chikondi chopanda chinyengo,+ 7 olankhula zoona, ndiponso okhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso, tikuchita zimenezi ponyamula zida+ za chilungamo kudzanja lamanja ndi lamanzere, 8 mwa kupatsidwa ulemerero ndi kutonzedwa, mwa kuneneredwa zoipa komanso zabwino. Mwa kukhala ngati achinyengo+ koma oona mtima, 9 ngati osadziwika koma odziwika bwino,+ ngati oti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa+ koma osakaphedwa,+ 10 ngati ogwidwa ndi chisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri, ngati opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.+
11 Takhala tikulankhula mosabisa mawu kwa inu Akorinto, tafutukula mtima wathu.+ 12 Malo sakukucheperani mumtima mwathu,+ koma m’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa.+ 13 Choncho mutibwezere zofanana ndi zimene takuchitirani. Ndikulankhula nanu ngati ana anga,+ inunso futukulani mtima wanu.
14 Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+ 15 Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Kapena munthu wokhulupirira angagawane+ chiyani ndi wosakhulupirira? 16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 17 “‘Choncho tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+ 18 “‘Ndidzakhala atate wanu,+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova Wamphamvuyonse.”+