Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 tsamba 1934-1937
  • 2 Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki

2 Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki

“Yehova.” Chiheberi, יהוה (YHWH kapena JHVH)

Tikaona Zakumapeto 1 ndi 3 n’zodziwikiratu kuti m’Malemba Achiheberi komanso mu Septuagint yachigiriki anagwiritsa ntchito zilembo zinayi zachiheberi zoimira dzina la Mulungu (יהוה). Choncho kaya Yesu ndi ophunzira ake anali kuwerenga Malemba m’Chiheberi kapena m’Chigiriki, ayenera kuti dzina la Mulungu anali kulipeza m’Malemba amenewo. Yesu anatchula dzina la Mulungu pamene anaimirira m’sunagoge ku Nazareti ndi kuwerenga m’buku la Yesaya pa chaputala 61, mavesi 1 ndi 2 pamene pali zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Izi zinali zogwirizana ndi cholinga chake chodziwikitsa dzina la Yehova kwa anthu. Cholinga chimenechi chimaonekera m’pemphero limene anapereka kwa Atate wake lakuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. . . . Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.”—Yoh. 17:6, 26.

Pali umboni wosonyeza kuti ophunzira a Yesu anagwiritsa ntchito zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu m’zolemba zawo. M’chaputala chachitatu cha buku lake lina, Jerome wa m’zaka za m’ma 300 analemba kuti: “Mateyu, amenenso ndi Levi, amene anasiya kukhometsa msonkho n’kukhala mtumwi, analemba Uthenga Wabwino wa Khristu ali ku Yudeya. Poyambapo, anaulemba m’Chiheberi pofuna kupindulitsa anthu odulidwa okhulupirira. Amene anaumasulira m’Chigiriki pambuyo pake sakudziwika bwino. Komanso, zolemba zake zachiheberizo zasungidwa mpaka lero mulaibulale ya ku Kaisareya. Zimenezi zinasonkhanitsidwa mwakhama ndi Pamphilus amene anafera chikhulupiriro. Anazareti amene anali kugwiritsa ntchito mpukutu umenewu mumzinda wa Bereya ku Siriya, anandilolanso ineyo kuukopera.” (De viris inlustribus [Za Anthu Otchuka], lomasuliridwa kuchokera m’Chilatini, lokonzedwa ndi E. C. Richardson ndipo lofalitsidwa m’zigawozigawo zotchedwa “Texte und Untersuchungen zur Geschichte der altchristlichen Literatur,” Vol. 14, Leipzig, 1896, mas. 8, 9.)

Mateyu anagwira mawu Malemba Achiheberi m’malo oposa 100. Choncho ngati m’malo amene anagwira mawuwo munali dzina la Mulungu, sakanachitira mwina koma kulemba mokhulupirika zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu mu Uthenga wake wabwino wachiheberiwo. Uthenga Wabwino wa Mateyu utamasuliridwa m’Chigiriki, zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu anazilembabe m’Chiheberi malinga ndi zimene omasulira ambiri anali kuchita panthawiyo.

Si Mateyu yekha amene anagwira mawu Malemba Achiheberi kapena Septuagint pamene pamapezeka dzina la Mulungu. Anthu onse amene analemba Malemba Achigiriki anachitanso zomwezo. Mwachitsanzo, pokamba nkhani yake yolembedwa pa Mac 3:22, Petulo anagwira mawu opezeka pa De 18:15 pamene pamapezeka zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu mumpukutu wa gumbwa wa Baibulo la Septuagint limene linamasuliridwa zaka za m’ma 100 B.C.E. zisanafike. Popeza kuti Petulo anali wotsatira Khristu, iye anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova. Nkhani ya Petulo italembedwa, zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu anazilembanso m’nkhaniyo malinga ndi zimene olemba nkhani anali kuchita m’zaka 100 zomalizira za m’ma B.C.E., komanso m’zaka 100 zoyambirira za m’ma C.E.

Ndiyeno m’zaka za m’ma 300 kapena 400 C.E. alembi okopera Baibulo anachotsa zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu m’Baibulo la Septuagint komanso m’Malemba Achigiriki. M’malo mwake anaikamo mawu akuti Kyʹri·os, kutanthauza “Ambuye” kapena akuti The·osʹ, otanthauza kuti “Mulungu.”

Ponena za kugwiritsa ntchito zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu m’Malemba Achigiriki, George Howard wa pa yunivesite ya Georgia, analemba kuti: “Zimene atulukira posachedwapa ku Iguputo ndi m’chipululu cha Yudeya zatithandiza kudzionera tokha mmene dzina la Mulungu anali kuligwiritsira ntchito Chikhristu chisanayambe. Zimene atulukirazi n’zofunika pa kufufuza za Chipangano Chatsopano chifukwa zikufanana kwambiri ndi zolemba zachikhristu zakale kwambiri, ndipo zingasonyeze mmene olemba Chipangano Chatsopano anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu. M’masamba otsatirawa tifotokoza mfundo yongoganizira imene ilipo yakuti dzina la Mulungu, יהוה (kapenanso chidule cha dzinali), linalembedwa m’Chipangano Chatsopano m’malo amene chinagwira mawu Chipangano Chakale kapena kufotokozera mawu a m’Chipangano Chakalecho. Tisonyezanso kuti m’kupita kwa nthawi analichotsamo n’kuikamo κς [chidule cha Kyʹri·os, “Ambuye”]. Malinga ndi kuona kwathu, kuchotsa zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu kumeneku, kunabweretsa chisokonezo m’maganizo a Akhristu oyambirira amene sanali Ayuda. Iwo sanathe kusiyanitsa bwinobwino pakati pa ‘Ambuye Mulungu’ ndi ‘Ambuye Khristu.’ Chisokonezo chimenechi chikuonekera bwino m’mipukutu ya malemba a Chipangano Chatsopano.”—Journal of Biblical Literature, Vol. 96, 1977, tsa. 63.

Zili pamwambazi tikugwirizana nazo, kungopatulapo mawu akuti, “mfundo yongoganizira.” Maganizo amenewa sitikuwaona ngati mfundo yongoganizira. Koma zimenezi ndiye zoona zenizeni za mmene mipukutu ya Baibulo anailembera.

KUBWEZERETSA DZINA LA MULUNGU M’MALO AKE

Kwa zaka mazana ambiri Malemba Achigiriki komanso zigawo zake zamasuliridwa kambirimbiri m’Chiheberi. Malemba omasuliridwawo, amene m’nkhani ino tawasonyeza ndi “J” wokhala ndi kanambala pamwamba pake, abwezeretsa dzina la Mulungu m’Malemba Achigiriki ouziridwa m’malo ake osiyanasiyana. Anabwezeretsa dzina la Mulungu limenelo osati pokhapo pamene Malemba Achigiriki akugwira mawu Malemba Achiheberi, komanso pamalo ena pamene panafunika kuti abwezeretse dzina la Mulungulo.

Kuti tidziwe pamene dzina la Mulungu linalowedwa m’malo ndi mawu achigiriki akuti Κύριος ndi Θεός, tinayamba ndi kuona kaye pamene olemba Baibulo ouziridwa achikhristu anagwira mawu a mu mavesi ena ake, m’ndime, ndiponso pamene anagwiritsa ntchito mawu ena ake a m’Malemba Achiheberi. Kenako tinabwerera ku malemba Achiheberiwo kuti tione ngati dzina la Mulungu linalipo pamenepo. Zimenezi zinatithandiza kudziwa kuti mawu akuti Kyʹri·os ndi The·osʹ anali kuimira ndani kwenikweni.

Kuti tisadutse malire a ntchito ya womasulira n’kuyamba kufotokozera malemba, tayesetsa kukhala osamala kwambiri polemba dzina la Mulungu. Nthawi zonse tinayamba tafufuza mosamala Malemba Achiheberi monga maziko. Tinafufuzanso mabaibulo achiheberi ambiri osiyanasiyana omasuliridwa ndi anthu ena kuti tione ngati akugwirizana ndi zimene talemba. Ndife okondwa kunena kuti pamalo onse 237 amene tinabwezeretsapo dzina la Yehova m’Malemba, alionse mwa malo amenewa anagwirizana ndi Baibulo lachiheberi limodzi kapena kuposerapo lokonzedwa ndi anthu ena.

M’munsimu tandandalika malo onsewo 237 pamene pamapezeka dzina lakuti “Yehova” m’Malemba a Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Kutsogolo kwa lemba lililonse kuli maumboni osiyanasiyana osonyeza kuti palembalo panafunikadi kukhala dzina la Mulungu.

Malemba amene tandandalika m’munsimu akusonyezanso mawu achigiriki amene amapezeka palembalo m’Baibulo lachigiriki lokonzedwa ndi Westcott ndi Hort. Mawu akuti Kyʹri·os, amene amatanthauza kuti “Ambuye,” komanso mawu ena ofanana nawo tawalemba ndi chizindikiro chakuti Ky. Mawu akuti The·osʹ, amene amatanthauza kuti “Mulungu” ndiponso mawu ena ofanana nawo tawalemba ndi chizindikiro chakuti Th. Kanyenyezi (*) kamene kali kutsogolo kwa zizindikiro zimenezi kakusonyeza kuti mawu achigirikiwo anali kuyamba ndi mawu enanso achigiriki akuti ho m’Malemba Achigiriki.

MATEYU

1:20 Ky; J3,4,7-14,16-18,22-24,28

1:22 Ky; J1-4,7-14,16-18,22-24,26,28

1:24 Ky; J1-4,7-14,16-18,22-24,28

2:13 Ky; J1-4,6-14,16-18,22-24,28

2:15 Ky; J1,3,4,6-14,16-18,22-24,28

2:19 Ky; J1-4,6-14,16-18,22-24,28

3:3 Ky; J1-4,7-14,16-18,20,22-24,26,28

4:4 Th; J1,3-14,17,18,20,22,23

4:7 Ky; J1-14,16-18,20,22-24,28

4:10 Ky; J1-14,16-18,20,22-24,28

5:33 *Ky; J1-4,7-14,16-18,22,23,28

21:9 Ky; J1-14,16-18,20-24,28

21:42 Ky; J1-4,7-14,16-18,20-24,28

22:37 Ky; J1-14,16-18,20-24,28

22:44 Ky; J1-14,16-18,20-24,28

23:39 Ky; J1,3-14,16-18,21-24,28

27:10 Ky; J1,3,4,7-14,16,17,22-24,28

28:2 Ky; J1-4,7-13,16-18,22-24,28

MALIKO

1:3 Ky; J7-14,16-18,22-24,28

5:19 *Ky; J7-10,17,18,22,28

11:9 Ky; J7,8,10-14,16-18,21-24,28

12:11 Ky; J7-14,16-18,21-24,28

12:29 Ky; J7-14,16-18,20-24,27,28

12:29 Ky; J7-14,16-18,20-24,28

12:30 Ky; J7-14,16-18,21-24,28

12:36 Ky; J7-14,16-18,21-24,28

13:20 Ky; J7,8,10,13,16-18,22-24,28

LUKA

1:6 *Ky; J7-17,23,28

1:9 *Ky; J7-18,22,23,28

1:11 Ky; J7-13,16-18,22-24,28

1:15 Ky; J7,8,10-18,22,23,28

1:16 Ky; J7-18,22-24,28

1:17 Ky; J7-18,22-24,28

1:25 Ky; J7-18,22,23,28

1:28 *Ky; J5,7-18,22,23

1:32 Ky; J5-18,22-24,28

1:38 Ky; J5,7-18,22-24,28

1:45 Ky; J5-18,22-24,28

1:46 *Ky; J5-18,22,23,28

1:58 Ky; J5-18,22-24

1:66 Ky; J5-18,22-24,28

1:68 Ky; J5-18,22-24,28

1:76 Ky; J5-18,22-24,28

2:9 Ky; J5,7-13,16,17,22-24

2:9 Ky; J5,7,8,10-18,22-24,28

2:15 *Ky; J5,7,8,10-18,22,23,28

2:22 *Ky; J5-18,22,23,28

2:23 Ky; J5-18,22-24,28

2:23 *Ky; J5-18,22,23,28

2:24 Ky; J5-18,22-24,28

2:26 Ky; J5-18,22-24,28

2:39 Ky; J5-18,22-24,28

3:4 Ky; J7-15,17,18,22-24,28

4:8 Ky; J7-18,22-24,28

4:12 Ky; J7-18,22-24,28

4:18 Ky; J7-15,20,23,24

4:19 Ky; J7-18,20,22-24,28

5:17 Ky; J7-18,22-24,28

10:27 Ky; J5-18,21-24,28

13:35 Ky; J7-18,21-24,28

19:38 Ky; J7-18,21-24,28

20:37 Ky; J9,11-18,21-24,27,28

20:42 Ky; J7-18,21-24,28

YOHANE

1:23 Ky; J5-14,16-19,22-24,28

6:45 Th; J7,8,10,14,17,19,20,22,23

12:13 Ky; J7-14,16-19,21-24,28

12:38 Ky; J12-14,16-18,22,23

12:38 Ky; J7-14,16-20,22-24,28

MACHITIDWE

1:24 Ky; J7,8,10,22,23

2:20 Ky; J7,8,10-18,20,22-24,28

2:21 Ky; J7,8,10-18,20,22-24,28

2:25 *Ky; J7,8,10-18,20,22,23,28

2:34 Ky; J7,8,10-18,21-24,28

2:39 Ky; J7,8,10,17,18,22-24

2:47 *Ky; J7,8,10

3:19 *Ky; J13-18,22,23,28

3:22 Ky; J7,8,10-18,20,22-24,28

4:26 *Ky; J7,8,10-18,20,22,23,28

4:29 Ky; J7,8,10

5:9 Ky; J7,8,10,13,15-18,22-24

5:19 Ky; J7,8,10,13,15-18,22-24,28

7:31 Ky; J11-18,22-24,28

7:33 *Ky; J11-18,22,23,28

7:49 Ky; J11-18,20,22-24,28

7:60 Ky; J17,18,22,23

8:22 *Ky; J18,22,23

8:24 *Ky; J7,8,10,13,15-18,22,23

8:25 *Ky; J7,8,10,17,18

8:26 Ky; J7,8,10,13,15-18,22-24,28

8:39 Ky; J13,15-18,22-24,28

9:31 *Ky; J7,8,10,13,15,16,18,22

10:33 *Ky; J17,18,23

11:21 Ky; J7,8,10,13,15-18,22,23,28

12:7 Ky; J7,8,10,13,15-18,22-24,28

12:11 *Ky; J7,8,10,13,15,16,18,23,28

12:17 *Ky; J7,8,10,28

12:23 Ky; J7,8,10,13,15-18,22-24,28

12:24 *Ky; J7,8,10,23

13:2 *Ky; J7,8,10,13,15-18,22,23

13:10 *Ky; J7,8,10,13,15-18,22,23,28

13:11 Ky; J7,8,10,15-18,22-24,28

13:12 *Ky; J7,8,10

13:44 *Th; J17,22

13:47 *Ky; J7,8,10,22,23

13:48 *Th; J7,8,10,13,15-17,22,23

13:49 *Ky; J7,8,10,13,15-18,22,23,28

14:3 *Ky; J7,8,10,15-18,23

14:23 *Ky; J7,8,10,13,15,16

15:17 *Ky; J11-18,22,23,28

15:17 Ky; J7,8,10-18,20,22-24,28

15:35 *Ky; J17,18,22,23

15:36 *Ky; J7,8,10,17,18,22,23

15:40 *Ky; J17,18,22

16:14 *Ky; J7,8,10,17,18,23

16:15 *Ky; J7,8,10

16:32 *Th; J7,8,10,17,18,22,23,28

18:21 *Th; J17

18:25 *Ky; J7,8,10,13,15,16,24

19:20 *Ky; J7,8,10,13,15-18,23

21:14 *Ky; J7,8,10,17,18,23

AROMA

4:3 *Th; J7,8,10,17,20,22

4:8 Ky; J7,8,10-18,20,22-25

9:28 Ky; J7,8,10,13,16,20,25

9:29 Ky; J7,8,10-18,20,22-24,28

10:13 Ky; J7,8,10,13-18,22-24,28

10:16 Ky; J7,8,10,13-18,23

11:3 Ky; J7,8,10-18,23,25

11:34 Ky; J7,8,10,13-18,20,22-25,28

12:11 *Ky; J7,8,10,13,16,18

12:19 Ky; J7,8,10-18,22-24

14:4 *Ky; J18,23

14:6 Ky; J7,8,10,13,16,18,22,24

14:6 Ky; J7,8,10,13,16,18,22,24

14:6 Ky; J7,8,10,13,16,22,24

14:8 *Ky; J7,8,10,13-16,18

14:8 *Ky; J7,8,10,13-16,18

14:8 *Ky; J7,8,10,13-16,18

14:11 Ky; J7,8,10-18,22-25,28

15:11 *Ky; J7,8,10-18,20,22,23,25,28

1 AKORINTO

1:31 Ky; J7,8,10-14,16-18,22-24,28

2:16 Ky; J13,14,16-18,22-24,28

3:20 Ky; J7,8,10-14,16-18,20,22-24,28

4:4 Ky; J7,8,10,17,18,23,24,28

4:19 *Ky; J7,8,10,22,23,28

7:17 *Ky; J28

10:9 *Ky; J18,22,23

10:21 Ky; J7,8,10,24

10:21 Ky; J7,8,10,24

10:22 *Ky; J7,8,10,14

10:26 *Ky; J7,8,10,11,13,14,16-18,20,22,23,28

11:32 *Ky; J13,16,18

14:21 Ky; J7,8,10-14,16-18,22-24,28

16:7 *Ky; J7,8,10,13,14,16-18,22,23

16:10 Ky; J7,8,10,13,14,16-18,24,28

2 AKORINTO

3:16 Ky; J7,8,13,14,16,22,24,28

3:17 *Ky; J7,8,13,14,16,28

3:17 Ky; J7,8,13,14,16,22,24,28

3:18 Ky; J7,8,13,14,16,22,24,28

3:18 Ky; J7,8,13,14,16,22,24,28

6:17 Ky; J7,8,11-14,16-18,22-24,28

6:18 Ky; J7,8,11-14,16-18,22-24,28

8:21 Ky; J7,8,24

10:17 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

10:18 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

AGALATIYA

3:6 *Th; J7,8

AEFESO

2:21 Ky; J7,8,13,16-18,22-24,28

5:17 *Ky; J7,8

5:19 *Ky; J7,8,13,16,23,28

6:4 Ky; J7,8,22,24

6:7 *Ky; J7,8

6:8 Ky; J22,24

AKOLOSE

1:10 *Ky; J7,8

3:13 *Ky; J23

3:16 *Th; J7,8,13,14,16,17

3:22 *Ky; J18,22,28

3:23 *Ky; J7,8,17,18,22,23

3:24 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24

1 ATESALONIKA

1:8 *Ky; J7,8,17,18,22,23

4:6 Ky; J7,8,17,18,22-24

4:15 Ky; J7,8,17,18,24

5:2 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24

2 ATESALONIKA

2:2 *Ky; J18,22,23

2:13 Ky; J13,16,24

3:1 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23

2 TIMOTEYO

1:18 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24

2:19 Ky; J7,8,13,14,16-18,20,22-24,28

2:19 Ky; J18,22-24,28

4:14 *Ky; J7,8,13,16-18,22,23

AHEBERI

2:13 *Th; J3,7,8,17,20,22

7:21 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24,28

8:2 *Ky; J7,8,13-16,18,22,23

8:8 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24,28

8:9 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24,28

8:10 Ky; J3,7,8,11-18,20,22,24,28

8:11 *Ky; J3,7,8,11-18,20,22,23,28

10:16 Ky; J3,7,8,11-18,22-24,28

10:30 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24,28

12:5 Ky; J7,8,11-18,20,22-24,28

12:6 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24,28

13:6 Ky; J3,7,8,11-18,20,22-24

YAKOBO

1:7 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

1:12 J7,8,13,16,17

2:23 *Th; J14,17,20,22

2:23 Th; J17

3:9 *Ky; J18,23,28

4:10 Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

4:15 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

5:4 Ky; J7,8,11-14,16-18,22-24,28

5:10 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

5:11 Ky; J7,8,13,14,16,18,22-24,28

5:11 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

5:14 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22

5:15 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23

1 PETULO

1:25 Ky; J7,8,13,14,16-18,20,22,23

3:12 Ky; J7,8,11-14,16-18,20,22-24,28

3:12 Ky; J7,8,11-14,16-18,20,22,24,28

2 PETULO

2:9 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

2:11 Ky; J7,8,13,16-18,22-24

3:8 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

3:9 Ky; J7,8,13,16-18,22-24,28

3:10 Ky; J7,8,13,16-18,22-24,28

3:12 *Th; J7,8,17

YUDA

5 Ky; J7,8,11-14,16-18,22,23

9 Ky; J7,8,11-14,16-18,22-24,28

14 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

CHIVUMBULUTSO

1:8 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

4:8 Ky; J7,8,11-14,16-18,22,24,28

4:11 *Ky; J7,8,13,14,16,18,28

11:17 Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

15:3 Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

15:4 Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

16:7 Ky; J13,14,16-18,22,23,28

18:8 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

19:6 Ky; J7,8,13,14,16-18,22-24,28

21:22 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,23,28

22:5 Ky; J7,8,11-14,16-18,22-24,28

22:6 *Ky; J7,8,13,14,16-18,22,24,28

M’munsimu muli m’ndandanda wa malo 72 amene pamapezeka dzina lakuti “Yehova” m’mawu a m’munsi, osati m’Malemba enieniwo a Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu.

Mt 22:32; Mko 11:10; Lu 1:2; 2:11, 29, 38; 4:4, 18; Yoh 5:4; Mac 2:30; 7:30, 37; 10:22; 13:43, 50; 14:25; 19:23; 20:25; 22:17; 26:7; Aro 7:6; 10:17; 11:8; 1Ak 7:17; 10:28; 11:23; Aga 2:6; 3:20; 5:10, 12; Afi 4:1, 4, 5, 10, 18; Akl 3:15; 1At 4:9, 16, 17, 17; 5:27; 1Ti 2:2, 10; 3:16; 4:7, 8; 5:4, 8; 6:2, 3, 6, 11; 2Ti 1:16, 18; 2:14, 22, 24; Tit 2:12; Ahe 4:3; 9:20; 10:30; 1Pe 2:13; 3:1, 15; 5:3; 2Pe 1:3; 2Yo 11; Chv 11:1, 19; 16:5; 19:1, 2.

Mawu akuti “Ya,” amene ndi chidule cha dzina la Mulungu, amapezeka m’mawu achigiriki akuti hal·le·lou·i·aʹ, amene anachokera ku mawu achiheberi akuti ha·lelu-Yahʹ, kutanthauza “Tamandani Ya, anthu inu!” Chv (malo anayi) 19:1, 3, 4, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena