Yohane
17 Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba+ ndi kunena kuti: “Atate, nthawi yafika, lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+ 2 Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+ 3 Pakuti moyo wosatha+ adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa+ za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona,+ ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.+ 4 Ndakulemekezani+ padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.+ 5 Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+
6 “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu.+ Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu. 7 Tsopano adziwa kuti zonse zimene munandipatsa n’zochokera kwa inu, 8 chifukwa mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo.+ Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera monga nthumwi yanu,+ ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.+ 9 Choncho ndikupempha m’malo mwa iwo, sindikupemphera dziko,+ koma awo amene mwandipatsa, chifukwa iwo ndi anu. 10 Zonse zimene ndili nazo ndi zanu ndipo zanu zonse ndi zanga.+ Ine ndalemekezeka pakati pawo.
11 “Komanso, ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwera kwa inu, koma iwo adakali m’dzikoli.+ Atate Woyera, ayang’anireni+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili.+ 12 Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinali kuwayang’anira+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa. Ine ndawasunga moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka+ kupatulapo mwana wa chiwonongeko,+ kuti malemba akwaniritsidwe.+ 13 Koma tsopano ndikubwera kwa inu, ndipo ndikulankhula zimenezi pamene ndili m’dziko kuti akhale ndi chimwemwe chosefukira ngati chimene ine ndili nacho.+ 14 Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo,+ chifukwa sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.+
15 “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo.+ 16 Iwo sali mbali ya dziko,+ monganso ine sindili mbali ya dziko.+ 17 Ayeretseni+ ndi choonadi. Mawu+ anu ndiwo choonadi.+ 18 Monga mmene munanditumizira ine m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko.+ 19 Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe+ ndi choonadi.
20 “Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo,+ 21 kuti onsewa akhale amodzi,+ mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana,+ kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife,+ ndi kuti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi.+ 22 Komanso, ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi.+ 23 Ine wogwirizana ndi iwo, inu wogwirizana ndi ine, kuti iwo akhale mu umodzi weniweni,+ kuti dziko lidziwe kuti inu munandituma ine, ndi kuti munawakonda iwo mmene munandikondera ine. 24 Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale,+ kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko+ a dziko.+ 25 Atate wolungama,+ ndithudi dziko silinakudziweni,+ koma ine ndikukudziwani ndipo awa adziwa kuti inu munandituma.+ 26 Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu+ ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”+