Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 35:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndipo mizinda imene mukaperekeyo, mizinda yothawirako 6 imeneyo, izikagwira ntchito imeneyi.

  • Yoswa 20:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ mogwirizana ndi zimene ndinakuuzani kudzera mwa Mose.

  • Yoswa 20:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.

  • Yoswa 20:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.

  • Yoswa 21:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu+ amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto,

  • Yoswa 21:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Motero anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto,

  • Yoswa 21:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Ana a Gerisoni+ a m’mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase.+ Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana, ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beesitera+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.

  • Yoswa 21:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Kuchokera m’fuko la Nafitali,+ anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Kedesi,+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu.

  • Yoswa 21:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kuchokera m’fuko la Rubeni,+ anawapatsa Bezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto,

  • Yoswa 21:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Kuchokera m’fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi,+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto,

  • Deuteronomo 4:41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano,+

  • Deuteronomo 4:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 kuti munthu wopha mnzake mwangozi,+ amene sanali kudana naye kale n’kale,+ azithawirako. Ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi ndi kukhala ndi moyo.+

  • Yoswa 20:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mizindayo ntchito yake ikhale yoti wopha munthu+ mwangozi azithawirako pothawa wobwezera magazi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena