3 Koma bambo ndi mayi akewo anam’funsa kuti: “Kodi wasowa mkazi pakati pa ana aakazi a abale ako ndi anthu onse a mtundu wathu,+ kuti upite kukatenga mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?”+ Koma Samisoni anauza atate akewo kuti: “Ingonditengerani mkazi ameneyu, chifukwa ndi amene ali woyenera kwa ine?”