Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 7:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Usachite nawo mantha pakuti Yehova Mulungu wako, Mulungu wamphamvu ndi wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+

  • Deuteronomo 28:58
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 58 “Ngati sudzatsatira mosamala mawu onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili,+ kuti uziopa dzina laulemerero+ ndi lochititsa manthali,+ dzina lakuti Yehova,+ amene ndi Mulungu wako,

  • Nehemiya 9:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu,+ wamphamvu+ ndi wochititsa mantha,+ wosunga pangano+ ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha,+ musachepetse+ mavuto onse amene agwera ifeyo,+ mafumu athu,+ akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu+ ndi anthu anu onse kuchokera masiku a mafumu a Asuri mpaka lero.+

  • Salimo 8:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,+

      Inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!+

  • Salimo 66:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+

      Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zanu, adani anu adzabwera kwa inu mogonjera.+

  • Salimo 148:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+

      Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+

      Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+

  • Yesaya 29:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 pakuti akaona ana ake pakati pake, ntchito ya manja anga,+ iwo adzayeretsa dzina langa.+ Adzayeretsadi Woyera wa Yakobo,+ ndipo adzalemekeza kwambiri Mulungu wa Isiraeli.+

  • Chivumbulutso 15:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kodi ndani sadzakuopani,+ inu Yehova?+ Ndani sadzalemekeza dzina lanu?+ Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika.+ Mitundu yonse ya anthu idzabwera kudzalambira pamaso panu,+ chifukwa malamulo anu olungama aonekera.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena