Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chivumbulutso 2
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso

      • Mauthenga opita ku Efeso (1-7), ku Simuna (8-11), ku Pegamo (12-17), ku Tiyatira (18-29)

Chivumbulutso 2:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 1:20
  • +Mac 19:1; Aef 1:1
  • +Chv 1:12, 13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Utumiki Komanso Moyo Wathu,

    11/2019, tsa. 5

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 33

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 11

    12/1/1999, ptsa. 15-16

Chivumbulutso 2:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 20:29, 30; 2Ak 11:13; 1Yo 4:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 33-34

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 11

Chivumbulutso 2:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Pe 4:14
  • +Aga 6:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    5/2022, tsa. 3

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 33

Chivumbulutso 2:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    5/2022, tsa. 3

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/2008, ptsa. 22-26

    3/15/2007, tsa. 12

    5/15/2003, ptsa. 11-12

    10/1/2002, ptsa. 20-21

    10/1/1997, tsa. 26

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 30, 34-35

Chivumbulutso 2:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 3:19
  • +Chv 1:20
  • +Chv 2:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/2007, tsa. 12

    5/15/2003, tsa. 11

    10/1/2002, ptsa. 20-21

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 31-32, 35

Chivumbulutso 2:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 11:19; Chv 2:15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 35-36

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 11

Chivumbulutso 2:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 11:15; Chv 2:17, 29
  • +1Yo 5:4
  • +Aro 2:6, 7; Chv 2:10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    1/15/2009, tsa. 31

    5/15/2003, tsa. 11

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 36-37, 306

Chivumbulutso 2:8

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 1:13, 17
  • +Aro 14:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 37-38

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 12

Chivumbulutso 2:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2Ak 6:4, 10; 1Ti 6:18, 19; Yak 2:5
  • +Chv 3:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 38

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 12

    11/15/1989, ptsa. 22-23

    4/1/1989, ptsa. 13-14

Chivumbulutso 2:10

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 10:28
  • +Aro 2:6, 7; 2Ti 4:7, 8; Yak 1:12; Chv 20:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    1/1/2007, tsa. 31

    8/15/2006, tsa. 24

    5/15/2003, ptsa. 12-13

    1/1/1989, tsa. 30

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 38-41

Chivumbulutso 2:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 13:9
  • +1Yo 5:5
  • +Chv 20:6, 14; 21:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 28-29, 38-39

Chivumbulutso 2:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 1:13, 16; 19:15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 41-42

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 13

Chivumbulutso 2:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mko 13:9; Chv 2:3
  • +Lu 12:8; 1Yo 2:23
  • +Mac 1:8
  • +Mt 24:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Galamukani!,

    6/2013, tsa. 7

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 42-43

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 13

Chivumbulutso 2:14

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 31:16; 2Pe 2:15; Yuda 11
  • +Nu 22:4
  • +Nu 25:1, 2; Mac 15:28, 29; Aef 5:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 43-44

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, ptsa. 13-14

    4/1/1990, tsa. 30

    4/1/1989, tsa. 13

Chivumbulutso 2:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2Pe 2:1; Chv 2:6

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 30, 44-45

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 14

    4/1/1989, tsa. 12

Chivumbulutso 2:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 1:13, 16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 31-32, 44-45

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 14

Chivumbulutso 2:17

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 2:7
  • +1Yo 5:5; Chv 3:12
  • +Eks 16:15, 31; Sl 78:24; Ahe 9:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 45-47

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 14

    8/15/1999, tsa. 28

Chivumbulutso 2:18

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “mkuwa.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 16:14
  • +Chv 19:12
  • +Chv 1:13-15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 47-48

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, ptsa. 15-16

Chivumbulutso 2:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 48

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 16

Chivumbulutso 2:20

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Mf 16:31; 2Mf 9:22
  • +1Ak 5:11; Aga 5:19; Aef 5:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 30, 48-49

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 16

    4/1/1990, tsa. 30

    4/1/1989, tsa. 13

Chivumbulutso 2:21

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 49-50

Chivumbulutso 2:22

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 31-32, 49-50

Chivumbulutso 2:23

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “ndimafufuza mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 22:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2015, tsa. 15

    9/15/2010, tsa. 27

    12/1/1999, tsa. 16

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 31-32, 50-51

Chivumbulutso 2:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 8:44

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    9/15/2010, tsa. 27

    5/15/2003, tsa. 16

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 51-52

Chivumbulutso 2:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 3:11

Chivumbulutso 2:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 2:8, 9; Mt 19:28; Lu 22:28-30; Chv 3:21; 20:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 53, 281

    Nsanja ya Olonda,

    8/15/1990, tsa. 31

Chivumbulutso 2:27

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 12:5; 19:15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, ptsa. 53, 281

    Nsanja ya Olonda,

    8/15/1990, tsa. 31

Chivumbulutso 2:28

Mawu a M'munsi

  • *

    “Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pangʼono kutuluka.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 22:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 53

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2003, tsa. 16

Chivumbulutso 2:29

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 54

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Chiv. 2:1Chv 1:20
Chiv. 2:1Mac 19:1; Aef 1:1
Chiv. 2:1Chv 1:12, 13
Chiv. 2:2Mac 20:29, 30; 2Ak 11:13; 1Yo 4:1
Chiv. 2:31Pe 4:14
Chiv. 2:3Aga 6:9
Chiv. 2:5Chv 3:19
Chiv. 2:5Chv 1:20
Chiv. 2:5Chv 2:16
Chiv. 2:61Ak 11:19; Chv 2:15
Chiv. 2:7Mt 11:15; Chv 2:17, 29
Chiv. 2:71Yo 5:4
Chiv. 2:7Aro 2:6, 7; Chv 2:10
Chiv. 2:8Chv 1:13, 17
Chiv. 2:8Aro 14:9
Chiv. 2:92Ak 6:4, 10; 1Ti 6:18, 19; Yak 2:5
Chiv. 2:9Chv 3:9
Chiv. 2:10Mt 10:28
Chiv. 2:10Aro 2:6, 7; 2Ti 4:7, 8; Yak 1:12; Chv 20:4
Chiv. 2:11Chv 13:9
Chiv. 2:111Yo 5:5
Chiv. 2:11Chv 20:6, 14; 21:8
Chiv. 2:12Chv 1:13, 16; 19:15
Chiv. 2:13Mko 13:9; Chv 2:3
Chiv. 2:13Lu 12:8; 1Yo 2:23
Chiv. 2:13Mac 1:8
Chiv. 2:13Mt 24:9
Chiv. 2:14Nu 31:16; 2Pe 2:15; Yuda 11
Chiv. 2:14Nu 22:4
Chiv. 2:14Nu 25:1, 2; Mac 15:28, 29; Aef 5:5
Chiv. 2:152Pe 2:1; Chv 2:6
Chiv. 2:16Chv 1:13, 16
Chiv. 2:17Chv 2:7
Chiv. 2:171Yo 5:5; Chv 3:12
Chiv. 2:17Eks 16:15, 31; Sl 78:24; Ahe 9:4
Chiv. 2:18Mac 16:14
Chiv. 2:18Chv 19:12
Chiv. 2:18Chv 1:13-15
Chiv. 2:201Mf 16:31; 2Mf 9:22
Chiv. 2:201Ak 5:11; Aga 5:19; Aef 5:5
Chiv. 2:23Chv 22:12
Chiv. 2:24Yoh 8:44
Chiv. 2:25Chv 3:11
Chiv. 2:26Sl 2:8, 9; Mt 19:28; Lu 22:28-30; Chv 3:21; 20:4
Chiv. 2:27Chv 12:5; 19:15
Chiv. 2:28Chv 22:16
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Chivumbulutso 2:1-29

Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira

2 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Efeso+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena wonyamula nyenyezi 7 mʼdzanja lake lamanja, amene akuyenda pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide:+ 2 ‘Ndikudziwa ntchito zako, khama lako ndi kupirira kwako ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Ndikudziwanso kuti unayesa anthu amene ankati ndi atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi abodza. 3 Ukuonetsanso kupirira ndipo walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa,+ koma sunafooke.+ 4 Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya kusonyeza chikondi ngati mmene unkachitira poyamba.

5 Choncho, kumbukira malo amene unali usanagwe ndipo ulape+ ndi kuchita ntchito zimene unkachita poyamba. Ngati suchita zimenezi, ndibwera kwa iwe ndipo ndidzachotsa choikapo nyale chako+ pamalo ake ngati sulapa.+ 6 Komabe, pali chinthu chimodzi chimene ukuchita bwino: Umadana ndi zochita za mpatuko wa Nikolao,+ zimenenso ine ndimadana nazo. 7 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Amene wapambana pankhondo,+ ndidzamulola kudya zipatso zamumtengo wa moyo+ umene uli mʼparadaiso wa Mulungu.’

8 Kwa mngelo wa mpingo wa ku Simuna lemba kuti: Izi ndi zimene akunena ‘Woyamba ndi Womaliza,’+ amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo:+ 9 ‘Ndikudziwa masautso ako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.+ Ndikudziwanso kuti pali anthu amene amanena kuti ndi Ayuda ndipo amakunyoza. Koma sikuti iwo ndi Ayuda, mʼmalomwake iwo ndi sunagoge wa Satana.+ 10 Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.+ Taona! Mdyerekezi apitiriza kuponya mʼndende ena a inu kuti muyesedwe mpaka pamapeto, ndipo mudzakhala mʼmasautso kwa masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa ndipo ndidzakupatsa mphoto* ya moyo.+ 11 Amene ali ndi makutu amve+ zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti: Amene wapambana pankhondo+ sadzakhudzidwa ndi imfa yachiwiri.’+

12 Kwa mngelo wa mpingo wa ku Pegamo lemba kuti: Izi ndi zimene akunena amene ali ndi lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse:+ 13 ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa+ ndipo sunakane kuti umandikhulupirira.+ Sunakane ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika,+ amene anaphedwa+ mumzinda wanu, kumene Satana akukhala.

14 Ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu amene akupitiriza kutsatira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuti aikire ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita chiwerewere.*+ 15 Kuwonjezera pamenepo, ulinso ndi anthu amene akupitiriza kutsatira chiphunzitso cha mpatuko wa Nikolao.+ 16 Choncho ulape. Ngati sulapa, ndibwera kwa iwe mwamsanga, ndipo ndidzamenyana nawo ndi lupanga lalitali lamʼkamwa mwanga.+

17 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Amene wapambana pankhondo+ ndidzamupatsa ena mwa mana obisika+ komanso ndidzamupatsa mwala woyera. Pamwala woyerawo panalembedwa dzina latsopano limene wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.’

18 Kwa mngelo wa mpingo wa ku Tiyatira+ lemba kuti: Izi ndi zimene Mwana wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi la moto+ ndipo mapazi ake ali ngati kopa* woyengedwa bwino:+ 19 ‘Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako komanso kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa nʼzambiri kuposa zimene unkachita poyamba.

20 Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti ukulekerera mayi uja Yezebeli,+ amene amadziona ngati mneneri. Iye akuphunzitsa ndi kusocheretsa akapolo anga kuti azichita chiwerewere*+ komanso kuti azidya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano. 21 Ndamupatsa nthawi kuti alape, koma sakufuna kulapa chiwerewere* chakecho. 22 Taona! Ndatsala pangʼono kumudwalitsa kwambiri, ndipo amene akuchita naye chigololo ndiwabweretsera masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo. 23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri woopsa, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ine ndi amene ndimafufuza maganizo* komanso mitima, ndipo aliyense payekha ndidzamubwezera mogwirizana ndi ntchito zake.+

24 Komabe, ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene simutsatira chiphunzitso chimenechi, amene simukudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amati ndi “zinthu zozama za Satana,”+ ndikukuuzani kuti: Sindikusenzetsani katundu aliyense wolemera. 25 Mʼmalomwake gwirani mwamphamvu zinthu zabwino zimene muli nazo mpaka nditabwera.+ 26 Ndipo amene wapambana pankhondo nʼkumatsatira ntchito zanga mpaka mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu.+ 27 Ulamuliro wake udzakhala wofanana ndi umene ine ndalandira kuchokera kwa Atate wanga. Iye adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo+ moti anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi. 28 Ndipo ndidzamupatsa nthanda.*+ 29 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.’”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena