Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 16:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+

  • 1 Mafumu 8:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 inuyo mumve muli kumwamba,+ malo anu okhala okhazikika+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu.+ Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inuyo nokha mumadziwa bwino mtima wa ana onse a anthu).+

  • 1 Mbiri 28:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+

  • Salimo 17:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+

      Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+

      Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+

  • Salimo 44:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+

      Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+

  • Salimo 139:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.+

      Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere,+

  • Yeremiya 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Inu Yehova, mumandidziwa bwino.+ Mumandiona ndipo mumasanthula mtima wanga kuti muone ngati uli wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,+ ndipo aikeni padera kuyembekezera tsiku lokaphedwa.

  • Yeremiya 20:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama.+ Mumaona impso ndi mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+ pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+

  • Aheberi 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena