Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 78:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,+

      M’badwo wosamva ndi wopanduka,+

      M’badwo umene sunakonze mtima wawo,+

      Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.+

  • Salimo 81:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuumitsa mtima wawo.+

      Iwo anapitiriza kuyenda mu nzeru zawo.+

  • Salimo 95:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kwa zaka 40, m’badwo umenewo unali kundinyansa,+

      Ndipo ndinati:

      “Anthu awa mitima yawo imasochera,+

      Ndipo sadziwa njira zanga.”+

  • Yesaya 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+

  • Yesaya 65:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+

  • Yeremiya 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+

  • Yeremiya 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ M’malomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse amene ndinanena m’pangano langa, amene ndinawalamula kuti awasunge, koma sanawasunge.’”

  • Yeremiya 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Koma iwo anati: “Zimenezo ayi!+ Ife titsatira maganizo athu, ndipo aliyense wa ife adzaumitsabe mtima wake woipawo.”+

  • Hoseya 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+ Akuwaitana kuti abwerere kwa amene ali wokwezeka, koma palibe ngakhale ndi mmodzi yemwe amene akuimirira.

  • Machitidwe 7:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena