Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 53:1-12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+ 2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pa winawake, ndiponso ngati muzu m’dziko lopanda madzi. Alibe maonekedwe alionse apamwamba kapena okongola,+ ndipo maonekedwe ake si osiririka m’maso mwathu.+

      3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+ 4 Zoonadi, iye anatinyamulira matenda athu+ ndipo anatisenzera zowawa zathu.+ Koma ifeyo tinamuona ngati wosautsidwa,+ wokwapulidwa ndi Mulungu,+ ndiponso wozunzidwa.+ 5 Iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+ Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo,+ ndipo chifukwa cha zilonda zake+ ifeyo tachiritsidwa.+ 6 Tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.+ Aliyense analowera njira yake ndipo Yehova wachititsa cholakwa cha aliyense wa ife kugwera pa ameneyo.+ 7 Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+

      8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.+ Ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake?+ Pakuti iye anadulidwa+ m’dziko la amoyo.+ Chifukwa cha zolakwa+ za anthu anga, iye anakwapulidwa.+ 9 Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa,+ ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake,+ ngakhale kuti iye sanachite zachiwawa zilizonse+ ndipo m’kamwa mwake munalibe chinyengo.+

      10 Koma zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe.+ Iye anamulola kuti adwale.+ Mukapereka moyo wake monga nsembe ya kupalamula,+ iye adzaona ana ake.+ Adzatalikitsa masiku ake+ ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda+ Yehova.+ 11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri+ ndipo iye adzagawana zolanda ndi amphamvu,+ chifukwa anakhuthula moyo wake mu imfa+ ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.+ Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri+ ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.+

  • Danieli 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+

      “Gulu lankhondo la mtsogoleri amene akubwera lidzawononga+ mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyera amenewo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira, ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mulungu wagamula kuti padzakhale chiwonongeko.+

  • Machitidwe 4:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Iwo anasonkhana pamodzi kuti achite zimene inu munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa chakuti zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+

  • 1 Petulo 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Anali kufufuza nyengo+ yake kapena mtundu wa nyengo imene mzimu+ umene unali mwa iwo unali kuwasonyeza yokhudzana ndi Khristu.+ Mzimuwo unali kuchitira umboni za masautso a Khristu+ ndi za ulemerero+ wobwera pambuyo pake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena