Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+

  • Yesaya 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 M’tsiku limenelo,+ padzakhala muzu wa Jese+ womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.+ Ngakhale anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awatsogolere,+ ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.+

  • Yesaya 52:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 momwemonso iye adzadabwitsa mitundu yambiri.+ Mafumu adzatseka pakamwa pawo akadzamuona,+ chifukwa iwo adzaona zimene sanauzidwepo, ndipo adzaganizira zimene sanamvepo.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Zekariya 13:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Iwe lupanga, nyamuka ukanthe m’busa wanga.+ Ukanthe mwamuna wamphamvu yemwe ndi mnzanga,”+ watero Yehova wa makamu. “Ipha m’busa+ ndipo nkhosa zake zibalalike.+ Ine ndidzakomera mtima nkhosa zonyozeka.”+

  • Malaki 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+

  • Luka 24:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi+ ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri+ ndi m’Masalimo+ ziyenera kukwaniritsidwa.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena