Amosi
9 Ndinaona Yehova ataima pamwamba pa guwa lansembe,+ ndipo anati: “Menya mutu wa chipilala kuti maziko ake agwedezeke ndipo udulenso mitu ya zipilala zonse.+ Ndiyeno otsala mwa anthuwo ndidzawapha ndi lupanga. Aliyense wa iwo amene adzathawa ndidzamuphabe, aliyense wa iwo amene adzathawa sadzapulumuka.+ 2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+ 3 Akabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, ndidzawafufuza mosamala ndi kuwatenga,+ ndipo akathawa pamaso panga ndi kubisala pansi pa nyanja,+ ndidzalamula njoka pansi pa nyanja pomwepo kuti iwalume. 4 Akatengedwa ndi adani awo kupita ku ukapolo, kumeneko ndidzalamula lupanga kuti liwaphe.+ Ndidzakhala tcheru kuti ndiwagwetsere tsoka osati kuwapatsa madalitso.+ 5 Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiye amasungunula dziko mwa kungolikhudza.+ Onse okhala mmenemo adzalira.+ Dziko lonse lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo, ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.+
6 “‘Yehova ndilo dzina+ la amene amamanga makwerero ake kumwamba+ ndi kumanganso nyumba pamwamba pa dziko lapansi limene analikhazikitsa,+ amene amaitana madzi akunyanja+ kuti awakhuthulire panthaka ya dziko lapansi.’+
7 “Yehova akufunsa kuti, ‘Inu ana a Isiraeli, kodi simuli ngati ana a Akusi kwa ine? Kodi si ndine amene ndinatulutsa Aisiraeli m’dziko la Iguputo,+ amenenso ndinatulutsa Afilisiti+ ku Kerete komanso Asiriya ku Kiri?’+
8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse. 9 Pakuti taonani, ine ndalamula kuti nyumba ya Isiraeli igwedezedwe pakati pa mitundu yonse,+ monga mmene munthu amachitira posefa, ndipo mwala sudzadutsa kuti ugwere pansi. 10 Anthu anga onse ochimwa adzaphedwa ndi lupanga.+ Iwo amanena kuti: “Tsoka silitiyandikira kapena kutigwera.”’+
11 “‘Pa tsiku limenelo, ndidzautsa+ nyumba+ ya Davide imene inagwa,+ ndi kukonza mmene khoma* lake linawonongeka. Ndidzautsa mabwinja ake ndipo ndidzaimanga kuti ikhale ngati masiku akale.+ 12 Ndidzachita zimenezi kuti anthu anga adzatenge zinthu zotsala za Edomu+ ndi mitundu yonse ya anthu imene inali kuitanira pa dzina langa,’+ watero Yehova, amene akuchita zimenezi.
13 “Yehova wanena kuti, ‘Masiku adzafika pamene wolima adzapitirira wokolola,+ ndipo woponda mphesa adzapitirira munthu amene wanyamula mbewu zoti akabzale.+ Mapiri adzachucha vinyo wotsekemera*+ ndipo zitunda zonse zidzatulutsa vinyo wochuluka.+ 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+
15 “‘Ine ndidzawabzala panthaka yawo ndipo sadzazulidwanso m’dziko limene ndawapatsa,’+ watero Yehova Mulungu wanu.”