-
Yoswa 13:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo kum’mawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi,+ ankalitcha dziko la Akanani.)+ Madera a Afilisitiwa akulamulidwa ndi olamulira ogwirizana asanu.+ Maderawo ndi Gaza,+ Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ komanso Aavi+ akukhala komweko.
-
-
Oweruza 16:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Pamenepo olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anafika kwa mkaziyo ndi kumuuza kuti: “Umunyengerere+ kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zazikuluzo ndi zimene tingachite kuti timugonjetse. Ufufuzenso zimene tingam’mange nazo kuti tithane naye. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva zokwana 1,100.”+
-
-
Oweruza 16:30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Ndipo Samisoni anati: “Ndife nawo limodzi+ Afilisitiwa.” Pamenepo anawerama atasonkhanitsa mphamvu zake zonse moti nyumbayo inagwera olamulira ogwirizana a Afilisiti ndi anthu onse amene anali m’nyumbayo.+ Anthu amene Samisoni anawapha pa imfa yake anali ambiri kuposa anthu amene anawapha pa moyo wake.+
-
-
1 Samueli 5:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Chotero anatumiza uthenga ndi kusonkhanitsa olamulira onse ogwirizana a Afilisiti ku Asidodi ndi kuwauza kuti: “Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Isiraeli?” Pamapeto pake iwo anati: “Likasa limeneli la Mulungu wa Isiraeli tilitumize kumzinda wa Gati.”+ Choncho anapititsa likasa la Mulungu wa Isiraeli kumeneko atayenda nalo mozungulira.
-
-
1 Samueli 6:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe ya kupalamula imene tiyenera kupereka ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi alauli aja anati: “Mupereke zifanizo zisanu zagolide za matenda a mudzi, ndi zifanizo zisanu zagolide za mbewa zoyenda modumpha, malinga ndi chiwerengero cha olamulira ogwirizana+ a Afilisiti. Muchite zimenezi pakuti mliri umene wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu ogwirizana ndi umodzi.
-
-
1 Mbiri 12:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Analiponso ena a fuko la Manase amene anapanduka n’kupita kwa Davide pamene iye anabwera ndi Afilisiti+ kudzamenyana ndi Sauli. Koma Davide sanawathandize Afilisitiwo chifukwa olamulira awo ogwirizana+ atakambirana, anam’bweza chifukwa anati: “Ameneyu akhoza kukatitembenukira n’kugwirizana ndi mbuye wake Sauli, kenako akatidula mitu.”+
-