Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 21:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Anamanga maguwa ansembe m’nyumba ya Yehova,+ imene ponena za iyo Yehova anati: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+

  • 2 Mbiri 33:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Anamanga maguwa ansembe+ m’nyumba ya Yehova, imene ponena za iyo Yehova anati: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+

  • Yeremiya 7:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 ‘Pakuti ana a Yuda achita zinthu zoipa m’maso mwanga,’ watero Yehova. ‘Aika zinthu zawo zonyansa m’nyumba yotchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+

  • Yeremiya 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova.

  • Ezekieli 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+

  • Ezekieli 8:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, takweza maso ako uyang’ane kumpoto.” Chotero ndinakweza maso anga n’kuyang’ana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa chipata cha guwa lansembe kunali chizindikiro choimira nsanje+ pakhomo la chipatalo.

  • Ezekieli 23:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa+ malo anga opatulika+ ndiponso sabata langa.+

  • Hoseya 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zam’chipululu.+ Ndinaona makolo a anthu inu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu wongoyamba kumene kubereka.+ Iwo anapita kwa Baala wa ku Peori+ ndipo anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazicho.+ Anakhala onyansa ngati chinthu chimene anali kuchikondacho.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena