Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 45:kam-17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.* Salimo la ana a Kora. Masikili.* Nyimbo yonena za akazi okondedwa.

      45 Mtima wanga wagalamuka chifukwa cha nkhani yosangalatsa.+

      Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za mfumu.”+

      Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera malemba waluso.+

       2 Ndiwedi wokongola kwambiri kuposa ana a anthu.+

      Mawu otuluka m’kamwa mwako ndi osangalatsadi.+

      N’chifukwa chake Mulungu adzakupatsa madalitso mpaka kalekale.+

       3 Mangirira lupanga lako+ m’chiuno mwako wamphamvu iwe,+

      Limodzi ndi ulemu ndiponso ulemerero wako.+

       4 Ndipo upambane mu ulemerero wako.+

      Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+

      Ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.+

       5 Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu,+

      Mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ako.+

       6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

      Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+

       7 Umakonda chilungamo+ ndipo umadana ndi zoipa.+

      N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako,+ wakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu+ kuposa cha mafumu ena.+

       8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+

      Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+

       9 Ana aakazi+ a mafumu ali m’gulu la akazi ako okondedwa.

      Mkazi wamkulu wa mfumu+ waima kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+

      10 Iwe mwana wanga wamkazi, mvetsera ndipo ona ndi kutchera khutu.

      Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.+

      11 Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,+

      Pakuti ndiyo mbuye wako,+

      Choncho iweramire.+

      12 Mwana wamkazi wa ku Turo alinso komweko ndi mphatso,+

      Olemera pakati pa anthu adzakhazika pansi mtima wako.+

      13 Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu m’nyumba ya mfumu.+

      Zovala zake ndi zagolide.

      14 Adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.+

      Anamwali anzake omuperekeza akubwera nawo kwa iwe.+

      15 Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.

      Ndipo adzalowa m’nyumba ya mfumu.

      16 Ana anu adzatenga+ malo a makolo anu,+

      Ndipo mudzawaika kukhala akalonga padziko lonse lapansi.+

      17 Ndidzatchula dzina lanu m’mibadwo yonse yam’tsogolo.+

      N’chifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.

  • Mateyu 22:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati+ wa mwana wake.

  • 2 Akorinto 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndikukuchitirani nsanje,+ ngati imene Mulungu amakuchitirani, popeza ndine ndinakuchititsani kulonjezedwa ukwati+ ndi mwamuna mmodzi,+ Khristu,+ ndipo ndikufuna kukuperekani ngati namwali woyera+ kwa iye.

  • Chivumbulutso 19:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero,+ chifukwa ukwati+ wa Mwanawankhosa wafika,+ ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena