Zekariya
3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Pa nthawiyi Satana+ anali ataimirira kudzanja lamanja la Yoswa kuti azim’tsutsa.+ 2 Kenako mngelo+ wa Yehova anauza Satana kuti: “Iwe Satana, Yehova akudzudzule!+ Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzule!+ Kodi munthu uyu si chikuni chimene chaphulidwa pamoto msangamsanga?”+
3 Pa nthawi imene Yoswa anaimirira pamaso pa mngelo, anali atavala zovala zonyansa.+ 4 Ndiyeno mngeloyo anauza amene anaimirira pamaso pake kuti: “Muvuleni zovala zonyansazi.” Kenako anauza Yoswa kuti: “Waona, ndakuchotsera zolakwa zako,+ ndipo wavekedwa mikanjo yapadera.”+
5 Pamenepo ndinanena kuti: “Auzeni kuti amuveke nduwira* yoyera kumutu kwake.”+ Ndipo anamuvekadi nduwira yoyera kumutu kwake. Anamuvekanso zovala. Apa n’kuti mngelo wa Yehova ataimirira pambali pake. 6 Mngelo wa Yehova uja anayamba kulimbikitsa Yoswa kuti: 7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ukayenda m’njira zanga ndi kusunga malamulo anga,+ udzakhala woweruza wa anthu a m’nyumba yanga+ ndipo uzidzayang’anira mabwalo a nyumba yanga. Ndithu ndidzakulola kumafika pamaso panga limodzi ndi amene aima panowa.’
8 “‘Tamvera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi pamaso pako, pakuti iwo ndi amuna amene ali ngati zizindikiro zolosera zam’tsogolo.+ Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+ 9 Taonani mwala+ umene ndauika pamaso pa Yoswa. Mwala umenewu uli ndi maso 7.+ Pamwalawu ndilembapo zinthu mochita kugoba,+ ndipo ndidzachotsa zolakwa za dzikoli m’tsiku limodzi,’+ watero Yehova wa makamu.
10 “‘Pa tsiku limenelo mudzaitanizana, aliyense atakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndiponso wa mkuyu,’+ watero Yehova wa makamu.”