Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 20
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Machitidwe

      • Paulo ku Makedoniya ndi ku Girisi (1-6)

      • Utiko anaukitsidwa ku Torowa (7-12)

      • Kuchoka ku Torowa kupita ku Mileto (13-16)

      • Paulo anakumana ndi akulu a ku Efeso (17-38)

        • Ankaphunzitsa kunyumba ndi nyumba (20)

        • “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri” (35)

Machitidwe 20:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 165-166

Machitidwe 20:2

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 166-167

Machitidwe 20:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 23:12, 16; 2Ak 11:23, 26

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 167-168

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/2001, tsa. 31

    6/15/1990, tsa. 21

Machitidwe 20:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:2
  • +Mac 16:1, 2
  • +Aef 6:21; Akl 4:7; 2Ti 4:12
  • +Mac 21:29; 2Ti 4:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 167-168

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/2001, tsa. 31

    7/15/1998, tsa. 7

Machitidwe 20:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 168

Machitidwe 20:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 12:15; 23:15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 168

Machitidwe 20:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,

    Nsanja ya Olonda,

    2/15/1993, tsa. 29

    4/15/1991, ptsa. 26-27

Machitidwe 20:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 165

Machitidwe 20:9

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 165

Machitidwe 20:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Mf 17:21, 22; 2Mf 4:32, 34
  • +Mt 9:23, 24; Yoh 11:39, 40; Mac 9:39, 40

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 165

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2000, ptsa. 12-13

Machitidwe 20:11

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “ananyemanyema mkate ndipo anayamba kudya.”

Machitidwe 20:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 168

Machitidwe 20:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 18:21
  • +Mac 24:17

Machitidwe 20:17

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/15/2004, tsa. 19

Machitidwe 20:18

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 19:9, 10

Machitidwe 20:19

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 15:9; 1At 2:6

Machitidwe 20:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 28:19, 20; 2Ti 4:2
  • +Mac 5:42

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 42, 169-170

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2008, ptsa. 17-18

    7/15/2008, ptsa. 3-4

    3/15/2004, tsa. 12

    8/1/1991, tsa. 24

    1/15/1991, ptsa. 10-13

    6/15/1990, ptsa. 21-22

    1/1/1988, tsa. 24

    2/15/1987, tsa. 26

    9/1/1986, ptsa. 31-32

    3/15/1986, ptsa. 15-16

    Kukambitsirana, ptsa. 277-278

Machitidwe 20:21

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mko 1:14, 15
  • +Lu 24:46, 47

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2008, ptsa. 17-19

    1/15/1991, ptsa. 11-13

    2/15/1987, tsa. 26

    9/1/1986, ptsa. 31-32

Machitidwe 20:22

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 173

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 22

Machitidwe 20:23

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 9:15, 16; 21:4, 11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 189

Machitidwe 20:24

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “wamtengo wapatali.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2Ti 4:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 170

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    7/2016, ptsa. 26-27

    Nsanja ya Olonda,

    9/15/2011, ptsa. 23-24

    12/15/2008, ptsa. 18-19

    5/15/2008, tsa. 32

Machitidwe 20:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eze 33:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    9/1/1986, ptsa. 31-32

Machitidwe 20:27

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “zonse zimene Mulungu akufuna kuchita.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 28:19, 20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    9/1/1986, ptsa. 31-32

Machitidwe 20:28

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ti 4:16
  • +1Ti 3:1-7; Tit 1:5-9; Ahe 13:17
  • +Yoh 21:15; Aef 4:11; 1Pe 5:2-4
  • +Mt 26:27, 28; 1Yo 1:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Yandikirani, ptsa. 101-102

    Nsanja ya Olonda,

    11/15/2013, tsa. 22

    6/15/2011, ptsa. 20-21

    3/15/2002, ptsa. 14, 15-16

    1/15/2001, ptsa. 13-16

    7/15/1993, ptsa. 24, 26-27

    7/1/1992, tsa. 16

    2/1/1992, tsa. 16

    9/15/1989, tsa. 14

    Kukambitsirana, tsa. 405

Machitidwe 20:29

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 7:15; 2At 2:3; 2Pe 2:1

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 170-172

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2013, tsa. 18

    5/15/2003, tsa. 27

    7/1/1992, ptsa. 16-17

    6/15/1990, tsa. 22

    9/15/1989, tsa. 16

    Galamukani!,

    2/2007, tsa. 8

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 33

Machitidwe 20:30

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ti 4:1; 2Ti 4:3, 4; 1Yo 2:18, 19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    7/15/2013, tsa. 18

    7/15/2011, tsa. 15

    9/1/2004, tsa. 15

    5/15/2003, tsa. 27

    6/15/1990, tsa. 22

    Galamukani!,

    2/2007, tsa. 8

Machitidwe 20:31

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 19:9, 10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Mapeto a Chivumbulutso, tsa. 33

Machitidwe 20:32

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aef 1:18; Akl 1:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 22

Machitidwe 20:33

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Sa 12:1, 3; Mt 10:8; 1Ak 9:11, 12; 2Ak 7:2; Tit 1:7

Machitidwe 20:34

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 18:3; 1Ak 4:11, 12; 1At 2:9

Machitidwe 20:35

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aef 4:28; 1At 4:11, 12; 2At 3:7, 8
  • +Miy 19:17; Mt 10:8; Lu 6:38

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    “Wotsatira Wanga,” ptsa. 109-110

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 172

    Yandikirani, tsa. 300

    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lesson 17

    Galamukani!,

    No. 1 2021 tsa. 7

    No. 1 2018, tsa. 5

    No. 1 2016, tsa. 6

    11/2013, tsa. 8

    11/2008, ptsa. 6-7

    4/2006, tsa. 6

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    8/2018, ptsa. 18-22

    Nsanja ya Olonda (Yogawira),

    No. 1 2018, tsatsa. 14-15

    Nsanja ya Olonda (Yogawira),

    No. 2 2017, tsatsa. 13-14

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/2012, tsa. 8

    7/1/2011, ptsa. 7-8

    8/1/2005, tsa. 6

    9/1/2002, tsa. 9

    7/1/2001, ptsa. 12-17

    11/15/2000, tsa. 10

    9/15/2000, ptsa. 23-24

    1/15/1992, tsa. 12

    12/1/1990, ptsa. 18-19

    6/15/1990, tsa. 22

    Mphunzitsi Waluso, ptsa. 92-96

Machitidwe 20:37

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “anamukumbatira.”

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 171-172

Machitidwe 20:38

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 20:25

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Mac. 20:3Mac 23:12, 16; 2Ak 11:23, 26
Mac. 20:4Mac 27:2
Mac. 20:4Mac 16:1, 2
Mac. 20:4Aef 6:21; Akl 4:7; 2Ti 4:12
Mac. 20:4Mac 21:29; 2Ti 4:20
Mac. 20:6Eks 12:15; 23:15
Mac. 20:101Mf 17:21, 22; 2Mf 4:32, 34
Mac. 20:10Mt 9:23, 24; Yoh 11:39, 40; Mac 9:39, 40
Mac. 20:16Mac 18:21
Mac. 20:16Mac 24:17
Mac. 20:18Mac 19:9, 10
Mac. 20:191Ak 15:9; 1At 2:6
Mac. 20:20Mt 28:19, 20; 2Ti 4:2
Mac. 20:20Mac 5:42
Mac. 20:21Mko 1:14, 15
Mac. 20:21Lu 24:46, 47
Mac. 20:23Mac 9:15, 16; 21:4, 11
Mac. 20:242Ti 4:7
Mac. 20:26Eze 33:8
Mac. 20:27Mt 28:19, 20
Mac. 20:281Ti 4:16
Mac. 20:281Ti 3:1-7; Tit 1:5-9; Ahe 13:17
Mac. 20:28Yoh 21:15; Aef 4:11; 1Pe 5:2-4
Mac. 20:28Mt 26:27, 28; 1Yo 1:7
Mac. 20:29Mt 7:15; 2At 2:3; 2Pe 2:1
Mac. 20:301Ti 4:1; 2Ti 4:3, 4; 1Yo 2:18, 19
Mac. 20:31Mac 19:9, 10
Mac. 20:32Aef 1:18; Akl 1:12
Mac. 20:331Sa 12:1, 3; Mt 10:8; 1Ak 9:11, 12; 2Ak 7:2; Tit 1:7
Mac. 20:34Mac 18:3; 1Ak 4:11, 12; 1At 2:9
Mac. 20:35Aef 4:28; 1At 4:11, 12; 2At 3:7, 8
Mac. 20:35Miy 19:17; Mt 10:8; Lu 6:38
Mac. 20:38Mac 20:25
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
  • 30
  • 31
  • 32
  • 33
  • 34
  • 35
  • 36
  • 37
  • 38
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe 20:1-38

Machitidwe a Atumwi

20 Chipolowe chija chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa nʼkutsanzikana nawo, ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya. 2 Iye anayendayenda mʼmadera akumeneko nʼkumalimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri, kenako anafika ku Girisi. 3 Atakhala kumeneko miyezi itatu, anaganiza zobwerera ku Makedoniya, chifukwa chakuti Ayuda+ anamukonzera chiwembu. Chiwembuchi anachikonza Paulo atangotsala pangʼono kuyamba ulendo wapamadzi wopita ku Siriya. 4 Pa ulendowu anali limodzi ndi Sopaturo mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe ndi Timoteyo,+ koma ochokera mʼchigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+ 5 Anthu amenewa anatsogola ndipo ankatiyembekezera ku Torowa. 6 Koma tinayamba ulendo wapanyanja ku Filipi masiku a Mkate Wopanda Zofufumitsa+ atatha. Ndipo tinawapeza ku Torowa patapita masiku 5. Kumeneko tinakhalako masiku 7.

7 Pa tsiku loyamba la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye chakudya, Paulo anayamba kuwakambira nkhani, chifukwa kunali koti anyamuka tsiku lotsatira. Ndipo analankhula kwa nthawi yaitali mpaka pakati pa usiku. 8 Mʼchipinda chamʼmwamba mmene tinasonkhanamo, munali nyale zambiri ndithu. 9 Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato. Ali mʼtulo choncho, anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja, ndipo anamupeza atafa. 10 Koma Paulo anatsika pansi, ndipo anafika pamene iye anali nʼkumukumbatira.+ Kenako ananena kuti: “Khalani chete, chifukwa ali moyo tsopano.”+ 11 Atatero Paulo anapitanso mʼchipinda chamʼmwamba chija ndipo anatenga mkate nʼkuyamba kudya.* Anakambirana nawo kwa nthawi yaitali mpaka mʼbandakucha ndipo kenako ananyamuka nʼkumapita. 12 Choncho iwo anatenga mnyamata uja ali wamoyo ndipo anatonthozedwa kwambiri.

13 Tsopano ife tinatsogola kukakwera ngalawa nʼkuyamba ulendo wopita ku Aso. Iye anatiuza kuti titsogole ndipo tikamutengere ku Aso chifukwa ankafuna kuyenda wapansi. 14 Choncho atatipeza ku Aso, tinamukweza mʼngalawa nʼkupita ku Mitilene. 15 Mʼmawa wake titachoka kumeneko, tinafika pafupi ndi Kiyo. Koma tsiku lotsatira tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo mʼmawa wake tinafika ku Mileto. 16 Paulo anaganiza zongolambalala Efeso,+ kuti asataye nthawi mʼchigawo cha Asia. Anachita zimenezi chifukwa ankafulumira kuti ngati nʼkotheka, pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.+

17 Komabe ali ku Mileto anatumiza uthenga woti akulu a mpingo wa ku Efeso abwere. 18 Akuluwo atafika, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinkachitira zinthu pa nthawi yomwe ndinali nanu, kuchokera tsiku limene ndinafika mʼchigawo cha Asia.+ 19 Ndinkatumikira Ambuye ngati kapolo modzichepetsa kwambiri,+ ndi misozi komanso ndi mayesero amene ndinakumana nawo chifukwa cha ziwembu za Ayuda. 20 Komatu sindinakubisireni chilichonse chothandiza ndipo sindinasiye kukuphunzitsani pagulu+ komanso kunyumba ndi nyumba.+ 21 Koma ndachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape+ nʼkubwerera kwa Mulungu komanso kuti ayambe kukhulupirira Ambuye wathu Yesu.+ 22 Ndipo tsopano, motsogoleredwa ndi mzimu, ndikupita ku Yerusalemu ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko. 23 Koma chinthu chimodzi chokha chimene ndikudziwa nʼchakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti ndikuyembekezera kumangidwa komanso kuzunzidwa.+ 24 Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika* kwa ine. Chimene ndikungofuna nʼchakuti ndimalize kuthamanga mpikisanowu, komanso kuti ndimalize+ utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.

25 Ndipo tamverani tsopano. Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikirani za Ufumu, simudzaonanso nkhope yanga. 26 Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndilibe mlandu wa magazi a anthu onse+ 27 chifukwa ndinakuuzani malangizo onse a Mulungu.*+ 28 Muzidziyangʼanira nokha+ komanso kusamalira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani kuti muziliyangʼanira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.+ 29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu+ ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. 30 Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.+

31 Choncho khalani maso, ndipo muzikumbukira kuti kwa zaka zitatu+ masana ndi usiku, sindinasiye kuchenjeza aliyense wa inu ndikutulutsa misozi. 32 Koma tsopano ndikukusiyani kuti mutetezedwe ndi Mulungu ndiponso mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu. Mawu amenewo angakulimbikitseni ndi kukupatsani cholowa pakati pa oyera onse.+ 33 Sindinasirire siliva, golide kapena chovala cha munthu.+ 34 Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zofunika pa moyo wanga+ ndi za amene ndinali nawo. 35 Pa zinthu zonse ndakusonyezani kuti pogwira ntchito molimbikira chonchi,+ muzithandiza ofooka ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Paja iye anati, ‘Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri+ kuposa kulandira.’”

36 Atanena zimenezi, iyeyo ndi akulu onsewo anagwada nʼkupemphera. 37 Zitatero onse analira kwambiri. Kenako anamuhaga* Paulo nʼkumukisa mwachikondi. 38 Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.+ Kenako anamʼperekeza kukakwera ngalawa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena