Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Philippians 1:1-4:23
  • Afilipi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Afilipi
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Afilipi

KALATA YOPITA KWA AFILIPI

1 Ine Paulo limodzi ndi Timoteyo, akapolo a Khristu Yesu, ndikulembera oyera onse amene ndi ophunzira a Khristu Yesu amene ali ku Filipi,+ komanso oyangʼanira ndi atumiki othandiza:+

2 Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.

3 Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga ndikakumbukira za inu. 4 Ndimachita zimenezi mʼpemphero langa lililonse lopembedzera limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu.+ 5 Ndimamuthokoza chifukwa cha chopereka chanu chimene mwakhala mukupereka kuti chithandize pa ntchito yolengeza* uthenga wabwino, kuyambira pa tsiku loyamba mpaka pano. 6 Chifukwa sindikukayikira kuti amene anayambitsa ntchito yabwino kwa inu, adzaipitiriza nʼkuimalizitsa+ mpaka tsiku la Khristu Yesu.+ 7 Nʼzoyenera kwa ine kuti ndiganizire nonsenu mwa njira imeneyi, chifukwa ndinu apamtima panga. Inu amene munandithandiza pa nthawi imene ndinamangidwa maunyolo mʼndende+ komanso poteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.+ Inu limodzi ndi ine tinapindula ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.

8 Ndipo Mulungu ndi mboni yanga kuti ndikufunitsitsa nditakuonani nonsenu. Chikondi changa pa inu ndi chachikulu ngati chimene Khristu Yesu ali nacho. 9 Ndipo ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula kwambiri,+ limodzi ndi kudziwa zinthu molondola+ komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.+ 10 Chitani zimenezi kuti muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri+ nʼcholinga choti mukhale opanda cholakwa ndiponso osakhumudwitsa ena+ mpaka tsiku la Khristu. 11 Muchite zimenezi kutinso mudzazidwe ndi zipatso zolungama mothandizidwa ndi Yesu Khristu,+ kuti Mulungu alemekezedwe ndi kutamandidwa.

12 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zimene zandichitikira, zathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire. 13 Chifukwa Asilikali Oteteza Mfumu ndi ena onse amva+ kuti ndamangidwa+ chifukwa cha Khristu. 14 Ndipo abale ambiri amene akutumikira Ambuye alimba mtima chifukwa cha kumangidwa kwanga, komanso akupitiriza kusonyeza kulimba mtima polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.

15 Nʼzoona kuti ena akulalikira zokhudza Khristu chifukwa akundichitira kaduka komanso akupikisana nane, koma ena akulalikira ndi cholinga chabwino. 16 Achiwiriwa akufalitsa uthenga wokhudza Khristu chifukwa cha chikondi, popeza akudziwa kuti ndinasankhidwa kuti nditeteze uthenga wabwino.+ 17 Koma oyambawo akuchita zimenezo chifukwa cha mtima wokonda mikangano, osati ndi cholinga chabwino. Iwo akungofuna kundiyambitsira mavuto mʼndende muno. 18 Ndiye kodi zotsatira zake nʼzotani? Ndi zoti uthenga wokhudza Khristu ukufalitsidwabe, kaya ndi mwachiphamaso kapena mʼchoonadi ndipo ine ndikusangalala chifukwa cha zimenezi. Ndipotu ndipitirizabe kusangalala 19 chifukwa ndikudziwa kuti zimenezi zidzachititsa kuti ndipulumutsidwe chifukwa cha mapembedzero anu+ komanso ndi thandizo la mzimu wa Yesu Khristu.+ 20 Zimenezi nʼzogwirizana ndi zimene ndikudikirira mwachidwi ndiponso chiyembekezo changa chakuti sindidzachititsidwa manyazi mwa njira iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula, tsopano Khristu alemekezedwa kudzera mwa ine,* ngati mmene zakhala zikuchitikira mʼmbuyo monsemu. Iye alemekezedwabe kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalira.+

21 Chifukwa kwa ine, ndikakhala ndi moyo, ndikhala ndi moyo kuti ndizitumikira Khristu+ ndipo ndikamwalira ndipindula.+ 22 Tsopano ngati ndipitirizabe kukhala ndi moyo mʼthupi limene ndili naloli, ntchito ya manja anga idzawonjezeka, koma choti ndisankhe pamenepa sindinena. 23 Ndagwira njakata kuti ndisankhe chiti pa zinthu ziwirizi, chifukwa ndikulakalaka nditamasulidwa nʼkukakhala ndi Khristu,+ zimene kunena zoona ndi zabwino kwambiri.+ 24 Komabe, ndi bwino kuti ndipitirizebe kukhala ndi moyo mʼthupi limene ndili naloli chifukwa cha inu. 25 Choncho, popeza kuti ndatsimikizira zimenezi, ndikudziwa kuti ndikhalabe ndi moyo ndipo ndipitiriza kukhala ndi nonsenu kuti mupite patsogolo komanso kuti musangalale chifukwa cha chikhulupiriro chanu. 26 Inde, kuti ndikadzabweranso kwa inu chisangalalo chanu chidzasefukire chifukwa ndinu otsatira a Khristu Yesu.

27 Koma chimene ndikungofuna nʼchakuti makhalidwe anu akhale ogwirizana* ndi uthenga wabwino wa Khristu,+ kuti kaya ndabwera kudzakuonani kapena pamene ine kulibe, ndizimva za inu, kuti mukupitirizabe kukhala ogwirizana.*+ Ndipo ndi mtima umodzi, mukuyesetsa mogwirizana kuti mupitirize kukhulupirira uthenga wabwino. 28 Komanso simukuchita mantha mʼnjira iliyonse ndi amene akukutsutsani. Umenewu ndi umboni wakuti adzawonongedwa,+ koma kwa inu, ndi umboni wakuti mudzapulumutsidwa+ ndipo umboni umenewu ndi wochokera kwa Mulungu. 29 Zili choncho chifukwa inu munapatsidwa mwayi, osati wokhulupirira Khristu wokha, komanso wovutika chifukwa cha iye.+ 30 Nʼchifukwa chake inunso mukukumana ndi mavuto ofanana ndi amene munaona ine ndikukumana nawo,+ amene panopa mukumva kuti ndikukumana nawobe.

2 Muzichita zonse zimene mungathe kuti muzilimbikitsana mwa Khristu, muzitonthozana mwachikondi, muzisonyeza mzimu wokonda kuchitira zinthu limodzi,* muzisonyezana chikondi chachikulu komanso chifundo. 2 Mukamachita zimenezi, mudzachititsa kuti chimwemwe changa chisefukire. Muzisonyeza kuti mumaganiza mofanana, muli ndi chikondi chofanana komanso kuti ndinu ogwirizana kwambiri ndipo maganizo anu ndi amodzi.+ 3 Musamachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano+ kapena chifukwa chodzikuza,+ koma modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.+ 4 Musamaganizire zofuna zanu zokha,+ koma muziganiziranso zofuna za ena.+

5 Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nawo.+ 6 Ngakhale kuti iye ankaoneka ngati Mulungu,+ sanaganizirepo zoti ayese kulanda udindo wa Mulungu kuti akhale wofanana naye.+ 7 Ayi sanachite zimenezo, koma anasiya zonse zimene anali nazo nʼkukhala ngati kapolo+ ndipo anakhala munthu.*+ 8 Kuposanso pamenepo, atakhala munthu,* anadzichepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa,+ inde imfa yapamtengo wozunzikirapo.*+ 9 Pa chifukwa chimenechi, Mulungu anamukweza nʼkumupatsa udindo wapamwamba+ ndipo mokoma mtima anamupatsa dzina loposa lina lililonse.+ 10 Anachita zimenezi kuti mʼdzina la Yesu, onse apinde mawondo awo, kaya ali kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka.*+ 11 Komanso kuti aliyense avomereze poyera kuti Yesu Khristu ndi Ambuye,+ zimene zidzapereka ulemerero kwa Mulungu Atate.

12 Abale ndi alongo anga okondedwa, pamene ndinali nanu limodzi, nthawi zonse munkamvera. Simunachite zimenezi pa nthawi yokhayo imene ine ndinalipo koma ngakhale panopa pamene sindilinso ndi inu, mukumvera kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, aliyense wa inu apitirize kuyesetsa kuchita zimenezi mwamantha ndi kunjenjemera kuti adzapulumuke. 13 Chifukwa Mulungu ndi amene amakulimbitsani. Amakupatsani mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Iye amachita zimenezi chifukwa ndi zimene zimamusangalatsa. 14 Mukamachita zinthu muzipewa kungʼungʼudza+ komanso kukangana+ 15 kuti mukhale opanda chifukwa chokunenezerani komanso osalakwa. Mukhale ana a Mulungu+ opanda chilema pakati pa mʼbadwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota.+ Pakati pa mʼbadwo umenewu inu mukuwala ngati zounikira mʼdzikoli.+ 16 Pamene mukuchita zimenezi, mugwire mwamphamvu mawu amoyo.+ Mukatero ndidzakhala ndi chifukwa chosangalalira mʼtsiku la Khristu, chifukwa ndidzadziwa kuti sindinathamange pachabe kapena kuchita khama pachabe. 17 Komabe, ngakhale kuti ndikuthiridwa ngati nsembe yachakumwa,+ ndikuwonjezera pa nsembe+ zimene inu mukupereka komanso pa utumiki wopatulika umene* mukuchita mokhulupirika. Choncho ndikusangalala ndipo nonsenu ndikukondwera nanu limodzi. 18 Ndikukulimbikitsani kuti inunso musangalale limodzi ndi ine.

19 Koma ine, ndikuyembekeza kuti Ambuye Yesu andilola kutumiza Timoteyo+ kwa inu posachedwapa kuti ndidzalimbikitsidwe ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu. 20 Chifukwa ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu. 21 Anthu ena onse akungoganizira zofuna zawo zokha, osati za Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa chitsanzo chabwino chimene Timoteyo anasonyeza, kuti monga mwana+ ndi bambo ake, watumikira ngati kapolo limodzi ndi ine pofalitsa uthenga wabwino. 23 Choncho, ndikuyembekezera kukutumizirani munthu ameneyu ndikangodziwa mmene zinthu zikhalire kwa ine. 24 Ndithudi, ndikukhulupirira kuti Ambuye andilola kuti inenso ndibwere posachedwa.+

25 Koma panopa ndikuona kuti ndi bwino kuti ndikutumizireni Epafurodito. Ameneyu ndi mʼbale wanga, wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga. Iye ndi nthumwi yanu komanso amanditumikira pa zosowa zanga.+ 26 Ndikufuna kumutumiza chifukwa akulakalaka kukuonani nonsenu ndipo akuvutika maganizo chifukwa munamva kuti ankadwala. 27 Nʼzoona kuti anadwaladi mpaka kutsala pangʼono kufa. Koma Mulungu anamuchitira chifundo. Ndipotu chifundo chimenecho sanachitire iye yekha, koma anachitiranso ine kuti chisoni changa chisawonjezeke. 28 Choncho, ndikumutumiza mofulumira kwambiri kuti inu mukamuona mukhalenso osangalala ndiponso kuti nkhawa zanga zichepe. 29 Ndiye monga mwa nthawi zonse, mulandireni ndi manja awiri ngati mmene mumachitira polandira otsatira a Ambuye. Mumulandire mwachimwemwe ndipo abale ngati amenewa muziwalemekeza kwambiri,+ 30 chifukwa anatsala pangʼono kufa pamene ankagwira ntchito ya Khristu* ndipo anaika moyo wake pachiswe* kuti adzanditumikire mʼmalo mwa inu, popeza simukanatha kubwera kuno kuti mudzandithandize.+

3 Pomalizira abale anga, pitirizani kusangalala monga otsatira a Ambuye.+ Kubwereza kulemba zinthu zimene ndinakulemberani kale si vuto kwa ine, koma ndi chitetezo kwa inu.

2 Chenjerani ndi anthu amene amachita zinthu ngati agalu. Chenjerani ndi anthu amene amavulaza anzawo. Chenjerani ndi anthu amene amachita mdulidwe.+ 3 Chifukwa ife tinachita mdulidwe weniweni,+ ife amene tikuchita utumiki wopatulika motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. Timadzitamandira mwa Khristu Yesu+ ndipo sitidalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, 4 ngakhale kuti ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika.

Ngati pali munthu wina amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndikuposa ameneyo, chifukwa: 5 ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini, ndine Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinkazunza mpingo.+ Kunena zochita chilungamo potsatira chilamulo, ndinasonyeza kuti ndilibe chifukwa chondinenezera. 7 Koma zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine ndikuziona kuti ndi zopanda phindu* chifukwa cha Khristu.+ 8 Zoonadi, ndimaona kuti zinthu zonse nʼzosapindulitsa chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Chifukwa cha iye, ndinataya zinthu zonse ndipo ndimaziona ngati mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu, 9 ndiponso kuti ndizionedwa kuti ndine wotsatira wake. Sikuti ndine wolungama chifukwa chakuti ndikuchita zonse moyenera potsatira Chilamulo, koma chifukwa chakuti ndimakhulupirira+ Khristu.+ Chilungamo chimenechi ndi chochokera kwa Mulungu ndipo chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro.+ 10 Cholinga changa nʼchoti ndimudziwe komanso kuti ndidziwe mphamvu za amene anamuukitsa kwa akufa.+ Ndikufunanso kuti ndivutike ngati mmene iye anavutikira,+ mpaka kulolera kufa ngati mmene iye anafera.+ 11 Ndachita zimenezi kuti ngati nʼkotheka ndidzapeze mwayi wodzauka kwa akufa pa kuuka koyamba.+

12 Sikuti ndalandira kale mphotoyo, kapena kuti ndakhala kale wangwiro ayi. Koma ndikuyesetsabe+ kuti ndikalandire mphoto chifukwa ndikudziwa kuti cholinga cha Khristu Yesu pondisankha chinali chimenechi.+ 13 Abale, ine sindikudziona ngati ndalandira kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo+ ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.+ 14 Ndikuyesetsa kuti ndikwaniritse cholinga changa chokalandira mphoto.+ Mphoto imeneyi ndi kukakhala ndi moyo kumwamba+ ndipo Mulungu adzaipereka kwa anthu amene anawaitana kudzera mwa Khristu Yesu. 15 Choncho, tiyeni tonse amene tili olimba mwauzimu+ tikhale ndi maganizo amenewa. Ndipo ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa pambali ina iliyonse, Mulungu adzakuululirani maganizo oyenerawo. 16 Komabe, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.

17 Abale, nonsenu muyesetse kumanditsanzira+ ndipo muzionetsetsa amene akuchita zinthu mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani. 18 Chifukwa pali anthu ambiri amene akuchita zinthu ngati adani a mtengo wozunzikirapo* wa Khristu. Kale ndinkawatchula pafupipafupi koma pano ndimawatchula ndikugwetsa misozi. 19 Anthu amenewo akuyembekezera kuwonongedwa ndipo mulungu wawo ndi mimba zawo. Iwo amanyadira zinthu zimene akuyenera kuchita nazo manyazi ndipo amangoganizira zinthu zapadziko lapansi.+ 20 Koma ife ndife nzika+ zakumwamba+ ndipo tikuyembekezera mwachidwi mpulumutsi wochokera kumeneko amene ndi Ambuye Yesu Khristu.+ 21 Iye adzasintha thupi lathu lonyozekali kuti lifanane* ndi thupi lake laulemerero.+ Adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu zimene zimamuthandiza kugonjetsa zinthu zonse kuti zikhale pansi pake.+

4 Choncho inu abale anga amene ndimakukondani ndipo ndikulakalaka kukuonani, ndinu chimwemwe changa ndi chipewa changa chaulemerero.+ Okondedwa anga, ndikukulimbikitsani kuti mupitirize kukhala okhulupirika+ kwa Ambuye.

2 Ndikudandaulira Eodiya komanso ndikudandaulira Suntuke kuti athetse kusemphana maganizo kwawo monga otsatira a Ambuye.*+ 3 Ndikupempha iwenso wantchito mnzanga weniweni,* kuti upitirize kuwathandiza azimayi amenewa. Iwo ayesetsa mwakhama kugwira ntchito yolengeza uthenga wabwino limodzi ndi ine. Achita zimenezi limodzinso ndi Kilementi komanso antchito anzanga ena onse amene mayina awo ali mʼbuku la moyo.+

4 Nthawi zonse muzisangalala chifukwa cha Ambuye. Ndikubwerezanso kunena kuti, Muzisangalala!+ 5 Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.+ Ambuye ali pafupi. 6 Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse.+ Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza.+ 7 Mukatero, mtendere+ wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu+ ndi maganizo anu pamene mukutsatira Khristu Yesu.

8 Chomalizira abale, pitirizani kuganizira* zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zolimbikitsa chikondi, zilizonse zimene anthu amaziyamikira, khalidwe labwino lililonse komanso chilichonse chotamandika.+ 9 Zinthu zimene munaphunzira, zimene munazivomereza, zimene munamva kwa ine komanso zimene munandiona ndikuchita, muzichita zimenezo+ ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

10 Ine ndikusangalala kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano mwayambiranso kundiganizira.+ Ndikudziwa kuti mwakhala mukundiganizira nthawi yonseyi, koma kungoti mumasowa mpata wosonyeza zimenezi. 11 Sindikulankhula zimenezi chifukwa chakuti ndikusowa kanthu, chifukwa ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wanga.+ 12 Ndikudziwa mmene zimakhalira ukakhala ndi zinthu zochepa+ komanso mmene umasangalalira ukakhala ndi zochuluka. Pa chilichonse komanso pa zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. Ndaphunziranso chinsinsi chokhala ndi zochuluka komanso chokhala wopanda kalikonse. 13 Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.+

14 Komabe, munachita bwino pondithandiza pa mavuto anga. 15 Ndipo inu Afilipi, mukudziwanso kuti pamene ndinkachoka ku Makedoniya, mutangomva kumene uthenga wabwino, panalibe mpingo ngakhale umodzi umene unathandizana nane pa nkhani ya kupatsa ndi kulandira, kupatulapo inu nokha.+ 16 Chifukwa pamene ndinali ku Tesalonika, inu munanditumizira kenakake kuti kandithandize pa zimene ndinkafunikira ndipo simunachite zimenezi kamodzi kokha, koma kawiri. 17 Sikuti ndikufuna kuti mundipatse mphatso, koma ndikufunitsitsa kuti muzichita zinthu zabwino zimene zingakupindulireni kwambiri. 18 Komabe, ine ndili ndi zonse zimene ndikufunikira ndipo zikuposa pa zimene ndikufunikira. Sindikusowa kanthu chifukwa Epafurodito+ wandipatsa zinthu zimene mwanditumizira. Zinthu zimenezi zili ngati fungo lonunkhira bwino+ ndiponso nsembe yovomerezeka yomwe ndi yosangalatsa kwa Mulungu. 19 Chifukwa cha zimenezi, Mulungu wanga adzakupatsani zonse zimene mukufunikira+ mogwirizana ndi kuchuluka kwa chuma chake chaulemerero, kudzera mwa Khristu Yesu. 20 Tsopano Mulungu amene ndi Atate wathu alandire ulemerero mpaka muyaya. Ame.

21 Mundiperekere moni kwa woyera aliyense amene ndi wophunzira wa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akukupatsani moni. 22 Oyera onse akupereka moni, koma makamaka a mʼnyumba ya Kaisara.+

23 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu, chifukwa muli ndi maganizo abwino.

Kapena kuti, “chifukwa cha kudzipereka kwanu polalikira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kudzera mʼthupi langa.”

Kapena kuti, “nʼchakuti muzichita zinthu monga nzika mogwirizana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mumzimu umodzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wokonda kugawana mzimu kulikonse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala wofanana ndi anthu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “atayamba kuoneka ngati munthu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kutanthauza anthu amene anamwalira ndipo adzaukitsidwa.

Kapena kuti, “pa ntchito yotumikira anthu imene.”

Mabaibulo ena amati, “ntchito ya Ambuye.”

Kapena kuti, “anaika moyo wake pangozi.”

Mabaibulo ena amati, “ndinazisiya mwakufuna kwanga.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ligwirizane.”

Kapena kuti, “kuti akhale ndi maganizo amodzi pamene akutumikira Ambuye.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mnzanga weniweni wosenza naye limodzi goli.”

Kapena kuti, “kuganizira mozama.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena