Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 17:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova anali kuchenjeza+ Aisiraeli+ ndi Ayuda+ kudzera mwa aneneri ake onse+ ndi wamasomphenya aliyense,+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo sungani malamulo anga,+ mogwirizana ndi chilamulo chonse+ chimene ndinalamula makolo anu,+ ndi chimene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”+

  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+

  • Yeremiya 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka, ndipo ndikuganizira zokuchitani chinthu choipa.+ Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.”’”+

  • Yeremiya 35:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri,+ kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza. Ndinali kuwatuma uthenga wakuti, ‘Bwererani chonde, aliyense asiye njira zake zoipa+ ndipo sinthani zochita zanu kuti zikhale zabwino.+ Musatsatire milungu ina ndi kuitumikira.+ Mupitirize kukhala m’dziko limene ndinakupatsani, inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera.+

  • Ezekieli 18:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 “‘Chotero ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Lapani ndi kusiya zolakwa zanu zonse+ ndipo musalole kuti chilichonse chizikupunthwitsani ndi kukulakwitsani.+

  • Ezekieli 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere+ kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+

  • Yona 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu ndi mphamvu zawo zonse, ndipo aliyense asiye njira zake zoipa+ ndi zinthu zonse zachiwawa zimene amachita.

  • Zekariya 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+

      “‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.

  • Malaki 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kuyambira m’masiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawasunge.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa makamu.

      Koma inu mukunena kuti: “Tibwerere motani?”

  • 2 Petulo 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena