Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Kumbukirani izi: Simuyenera kuiwala mmene munaputira Yehova Mulungu wanu m’chipululu.+ Anthu inu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova kuyambira tsiku limene munatuluka m’dziko la Iguputo mpaka kudzafika malo ano.+

  • 2 Mafumu 17:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo,+ ndipo anapitiriza kumanga malo okwezeka+ m’mizinda yawo yonse, kuyambira kunsanja+ ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.

  • Nehemiya 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu.

  • Salimo 106:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+

      Tachita zinthu zosayenera, tachita zinthu zoipa.+

  • Yeremiya 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “M’kupita kwa nthawi, ndinakulowetsani m’dziko la minda ya zipatso kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino za m’dzikolo,+ koma munalowa m’dziko langa ndi kuliipitsa. Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+

  • Yeremiya 3:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Tagona pansi mwamanyazi+ ndipo manyazi athuwo akupitiriza kutiphimba.+ Zimenezi zakhala choncho chifukwa chakuti ifeyo ndi makolo athu, tachimwira Yehova Mulungu wathu+ ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu+ kuyambira tili anyamata mpaka lero.”+

  • Ezekieli 16:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘Ndinadutsa pafupi nawe n’kukuona, ndipo ndinaona kuti inali nthawi yako yoti uchite zachikondi.+ Chotero ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinakulumbirira n’kuchita nawe pangano+ ndipo unakhala wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

  • Ezekieli 20:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko+ limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali+ ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+

  • Machitidwe 7:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena