ESITERE
1 Ahasiwero,* ankalamulira zigawo 127+ kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya,* ndipo mʼmasiku ake, 2 mfumuyi inkakhala pampando wake mʼnyumba yachifumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*+ 3 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wake, Ahasiwero anakonzera phwando akalonga ndi atumiki ake onse. Asilikali a Perisiya+ ndi Mediya,+ anthu olemekezeka ndiponso akalonga amʼzigawo za ufumu wake analinso pomwepo. 4 Ndipo kwa masiku ambiri, masiku okwana 180, iye anaonetsa anthuwo chuma chimene chinkachititsa kuti anthu azimulemekeza mu ufumu wake. Anawaonetsanso chuma ndi ulemerero wa ufumu wakewo. 5 Zimenezi zitatha, mfumu inakonza phwando la masiku 7 pabwalo la nyumba yake pomwe anadzalapo maluwa. Phwandoli inakonzera anthu onse, kaya olemekezeka kapena anthu wamba, amene ankakhala kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.* 6 Panali makatani a nsalu zoyera, makatani opangidwa ndi thonje labwino kwambiri ndi makatani abuluu. Makataniwo anawamanga ndi zingwe zopangidwa ndi nsalu zabwino kwambiri ndipo anawapachika mʼmikombero yasiliva yokulungidwa ndi ulusi wapepo. Mikomberoyo anaikoleka pa zipilala za miyala ya mabo. Panalinso mipando yagolide ndi siliva yokhala ngati mabedi imene inali pakhonde la miyala ya pofeli,* miyala yoyera ya mabo, ngale ndi miyala yakuda ya mabo.
7 Panali vinyo yemwe anthu ankamwera mʼmakapu agolide. Kapu iliyonse inali yosiyana ndi inzake, ndipo vinyo amene mfumu inapereka anali wambiri, mogwirizana ndi chuma cha mfumuyo. 8 Lamulo limene ankatsatira linali lakuti aliyense amwe mmene akufunira chifukwa mfumu ndi akuluakulu ogwira ntchito kunyumba yake anakonza zoti aliyense amwe mmene akufunira.
9 Nayenso Mfumukazi Vasiti+ anakonzera phwando azimayi kunyumba yachifumu ya Mfumu Ahasiwero.
10 Pa tsiku la 7, mtima wa mfumu utasangalala chifukwa chomwa vinyo, mfumuyo inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 zomwe zinkatumikira Mfumu Ahasiwero, 11 kuti akatenge Mfumukazi Vasiti nʼkubwera naye kwa mfumu atavala duku lachifumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kukongola kwake, chifukwa analidi wokongola kwambiri. 12 Koma Mfumukazi Vasiti anakana atauzidwa ndi nduna zapanyumba ya mfumu kuti mfumu yalamula kuti apite. Zitatero mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inapsa mtima.
13 Ndiyeno mfumu inalankhula ndi amuna anzeru, odziwa miyambo ya masiku amenewo. (Zimenezi zinkathandiza kuti nkhani zokhudza mfumu zifike kwa anthu onse odziwa malamulo komanso milandu. 14 Alangizi amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali Karisena, Setara, Adimata, Tarisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, akalonga 7+ a Perisiya ndi Mediya, amene ankafika kwa mfumu komanso anali ndi maudindo akuluakulu mu ufumuwo.) 15 Mfumu inawafunsa kuti: “Mogwirizana ndi malamulo, kodi tichite chiyani ndi Mfumukazi Vasiti popeza sanamvere zimene Mfumu Ahasiwero yanena kudzera mwa nduna zake?”
16 Memukani anauza mfumu ndi akalonga kuti: “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha,+ koma walakwiranso akalonga onse ndi anthu onse amʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero. 17 Chifukwa zimene mfumukazi yachita zidziwika kwa akazi onse okwatiwa ndipo ayamba kunyoza amuna awo nʼkumanena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero anaitana Mfumukazi Vasiti, koma Vasiti anakana.’ 18 Lero akazi a akalonga a Perisiya ndi Mediya amene amva zimene mfumukazi yachita, alankhula za zimenezi ndi amuna awo ndipo zichititsa kuti ayambe kunyozana kwambiri ndiponso kukwiyitsana. 19 Ngati mungavomereze mfumu, mupereke lamulo ndipo lamuloli lilembedwe mʼmalamulo a Perisiya ndi Mediya omwe sasintha.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke udindo wake kwa mkazi wina, wabwino kuposa iyeyo. 20 Anthu akamva za lamulo limene muperekeli mu ufumu wanu wonse, womwe ndi waukulu, akazi onse okwatiwa azilemekeza amuna awo, kaya amunawo ndi olemekezeka kapena anthu wamba.”
21 Mawu amenewa anasangalatsa mfumu ndi akalonga, ndipo mfumuyo inachita zimene Memukani ananena. 22 Choncho mfumu inatumiza makalata mʼzigawo zonse za ufumu wake.+ Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu akumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Anachita izi kuti mwamuna aliyense azitsogolera banja lake ndiponso kuti banjalo lizilankhula chilankhulo cha mwamunayo.
2 Kenako mkwiyo wa Mfumu Ahasiwero+ utachepa, anakumbukira zimene Vasiti anachita,+ komanso chilango chimene anapatsidwa.+ 2 Ndiyeno atumiki a mfumu anati: “Pakhale anthu oti akufufuzireni inu mfumu anamwali okongola. 3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Anthuwo asonkhanitse anamwali okongola kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndipo azikhala mʼnyumba ya akazi. Atsikanawa aziyangʼaniridwa ndi Hegai,+ munthu wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa. 4 Mtsikana amene mfumu idzasangalale naye kwambiri adzakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.”+ Mawu amenewa anasangalatsa mfumu ndipo inachitadi zomwezo.
5 Panali munthu wina, Myuda, amene ankakhala kunyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Dzina lake anali Moredikayi.+ Moredikayi anali mwana wa Yairi, Yairi anali mwana wa Simeyi ndipo Simeyi anali mwana wa Kisi wa fuko la Benjamini.+ 6 Moredikayi ndi anthu ena anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo pamodzi ndi Yekoniya*+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anamutenga kupita naye ku ukapolo. 7 Moredikayi ndi amene ankalera Hadasa,* amene ndi Esitere, mwana wa achimwene awo a bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri. Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredikayi anamʼtenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake. 8 Ndiyeno anthu atalengeza mawu a mfumu ndiponso lamulo lake, komanso atasonkhanitsa atsikana ambiri kunyumba ya mfumu ku Susani* kuti Hegai aziwayangʼanira,+ Esitere nayenso anatengedwa kupita kunyumba ya mfumuyo kuti azikayangʼaniridwa ndi Hegai amene ankayangʼanira akazi.
9 Hegai anasangalala naye mtsikanayu moti ankamukomera mtima.* Choncho nthawi yomweyo anakonza za mafuta okongoletsa oti azipakidwa+ komanso chakudya choti azipatsidwa. Anamupatsanso atsikana 7 amene anachita kuwasankha kuchokera kunyumba ya mfumu. Kenako anamusamutsa pamodzi ndi atsikanawo nʼkuwapatsa malo abwino kwambiri mʼnyumba ya akaziyo. 10 Esitere sananene za mtundu wa anthu ake+ kapena za abale ake, chifukwa Moredikayi+ anali atamulangiza kuti asauze aliyense.+ 11 Tsiku lililonse Moredikayi ankadutsa kutsogolo kwa bwalo la nyumba ya akazi kuti adziwe ngati Esitere ali bwino komanso zimene zikumuchitikira.
12 Mtsikana aliyense ankakhala ndi nthawi yake yokaonekera kwa Mfumu Ahasiwero akamaliza kumuchitira zonse zimene amayenera kuwachitira akazi pa miyezi 12. Atsikanawo ankawapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako nʼkuwapakanso mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ankakhala kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera. 13 Akatero mtsikana aliyense ankapita kwa mfumu. Akamachoka kunyumba ya akazi kupita kunyumba ya mfumu, ankamupatsa chilichonse chimene wapempha. 14 Mtsikanayo ankapita kwa mfumu madzulo nʼkubwerako mʼmawa ndipo ankapita kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi ankayangʼanira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu+ yemwe ankayangʼanira akazi aangʼono* a mfumu. Mtsikanayo sankapitanso kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yasangalala naye ndipo yamuitanitsa pomutchula dzina.+
15 Esitere anali mwana wa Abihaili, mchimwene wawo wa bambo ake a Moredikayi. Moredikayi anamutenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake.+ Ndiyeno nthawi yoti Esitere akaonekere kwa mfumu itakwana, sanapemphe kalikonse kupatulapo zimene Hegai anamuuza. Hegai anali munthu wofulidwa wa mfumu amenenso ankayangʼanira akazi. (Pa nthawi yonseyi aliyense womuona Esitere ankamukonda.) 16 Esitere anapita naye kunyumba yachifumu ya Mfumu Ahasiwero mʼmwezi wa 10 umene ndi mwezi wa Tebeti,* mʼchaka cha 7+ cha ulamuliro wa mfumuyi. 17 Ndiyeno mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti inasangalala naye ndipo inaona kuti ndi wabwino* kuposa anamwali ena onse. Choncho mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake nʼkumuika kukhala mfumukazi+ mʼmalo mwa Vasiti.+ 18 Kenako mfumu inakonzera akalonga ake ndi atumiki ake onse phwando lalikulu, phwando la Esitere. Ndiyeno mfumu inamasula akaidi amʼzigawo zake zonse, ndipo inayamba kupereka mphatso mogwirizana ndi chuma chimene mfumuyo inali nacho.
19 Pamene anamwali*+ anasonkhanitsidwa kachiwiri, Moredikayi anali atakhala pansi kugeti la mfumu. 20 Esitere sananene zokhudza abale ake ndiponso anthu a mtundu wake,+ mogwirizana ndi zimene Moredikayi anamulangiza. Esitere ankachita zimene Moredikayi wanena ngati mmene ankachitira pa nthawi imene ankakhala naye.+
21 Mʼmasiku amenewo, pamene Moredikayi ankakhala pageti la mfumu, Bigitana ndi Teresi, omwe anali nduna ziwiri zapanyumba ya mfumu, omwenso anali alonda apakhomo, anakwiya ndipo anakonza zoti aphe Mfumu Ahasiwero. 22 Koma Moredikayi anamva zimenezi ndipo nthawi yomweyo anauza Mfumukazi Esitere. Kenako Esitere anakalankhula ndi mfumu mʼmalo mwa Moredikayi.* 23 Choncho nkhaniyi inafufuzidwa ndipo zinadziwika kuti inali yoona, moti Bigitana ndi Teresi anapachikidwa pamtengo. Zimenezi zinalembedwa pamaso pa mfumu mʼbuku la mbiri ya masiku amenewo.+
3 Kenako Mfumu Ahasiwero anakweza pa udindo Hamani+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ ndipo anamupatsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse a mfumuyo.+ 2 Choncho atumiki onse a mfumu amene ankakhala pageti la mfumu ankaweramira Hamani ndiponso kumugwadira chifukwa mfumu ndi imene inalamula kuti azimuchitira zimenezi. Koma Moredikayi ankakana kumuweramira kapena kumugwadira. 3 Choncho atumiki a mfumu amene ankakhala pagetiwo anafunsa Moredikayi kuti: “Nʼchifukwa chiyani sukutsatira lamulo la mfumu?” 4 Ankamufunsa zimenezi tsiku ndi tsiku koma iye sankawamvera. Kenako anthuwo anauza Hamani kuti aone ngati khalidwe la Moredikayi lingalekereredwe+ popeza iye anali atawauza kuti anali Myuda.+
5 Hamani ataona kuti Moredikayi sankamuweramira ndiponso kumugwadira, anakwiya kwambiri.+ 6 Koma Hamani anaona kuti nʼzosakwanira kupha Moredikayi yekha chifukwa anthu anali atamuuza za anthu a mtundu wa Moredikayi. Choncho Hamani anaganiza zoti aphe Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredikayi mʼmadera onse amene Ahasiwero ankalamulira.
7 Ndiyeno mʼmwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, anthu anachita Puri+ kapena kuti maere pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 8 Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu+ umene ukupezeka paliponse mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira malamulo anu. Choncho ngati mungawasiye anthu amenewa, zinthu sizikuyenderani bwino mfumu. 9 Ngati mungakonde mfumu, palembedwe lamulo loti anthu amenewa aphedwe. Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente* 10,000 asiliva kwa akuluakulu ogwira ntchito kunyumba ya mfumu kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu.”*
10 Zitatero mfumu inavula mphete yake yodindira+ nʼkuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ yemwe ankadana kwambiri ndi Ayuda. 11 Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva* komanso anthuwo ndakupatsa ndipo uchite nawo zilizonse zimene ukufuna.” 12 Kenako pa tsiku la 13 la mwezi woyamba, alembi a mfumu+ anaitanidwa. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a mʼzigawo zosiyanasiyana ndiponso akalonga a anthu osiyanasiyana. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu a kumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Makalatawa anawalemba mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yodindira ya mfumuyo.+
13 Makalatawo anawatumiza kuzigawo zonse za mfumu kudzera mwa anthu operekera makalata. Anachita izi kuti tsiku limodzi, tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ aphe Ayuda onse, kaya ndi achinyamata, amuna achikulire, ana ndiponso akazi nʼkutenga zinthu zawo.+ 14 Lamulo lopita kuzigawo zonse, limene analilemba mʼmakalatawo, linafalitsidwa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15 Mfumu inalamula kuti operekera makalatawo apite mwamsanga.+ Lamuloli linaperekedwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako mfumu ndi Hamani, anakhala pansi nʼkumamwa vinyo, koma mumzinda wa Susani munali chipwirikiti.
4 Moredikayi+ atadziwa zonse zimene zinachitika,+ anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli ndipo anadzithira phulusa. Kenako anapita pakati pa mzinda nʼkuyamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima. 2 Koma anangofika pageti la mfumu chifukwa palibe amene ankaloledwa kulowa pageti la mfumu atavala chiguduli. 3 Ndipo mʼzigawo zonse+ kumene kunafika mawu a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali ndi chisoni kwambiri ndipo ankasala kudya+ komanso kulira mofuula. Ambiri ankagona paziguduli ndi paphulusa.+ 4 Atsikana otumikira Mfumukazi Esitere ndiponso amuna ofulidwa amene ankamuyangʼanira atabwera nʼkudzamuuza zimenezi, zinamukhudza kwambiri. Choncho anatumiza zovala kuti Moredikayi akavale mʼmalo mwa zigudulizo, koma Moredikayi anakana. 5 Ndiyeno Esitere anaitana Hataki, mmodzi wa amuna ofulidwa a mfumu amene mfumuyo inamuika kuti azitumikira Esitere. Ndipo anamutuma kwa Moredikayi kuti akafufuze zimene zachitika.
6 Choncho Hataki anapita kwa Moredikayi kubwalo la mzinda limene linali kutsogolo kwa geti la mfumu. 7 Moredikayi anauza Hataki zonse zimene zinamuchitikira. Anamuuzanso zokhudza ndalama zonse+ zimene Hamani analonjeza kuti apereka mosungiramo chuma cha mfumu, nʼcholinga choti aphe Ayuda.+ 8 Anamupatsanso kalata imene munali lamulo lochokera ku Susani*+ loti Ayuda onse aphedwe. Anamupatsa kalatayi kuti akaonetse Esitere ndiponso akamufotokozere mmene zinthu zilili. Moredikayi anauzanso Hataki kuti akauze Esitere+ kuti akaonekere kwa mfumu nʼkupempha kuti imuchitire chifundo ndiponso kuti akachonderere mfumuyo pamasomʼpamaso mʼmalo mwa anthu a mtundu wake.
9 Ndiyeno Hataki anapita kukauza Esitere zimene Moredikayi ananena. 10 Kenako Esitere anauza Hataki kuti akauze Moredikayi kuti:+ 11 “Atumiki onse a mfumu ndi anthu amʼzigawo zonse za mfumu akudziwa kuti, pali lamulo lakuti mwamuna kapena mkazi aliyense wopita mʼbwalo lamkati+ la mfumu asanaitanidwe, ayenera kuphedwa. Munthu saphedwa pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide.+ Ndiye ine sindinaitanidwe kukaonekera kwa mfumu kwa masiku 30 tsopano.”
12 Moredikayi atauzidwa zimene Esitere ananena, 13 anayankha Esitere kuti: “Usaganize kuti chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu, iweyo udzapulumuka Ayuda onse akamadzaphedwa. 14 Ngati iwe ungakhale chete panopa, thandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zichokera kwina.+ Koma iweyo ndi anthu a mʼnyumba ya bambo ako, nonse mudzaphedwa. Ndipo ndani akudziwa? Mwina iwe unakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.”+
15 Esitere anayankha Moredikayi kuti: 16 “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene ali ku Susani* ndipo musale kudya+ mʼmalo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ masana ndiponso usiku. Inenso ndi atsikana onditumikira tisala kudya. Ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu ndipo ngati nʼkufa, ndife.” 17 Choncho Moredikayi anapita kukachita zonse zimene Esitere anamuuza.
5 Pa tsiku lachitatu,+ Esitere anavala zovala zachifumu nʼkukaima mʼbwalo lamkati la nyumba ya mfumu kutsogolo kwa nyumba ya mfumuyo. Pa nthawiyi nʼkuti mfumu itakhala pampando wake wachifumu mʼnyumba yakeyo pafupi ndi khomo la nyumbayo. 2 Mfumuyo itangoona Mfumukazi Esitere ataima mʼbwalo la nyumba ya mfumu, inasangalala moti inamuloza ndi ndodo yachifumu yagolide+ imene inali mʼmanja mwake. Kenako Esitere anayandikira nʼkugwira kutsogolo kwa ndodoyo.
3 Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Chavuta nʼchiyani Mfumukazi Esitere? Ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.” 4 Esitere anati: “Ngati mungavomereze mfumu, inu ndi Hamani+ mubwere lero kuphwando limene ine ndakukonzerani.” 5 Ndiyeno mfumu inauza atumiki ake kuti: “Pitani mukamuuze Hamani kuti abwere mofulumira mogwirizana ndi zimene Esitere wapempha.” Choncho mfumu ndi Hamani anapita kuphwando limene Esitere anakonza.
6 Pa nthawi yomwe ankamwa vinyo paphwandolo, mfumu inafunsa Esitere kuti: “Ukufuna kupempha chiyani? Chimene ukufuna ndikupatsa. Ukufuna ndikupatse chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.”+ 7 Esitere anayankha kuti: “Pempho langa ndi ili, 8 Ngati mungandikomere mtima mfumu ndiponso ngati mungakonde kundipatsa zimene ndapempha nʼkuchita zomwe ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzereni mawa. Ndipo mawa ndidzakuuzani pempho langa ngati mmene inu mfumu mwanenera.”
9 Pa tsikuli Hamani anatuluka ali wosangalala kwambiri. Koma atangoona Moredikayi pageti la mfumu nʼkuonanso kuti sanaimirire ndi kumunjenjemerera, Hamani anamukwiyira kwambiri Moredikayi.+ 10 Koma Hamani anaugwira mtima ndipo anapita kunyumba kwake. Kenako anaitanitsa anzake ndi mkazi wake Zeresi.+ 11 Ndiyeno Hamani anayamba kudzitama kuti ali ndi chuma chambiri, ana aamuna ambiri+ ndiponso kuti mfumu inamukweza pa udindo kuposa akalonga ndi atumiki ena onse a mfumuyo.+
12 Hamani ananenanso kuti: “Kuwonjezera pamenepo, Mfumukazi Esitere sanaitane wina aliyense kuphwando limene anakonza,+ koma anaitana ineyo kuti ndipite ndi mfumu, ndipo mawa wandiitananso pamodzi ndi mfumu.+ 13 Koma zonsezi sizikundikwanira ndikamaona Moredikayi, Myuda, atakhala pageti la mfumu.” 14 Choncho mkazi wake Zeresi ndiponso anzake onsewo anamuuza kuti: “Mukonzetse mtengo wautali mikono 50.* Ndiyeno mawa mʼmawa mukauze mfumu kuti Moredikayi apachikidwe pamtengowo.+ Mukatero mukapite ndi mfumu kuphwandoko kukasangalala.” Hamani anaona kuti maganizo amenewa ndi abwino, choncho anakonzetsa mtengowo.
6 Usiku wa tsiku limenelo mfumu inasowa tulo. Choncho inaitanitsa buku lomwe ankalembamo zochitika za masiku amenewo+ ndipo anayamba kuwerengera mfumu zimene zinalembedwa mʼbukulo. 2 Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zimene Moredikayi anaulula zokhudza Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri zapanyumba ya mfumu, alonda apakhomo, amene ankafuna kupha Mfumu Ahasiwero.+ 3 Ndiyeno mfumu inafunsa kuti: “Kodi Moredikayi analandira ulemu wotani chifukwa cha zimene anachitazi?” Atumiki a mfumu anayankha kuti: “Palibe chilichonse chimene anachitiridwa.”
4 Kenako mfumu inati: “Kodi pabwalopo pali ndani?” Pa nthawiyi nʼkuti Hamani atafika pabwalo lakunja+ la nyumba ya mfumu kudzakambirana ndi mfumuyo zoti Moredikayi apachikidwe pamtengo umene anamukonzera.+ 5 Atumiki a mfumu anati: “Pabwalo pali Hamani.”+ Ndiyeno mfumu inati: “Muuzeni alowe.”
6 Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti: “Kodi tingamuchitire chiyani munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemu?” Hamani atamva zimenezi anaganiza kuti: “Kodi winanso ndani amene mfumu ingafune kumupatsa ulemu kuposa ine?”+ 7 Choncho Hamani anauza mfumu kuti: “Munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemu, 8 amubweretsere zovala zachifumu zimene mfumu imavala+ ndi hatchi* imene mfumu imakwera ndipo hatchiyo aiveke duku lachifumu. 9 Ndiyeno chovalacho ndi hatchiyo azipereke kwa mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu. Kenako aveke chovalacho munthu amene mfumu ikufuna kumupatsa ulemuyo ndipo amukweze pahatchiyo nʼkumuyendetsa mʼbwalo la mzinda. Ndiye azifuula patsogolo pake kuti, ‘Izi ndi zimene timachitira munthu amene mfumu yafuna kumʼpatsa ulemu!’”+ 10 Nthawi yomweyo mfumu inauza Hamani kuti: “Fulumira, tenga chovala ndi hatchi ngati mmene wanenera, ndipo ukachitire zimenezi Moredikayi, Myuda, amene ali kugeti. Uonetsetse kuti wachita zonse zimene wanenazi.”
11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi hatchi, ndipo anaveka Moredikayi+ chovalacho. Kenako anamʼkweza pahatchiyo nʼkumuyendetsa mʼbwalo la mzinda, akufuula patsogolo pake kuti: “Izi ndi zimene timachitira munthu amene mfumu yafuna kumʼpatsa ulemu!” 12 Kenako, Moredikayi anabwerera kugeti la mfumu. Koma Hamani anapita kunyumba kwake mofulumira, akulira ndiponso ataphimba kumutu. 13 Hamani atafotokozera mkazi wake Zeresi+ ndiponso anzake onse zonse zimene zinamuchitikira, amuna anzeru amene ankamutumikira komanso mkazi wakeyo anati: “Ngati wayamba kufooka pamaso pa Moredikayi, yemwe ndi Myuda, ndiye kuti supambana koma akugonjetsa ndithu.”
14 Ali mkati mokambirana nkhaniyi, nduna zakunyumba ya mfumu zinafika, ndipo nthawi yomweyo zinatenga Hamani nʼkupita naye kuphwando limene Esitere anakonza.+
7 Kenako mfumu ndi Hamani+ anafika kuphwando limene Mfumukazi Esitere anakonza. 2 Pa tsiku lachiwiri la phwando, pamene ankamwa vinyo, mfumu inafunsanso Esitere kuti: “Ukufuna chiyani Mfumukazi Esitere? Chilichonse chimene ukufuna ndikupatsa. Ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.”+ 3 Mfumukazi Esitere anayankha kuti: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndiponso ngati mungandichitire chifundo, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso muteteze anthu a mtundu wanga.+ 4 Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa+ kuti tonse tiphedwe.+ Tikanagulitsidwa kuti tikhale akapolo aamuna ndi aakazi, sindikanalankhula kanthu. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike, chifukwa libweretsanso mavuto kwa inu mfumu.”
5 Zitatero, Mfumu Ahasiwero anafunsa Mfumukazi Esitere kuti: “Wachita zimenezo ndi ndani? Ali kuti munthu amene walimba mtima kuchita zimenezo?” 6 Esitere anati: “Munthu wake ndi Hamani ali apayu, mdani wathu ndiponso munthu woipa.”
Hamani anachita mantha chifukwa cha mfumu ndi mfumukazi. 7 Ndiyeno mfumu inanyamuka paphwandolo itakwiya kwambiri nʼkupita kumunda wamaluwa wapanyumba ya mfumu. Zitatero Hamani ananyamuka kuti achonderere Mfumukazi Esitere kuti ipulumutse moyo wake, chifukwa anadziwa kuti mfumu yatsimikiza kuti imupatse chilango. 8 Kenako mfumu inabwera kuchokera kumunda wamaluwa uja nʼkulowanso mʼnyumba imene munali phwando la vinyo. Ndipo inapeza Hamani atadzigwetsa pampando wokhala ngati bedi pamene panali Esitere. Choncho mfumu inati: “Kodi akufunanso kugwirira mfumukazi mʼnyumba mwanga momwe?” Mfumu itangolankhula zimenezi, anthu anamuphimba nkhope Hamani. 9 Ndiyeno Haribona,+ mmodzi mwa nduna zapanyumba ya mfumu, anati: “Hamani anapanganso mtengo woti apachikepo Moredikayi,+ amene anapereka lipoti lomwe linapulumutsa mfumu.+ Mtengowo ndi wautali mikono 50* ndipo uli kunyumba kwa Hamani.” Zitatero mfumu inati: “Kamʼpachikeni pamtengo womwewo.” 10 Choncho Hamani anamupachika pamtengo umene anakonzera Moredikayi, ndipo mkwiyo wa mfumu unatha.
8 Pa tsikuli, Mfumu Ahasiwero anapereka kwa Mfumukazi Esitere nyumba ya Hamani,+ yemwe anali mdani wa Ayuda.+ Ndipo Moredikayi anapita kwa mfumu chifukwa Esitere anali atafotokozera mfumuyo chibale chomwe chinali pakati pawo.+ 2 Kenako mfumu inavula mphete yake yodindira+ imene inalanda Hamani nʼkuipereka kwa Moredikayi. Ndiyeno Esitere anaika Moredikayi kuti aziyangʼanira nyumba ya Hamani.+
3 Kuwonjezera pamenepo, Esitere analankhulanso ndi mfumu. Iye anagwada pamapazi a mfumuyo ndipo anachonderera kuti mfumu isinthe chiwembu chimene Hamani, mbadwa ya Agagi, anakonzera Ayuda.+ 4 Ndiyeno mfumu inaloza Esitere ndi ndodo yachifumu yagolide+ ndipo Esitere anadzuka nʼkuima pamaso pa mfumu. 5 Kenako Esitere ananena kuti: “Ngati mungavomereze mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima, komanso ngati inu mfumu mukuona kuti nʼzoyenera ndipo mukusangalala nane, palembedwe lamulo lofafaniza zimene zinalembedwa mʼmakalata amene munthu wachiwembu Hamani,+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ analemba pofuna kupha Ayuda amene ali mʼzigawo zanu zonse mfumu. 6 Ndidzapirira bwanji kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndipo ndidzapirira bwanji kuona abale anga akuphedwa?”
7 Choncho Mfumu Ahasiwero anauza Mfumukazi Esitere ndi Moredikayi Myuda kuti: “Nyumba ya Hamani ndaipereka kwa Esitere,+ ndipo Hamaniyo ndinalamula kuti apachikidwe pamtengo+ chifukwa anakonza chiwembu choti aphe Ayuda. 8 Ndiye inu lembani makalata mʼmalo mwa Ayuda. Mulembe mʼdzina la mfumu zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino ndipo mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu. Chifukwa nʼzosatheka kufafaniza lamulo limene lalembedwa mʼdzina la mfumu nʼkudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+
9 Choncho pa nthawiyi anaitana alembi a mfumu. Limeneli linali tsiku la 23 la mwezi wachitatu womwe ndi mwezi wa Sivani.* Iwo analemba zonse zimene Moredikayi analamula Ayuda kuti achite. Makalatawo analinso opita kwa masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi akalonga amʼzigawo zonse+ kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya, zigawo 127. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu akumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Nawonso Ayuda anawalembera mogwirizana ndi kalembedwe kawo ndiponso chilankhulo chawo.
10 Moredikayi analemba makalatawo mʼdzina la Mfumu Ahasiwero nʼkuwadinda ndi mphete yodindira ya mfumu.+ Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa anthu operekera makalata okwera pamahatchi. Iwo anapita pamahatchi aliwiro amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu. 11 Mʼmakalatawo mfumu inapereka chilolezo kwa Ayuda mʼmizinda yosiyanasiyana kuti asonkhane nʼcholinga choti adziteteze komanso aphe asilikali a gulu lililonse kapena chigawo chilichonse amene angawaukire, kuphatikizapo akazi ndi ana nʼkutenga zinthu zawo.+ 12 Zimenezi zinkayenera kuchitika mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku la 13 lomwelo la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 13 Zimene analemba mʼmakalatawo anazipereka kuti zikhale lamulo mʼzigawo zonse. Analengeza kwa anthu a mitundu yonse nʼcholinga choti Ayuda akonzekere kudzabwezera adani awo pa tsiku limeneli.+ 14 Anthu operekera makalatawo anapita mofulumira atakwera pamahatchi amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu ndipo anachita zimenezi chifukwa cha lamulo la mfumu. Lamuloli linaperekedwanso kunyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
15 Ndiyeno Moredikayi anachoka pamaso pa mfumu atavala chovala chachifumu chansalu yabuluu ndi yoyera. Analinso atavala chipewa chachikulu chachifumu chagolide ndiponso mkanjo wa nsalu yabwino kwambiri yaubweya wa nkhosa wapepo.+ Ndipo anthu amumzinda wa Susani* anafuula chifukwa chosangalala. 16 Ayuda anaona kuti imeneyi inali nkhani yabwino moti anayamba kusangalala ndi kukondwera ndipo anthu ankawalemekeza. 17 Mʼzigawo zonse ndiponso mʼmizinda yonse kumene lamulo la mfumu linafika, Ayuda ankasangalala, kukondwera ndiponso kuchita phwando komanso zikondwerero. Anthu ambiri amʼdzikomo anayamba kunena kuti ndi Ayuda+ chifukwa ankaopa kwambiri Ayudawo.
9 Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,*+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda ankayembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayuda ndi amene anagonjetsa adani awowo.+ 2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda yawo mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero+ kuti amenyane ndi adani awo amene ankafuna kuwapha. Ndipo palibe munthu amene anakwanitsa kulimbana nawo chifukwa anthu a mitundu yonse ankaopa Ayudawo.+ 3 Akalonga onse a mʼzigawo, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi onse ogwira ntchito za mfumu ankathandiza Ayudawo chifukwa ankaopa Moredikayi. 4 Moredikayi anali ndi mphamvu zambiri+ mʼnyumba ya mfumu ndipo anatchuka mʼzigawo zonse chifukwa anapitiriza kukhala ndi mphamvu.
5 Ndiyeno Ayuda anapha adani awo onse ndi lupanga. Ayudawo anachita zonse zimene ankafuna kwa adani awo.+ 6 Kunyumba ya mfumu ya ku Susani,*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, Ayudawo anapha amuna 500. 7 Anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaizata, 10 omwe anali ana aamuna 10 a Hamani mwana wa Hamedata yemwe ankadana ndi Ayuda.+ Koma atawapha, sanatenge zinthu zawo.+
11 Pa tsikuli mfumu inauzidwa chiwerengero cha anthu amene anaphedwa kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
12 Ndiyeno mfumu inauza Mfumukazi Esitere kuti: “Kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, Ayuda apha amuna 500 komanso ana 10 a Hamani. Ndiye kuli bwanji mʼzigawo zina zonse za mfumu?+ Panopa ukufuna kupempha chiyani? Ndikupatsa. Pali zinanso zimene ukufuna kupempha? Zimene ukufuna zichitika.” 13 Esitere anayankha kuti: “Ngati mungavomereze mfumu,+ bwanji mawa Ayuda amene ali ku Susani* achitenso zimene lamulo laleroli likunena?+ Ndikupemphanso kuti ana aamuna 10 a Hamani apachikidwe pamtengo.”+ 14 Choncho mfumu inalamula kuti achite zimenezo ndipo lamulo linaperekedwa ku Susani.* Komanso ana aamuna 10 a Hamani anapachikidwa.
15 Ndiyeno Ayuda amene anali ku Susani* anasonkhananso pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara,+ ndipo anapha amuna 300 ku Susani, koma sanatenge zinthu zawo.
16 Nawonso Ayuda ena onse amene anali mʼzigawo za mfumu anasonkhana kuti adziteteze.+ Ndipo anapha adani awo+ okwana 75,000 koma sanatenge zinthu zawo. 17 Limeneli linali tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Ndiyeno pa tsiku la 14 anapuma nʼkuchita phwando ndipo anasangalala kwambiri.
18 Ayuda amene anali ku Susani* anasonkhana pa tsiku la 13+ ndi la 14+ la mweziwo. Iwo anapuma pa tsiku la 15 ndipo anachita phwando komanso chikondwerero. 19 Nʼchifukwa chake Ayuda akumidzi amene ankakhala mʼmadera akutali ndi mzinda, anasankha kuti tsiku la 14 la mwezi wa Adara likhale tsiku lachikondwerero, lochita phwando, losangalala+ ndiponso lotumizirana chakudya.+
20 Ndiyeno Moredikayi+ analemba zimene zinachitikazi nʼkutumiza makalata kwa Ayuda onse amene anali mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero, zakutali ndiponso zapafupi. 21 Mʼmakalatawo anawauza kuti pa tsiku la 14 ndi la 15 la mwezi wa Adara azichita chikondwerero chimenechi chaka chilichonse. 22 Anawauza zimenezi chifukwa masiku amenewa Ayuda anasiya kuvutitsidwa ndi adani awo, komanso mʼmwezi umenewu chisoni chawo chinasintha nʼkukhala chikondwerero ndipo tsiku lolira+ linasintha nʼkukhala tsiku losangalala. Masiku amenewa ankayenera kukhala ochita phwando, kusangalala, kutumizirana chakudya ndiponso kupereka mphatso kwa anthu osauka.
23 Ndipo Ayuda anavomereza kuti apitiriza chikondwerero chimene anali atayamba kale komanso achita zimene Moredikayi anawalembera. 24 Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ amene ankadana ndi Ayuda onse, anawakonzera Ayudawo chiwembu kuti awaphe.+ Ndiponso iye anachita Puri+ kapena kuti maere, nʼcholinga choti awasokoneze maganizo nʼkuwapha. 25 Koma Esitere atakaonekera kwa mfumu, mfumuyo inalemba+ lamulo lakuti: “Chiwembu chimene anakonzera Ayuda+ chimubwerere iyeyo.” Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+ 26 Nʼchifukwa chake masiku amenewa anawapatsa dzina lakuti Purimu, kutengera dzina lakuti Puri.*+ Choncho chifukwa cha zonse zomwe zinalembedwa mʼkalatayi, zimene anaona pa nkhani imeneyi komanso zimene zinawachitikira, 27 Ayudawo analonjeza kuti iwo, mbadwa zawo ndiponso anthu onse amene anakhala kumbali yawo,+ azichita chikondwerero masiku awiri amenewa komanso azichita zimene zinalembedwa zokhudza masikuwa pa nthawi yake chaka chilichonse. 28 Mʼbadwo uliwonse uyenera kukumbukira masiku amenewa ndipo zizichitika mʼbanja lililonse, chigawo chilichonse ndiponso mzinda uliwonse. Ayuda sayenera kusiya kukumbukira masiku a Purimu ndipo mbadwa zawo siziyenera kusiya kukumbukira masiku amenewa.
29 Ndiyeno Mfumukazi Esitere, mwana wa Abihaili, komanso Moredikayi Myuda, analemba kalata yachiwiri ndi ulamuliro wonse, kutsimikizira za Purimu. 30 Kenako anatumiza makalata okhala ndi mawu amtendere ndiponso oona kwa Ayuda onse mʼzigawo 127+ zimene Ahasiwero ankalamulira.+ 31 Anatumiza makalatawo kuti atsimikizire kuti azichita chikondwerero cha Purimu pa nthawi yake, mogwirizana ndi zimene Moredikayi Myuda ndi Mfumukazi Esitere anawalamulira kuti azichita.+ Komanso mogwirizana ndi zimene analonjeza kuti Ayudawo ndi mbadwa zawo azichita,+ kuphatikizapo kusala kudya+ komanso kupemphera mochonderera.+ 32 Choncho lamulo la Esitere linatsimikizira nkhani zimenezi zokhudza Purimu+ ndipo zinalembedwa mʼbuku.
10 Mfumu Ahasiwero anayambitsa ntchito ya ukapolo mʼdzikomo ndiponso pazilumba zamʼnyanja.
2 Zinthu zonse zimene anachita chifukwa cha mphamvu zake, ndiponso mphamvu zonse za Moredikayi+ zimene anapatsidwa ndi mfumu,+ zinalembedwa mʼbuku la mbiri+ ya mafumu a Mediya ndi Perisiya.+ 3 Moredikayi Myuda anali wachiwiri kwa Mfumu Ahasiwero. Iye anali wamkulu pakati pa Ayuda ndipo abale ake ambiri ankamulemekeza. Moredikayi ankachitira zabwino anthu a mtundu wake ndipo ankaonetsetsa kuti mbadwa zawo zinthu zidzawayendere bwino.
Anthu amati ameneyu anali Sasita Woyamba, mwana wa Dariyo Wamkulu (Dariyo Hisitasipi).
Kapena kuti, “Kusi.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
“Pofeli” ndi mtundu wa mwala wolimba kwambiri. Kawirikawiri mwala umenewu umaoneka wakuda mofiirira, wokhala ndi mawanga oyera ndipo ndi wamtengo wapatali kwambiri.
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Amatchedwanso Yehoyakini pa 2Mf 24:8.
Kutanthauza “Mtengo wa Mchisu.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “ankamusonyeza chikondi chokhulupirika.”
“Mule” ndi madzi onunkhira ochokera kumitengo inayake ndipo nthawi zina ankapangira mafuta odzola.
Kapena kuti, “adzakazi.”
Onani Zakumapeto B15.
Kapena kuti, “moti inamusonyeza chikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “atsikana.”
Kapena kuti, “mʼdzina la Moredikayi.”
Onani Zakumapeto B15.
Onani Zakumapeto B15.
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente 10,000 asiliva kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu zoti zipite kwa anthu amene adzagwire ntchitoyi.”
Nʼkutheka kuti amanena za siliva amene akatenge akakapha Ayuda.
Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Amenewa ndi mamita pafupifupi 22.3. Onani Zakumapeto B14.
Ena amati “hosi.”
Amenewa ndi mamita pafupifupi 22.3. Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B15.
Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
Onani Zakumapeto B15.
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Onani Zakumapeto B15.
Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Kapena kuti, “Susa.”
Mawu akuti “Puri” amatanthauza “Maere.” Koma kenako mawu akuti “Purimu,” komwe ndi kuchulukitsa, anayamba kuwagwiritsa ntchito ponena za chikondwerero cha Ayuda cha mwezi wa 12 pakalendala yopatulika. Onani Zakumapeto B15.