Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt James 1:1-5:20
  • Yakobo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yakobo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yakobo

KALATA YA YAKOBO

1 Ine Yakobo,+ kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikulembera mafuko 12 amene anamwazikana mʼmadera osiyanasiyana.

Landirani moni!

2 Abale anga, muzisangalala kwambiri pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana,+ 3 chifukwa monga mukudziwira, chikhulupiriro chanu chikakhalabe cholimba pamene mukuyesedwa, mumaphunzira kukhala opirira.+ 4 Koma lolani kuti kupirirako kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda cholakwa pa mbali iliyonse, kapena kuti mukhale ndi makhalidwe onse abwino.+

5 Choncho ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu+ ndipo adzamupatsa,+ chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.*+ 6 Koma azipempha ndi chikhulupiriro,+ asamakayikire ngakhale pangʼono,+ chifukwa amene akukayikira ali ngati funde lapanyanja limene limatengeka ndi mphepo nʼkumawindukawinduka. 7 Munthu wotero asayembekezere kuti adzalandira kanthu kuchokera kwa Yehova.* 8 Iye ndi wokayikakayika+ ndipo zochita zake zonse zimasinthasintha.

9 Mʼbale wonyozeka asangalale* chifukwa walemekezedwa ndi Mulungu,+ 10 ndipo wachuma asangalale chifukwa waphunzira kukhala wodzichepetsa,+ chifukwa mofanana ndi duwa lakutchire, iye adzafota. 11 Dzuwa likatuluka limatentha kwambiri nʼkufotetsa zomera ndipo maluwa a zomerazo amathothoka moti kukongola kwake kumatha. Mofanana ndi zimenezi munthu wachumayo adzafa ali mkati mofunafuna chuma.+

12 Wosangalala ndi munthu amene akupirira mayesero,+ chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto* ya moyo,+ imene Yehova* analonjeza onse amene akupitiriza kumukonda.+ 13 Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Chifukwa Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako chake chimene chimamukopa* ndi kumukola.+ 15 Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabereka tchimo. Ndipo tchimo likachitika, limabweretsa imfa.+

16 Abale anga okondedwa, musasocheretsedwe. 17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba.+ Imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zakuthambo,+ amene sasintha ngati mthunzi umene umasunthasuntha.+ 18 Mwakufuna kwake, iye anatibereka pamene tinakhulupirira mawu ake omwe ndi choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira pa zolengedwa zake.+

19 Abale anga okondedwa, dziwani izi: Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule+ komanso asamafulumire kukwiya,+ 20 chifukwa munthu amene wakwiya sachita zinthu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu.+ 21 Choncho siyani khalidwe lililonse lonyansa ndipo chotsani zoipa zilizonse* zimene zatsalira mwa inu.+ Modzichepetsa vomerezani kuti mawu amene angathe kukupulumutsani adzalidwe mwa inu.

22 Komabe muzichita zimene mawu amanena,+ osati kungomva chabe, nʼkumadzipusitsa ndi maganizo abodza. 23 Chifukwa ngati munthu amangomva mawu koma osachita,+ amafanana ndi munthu amene akudziyangʼanira nkhope yake pagalasi. 24 Iye amadziyangʼana nʼkuchokapo ndipo nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani. 25 Koma amene amayangʼanitsitsa mulamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu ndipo amapitiriza kuliyangʼanitsitsa, adzakhala wosangalala ndi zimene akuchita+ chifukwa chakuti si munthu amene amangomva nʼkuiwala, koma amene amachita zimene wamvazo.

26 Ngati munthu akuganiza kuti amalambira Mulungu,* koma satha kulamulira lilime lake,+ akudzipusitsa* ndipo kulambira kwake nʼkopanda phindu. 27 Kulambira* koyera komanso kosadetsedwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ amene akukumana ndi mavuto*+ komanso kupewa kuti dzikoli likuchititseni kukhala ndi banga.+

2 Abale anga, kodi mukuganiza kuti mukukhulupirira Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ndi waulemerero, pamene mukuchita zokondera?+ 2 Munthu amene wavala mphete zagolide ndi zovala zapamwamba akafika pamsonkhano wanu, ndiye winanso wosauka amene wavala zovala zakuda akafika, 3 kodi mumasangalala ndi amene wavala zovala zapamwamba uja nʼkumuuza kuti, “Khalani pamalo abwinowa” koma wosauka uja nʼkumuuza kuti: “Iwe ubaima choncho,” kapena, “Khala pansipa pafupi ndi chopondapo mapazi anga”?+ 4 Ndiye mukamachita zimenezi, kodi simukusonyeza tsankho pakati panu?+ Ndipo kodi pamenepa simunakhale oweruza amene akupereka zigamulo zoipa?+

5 Tamverani abale anga okondedwa. Kodi Mulungu sanasankhe anthu amene dzikoli limawaona kuti ndi osauka kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro+ komanso kuti akhale oyenera kupatsidwa Ufumu umene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda?+ 6 Koma inu simukulemekeza anthu osauka. Kodi si olemera amene amakuvutitsani+ komanso kukupititsani kumabwalo amilandu? 7 Kodi si omwewo amene amanyoza dzina labwino kwambiri limene munapatsidwa? 8 Ndiye ngati mukutsatira lamulo lachifumu lakuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ ngati mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu. 9 Koma mukapitiriza kukhala okondera,+ mukuchita tchimo ndipo lamulo likusonyezeratu* kuti ndinu olakwa.+

10 Aliyense amene amamvera Chilamulo akalakwitsa mbali imodzi, ndiye kuti walakwira Chilamulo chonse.+ 11 Chifukwa amene ananena kuti, “Musachite chigololo,”+ ananenanso kuti, “Musaphe munthu.”+ Ndiye ngati iwe sunachite chigololo koma wapha munthu, ndiye kuti walakwira chilamulo. 12 Muzilankhula komanso kuchita zinthu ngati anthu amene adzaweruzidwe ndi chilamulo cha anthu amene ali pa ufulu.*+ 13 Chifukwa munthu amene sasonyeza chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.+ Chifundo nʼchachikulu kuposa chiweruzo.

14 Abale anga, kodi pali phindu lanji ngati wina atanena kuti ali ndi chikhulupiriro koma sachita ntchito zake?+ Kodi chikhulupiriro chimenecho chingamupulumutse?+ 15 Ngati mʼbale kapena mlongo alibe zovala* komanso chakudya chokwanira pa tsikulo, 16 koma wina mwa inu nʼkumuuza kuti, “Uyende bwino, upeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene akufunikirazo kuti akhale ndi moyo, kodi pali phindu lanji?+ 17 Chimodzimodzinso chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.+

18 Koma wina anganene kuti: “Iweyo uli ndi chikhulupiriro, koma ine ndili ndi ntchito zake. Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa kudzera muntchito zanga.” 19 Umakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi, si choncho? Ukuchita bwino. Komatu ziwanda nazonso zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera.+ 20 Mbuli iwe, kodi sukudziwa kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nʼchopanda phindu? 21 Kodi Abulahamu atate wathu sanaonedwe kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa?+ 22 Nʼzoonekeratu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo ntchito zakezo zinachititsa kuti chikhulupiriro chakecho chikhale changwiro.+ 23 Choncho lemba linakwaniritsidwa limene limati: “Abulahamu anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza ndipo ankaonedwa kuti ndi wolungama,”+ choncho ankadziwika kuti ndi mnzake wa Yehova.*+

24 Mwaonatu kuti munthu amaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, osati chifukwa cha chikhulupiriro chokha. 25 Mofanana ndi zimenezi, kodi Rahabi amene anali hule uja, sanaonedwenso kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atalandira bwino anthu amene ankafufuza dziko lawo nʼkuwathandiza kuti athawe kudzera njira ina?+ 26 Ndithudi, thupi lopanda mzimu* limakhala lakufa,+ mofanana ndi zimenezi nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.+

3 Abale anga, pasakhale aphunzitsi ambiri pakati panu, podziwa kuti tidzalandira chiweruzo chokhwima.+ 2 Paja tonsefe timapunthwa* nthawi zambiri.+ Ngati munthu sapunthwa pa mawu, ndiye kuti ndi wangwiro ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse. 3 Tikamangirira zingwe pakamwa pa mahatchi kuti azitimvera, timatha kulamuliranso matupi awo onse. 4 Ganiziraninso za ngalawa. Ngakhale kuti ndi zazikulu kwambiri ndipo zimayenda mokankhidwa ndi mphepo zamphamvu, munthu amene akuziyendetsa amaziwongolera ndi thabwa lalingʼono kwambiri kuti zipite kumene iye akufuna.

5 Lilime nalonso ndi kachiwalo kakangʼono, koma limadzitama kwambiri. Taganizirani mmene kamoto kakangʼono kamayatsira nkhalango yaikulu. 6 Lilimenso ndi moto.+ Pa ziwalo zonse za thupi lathu, lilime ndi lodzaza ndi zinthu zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse+ komanso limayatsa moyo wonse wa munthu* ndipo lili ndi moto wa Gehena.* 7 Anthu angathe kuweta mtundu uliwonse wa nyama zakutchire, mbalame, nyama zokwawa ndiponso zamoyo zamʼnyanja ndipo akhala akuchita zimenezi. 8 Koma palibe munthu amene angathe kuweta lilime. Lilime ndi losalamulirika ndipo limavulaza komanso ndi lodzaza ndi poizoni wakupha.+ 9 Lilime timaligwiritsa ntchito potamanda Yehova,* amene ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu amene analengedwa “mʼchifaniziro cha Mulungu.”+ 10 Pakamwa pamodzi pomwepo pamatuluka mawu otamanda komanso otemberera.

Abale anga, nʼzosayenera kuti zinthu zizichitika mwa njira imeneyi.+ 11 Kodi kasupe angatulutse madzi abwino* komanso madzi owawa padzenje limodzi? 12 Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu ungabereke maolivi, kapena kodi mtengo wa mpesa ungabereke nkhuyu?+ Ngakhale kasupe wa madzi amchere sangatulutse madzi abwino.

13 Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu? Ngati alipo asonyeze zimenezi pochita zinthu zabwino pa moyo wake. Azichita zinthu zonse mofatsa, lomwe ndi khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru. 14 Koma ngati mʼmitima yanu muli nsanje yaikulu+ ndi kukonda mikangano,*+ musadzitame+ chifukwa kuchita zimenezo nʼkunamizira choonadi. 15 Imeneyi si nzeru yochokera kumwamba, koma ndi yapadziko lapansi,+ yauchinyama ndiponso yauchiwanda. 16 Chifukwa pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano,* pamakhalanso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.+

17 Koma nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+ 18 Komanso, chilungamo ndi chipatso chimene anthu obweretsa mtendere+ amafesa mumtendere.+

4 Kodi nkhondo ndi ndewu zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Kodi sizikuchokera mʼzilakolako za thupi lanu zimene zikulimbana kuti zizilamulira matupi anu?*+ 2 Mumalakalaka, koma simulandira zimene mukulakalakazo. Mukupitiriza kupha anthu ndiponso mumasirira mwansanje koma simupeza kanthu. Mukupitiriza kukangana komanso kuchita nkhondo.+ Simunalandire chifukwa chakuti simunapemphe. 3 Mukapempha, simulandira chifukwa mumapempha ndi cholinga choipa, kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.

4 Achigololo inu,* kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko nʼkudziika pa udani ndi Mulungu? Choncho aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzipangitsa kuti akhale mdani wa Mulungu.+ 5 Kapena kodi mukuganiza kuti lemba limanena popanda chifukwa kuti: “Mzimu umene wakhazikika mwa ife umalakalaka mwansanje zinthu zosiyanasiyana”?+ 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli. Nʼchifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikuza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+

7 Choncho gonjerani Mulungu,+ koma tsutsani Mdyerekezi+ ndipo adzakuthawani.+ 8 Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu+ okayikakayika inu. 9 Imvani chisoni ndipo lirani.+ Kuseka kwanu kusanduke kulira ndipo chisangalalo chanu chisanduke chisoni. 10 Dzichepetseni pamaso pa Yehova*+ ndipo iye adzakukwezani.+

11 Abale, musiye kunenerana zoipa.+ Aliyense amene akunenera zoipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akunenera zoipa komanso kuweruza lamulo. Ndiye ngati ukuweruza lamulo, sukuchita zimene lamulo limanena koma ndiwe woweruza. 12 Komatu Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha,+ amenenso akhoza kupulumutsa ndi kuwononga.+ Ndiye iwe ndiwe ndani kuti uziweruza mnzako?+

13 Tamverani inu amene mumanena kuti: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko nʼkupeza phindu.”+ 14 Mumanena zimenezi chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Chifukwa muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa kenako nʼkuzimiririka.+ 15 Mʼmalomwake muzinena kuti: “Yehova* akalola,+ tikhala ndi moyo ndipo tichita zakutizakuti.” 16 Koma inu mumakonda kunyada komanso kudzitama. Kudzitama konse koteroko ndi koipa. 17 Choncho ngati munthu akudziwa kuchita chabwino koma sakuchichita, akuchimwa.+

5 Tamverani inu anthu achuma. Lirani mofuula chifukwa cha masautso amene akubwera kwa inu.+ 2 Chuma chanu chawola ndipo zovala zanu zadyedwa ndi njenjete.*+ 3 Golide ndi siliva wanu wawonongeka ndi dzimbiri. Dzimbiri limenelo lidzakhala umboni wokutsutsani ndipo lidzadya mnofu wanu. Zimene mwasunga zidzakhala ngati moto mʼmasiku otsiriza.+ 4 Tamverani! Malipiro amene simunapereke kwa anthu amene anagwira ntchito yokolola mʼminda yanu akufuula ndipo Yehova* wa magulu ankhondo akumwamba wamva kufuula kopempha thandizo kwa anthu okololawo.+ 5 Mwakhala moyo wa mwanaalirenji ndipo dziko lapansi mwalidyerera. Mwadya ndipo mwanenepa ngati nyama pa tsiku limene ikukaphedwa.+ 6 Mwaweruza ndiponso kupha munthu wolungama. Iye akukutsutsani.

7 Choncho lezani mtima abale, mpaka kukhalapo kwa Ambuye.+ Ganizirani mmene mlimi amachitira. Iye amayembekezerabe zipatso zamtengo wapatali zochokera munthaka. Amayembekezera moleza mtima mpaka mvula yoyamba komanso mvula yomaliza itagwa.+ 8 Inunso khalani oleza mtima.+ Limbitsani mitima yanu, chifukwa kukhalapo kwa Ambuye kwayandikira.+

9 Musamadandaule za ena* abale, kuti musaweruzidwe.+ Taonani, Woweruza waima pakhomo. 10 Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula mʼdzina la Yehova.*+ 11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawaona kuti ndi odala.*+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mukudziwa madalitso amene Yehova* anamupatsa.+ Mukuona nokha kuti Yehova* ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.+

12 Koma koposa zonse abale anga, siyani kulumbira, potchula kumwamba kapena dziko lapansi kapena lumbiro lina lililonse. Koma mukati “Inde,” azikhaladi inde ndipo mukati “Ayi,” azikhaladi ayi+ kuti musakhale oyenera kuweruzidwa.

13 Kodi pali aliyense amene akukumana ndi mavuto pakati panu? Apitirize kupemphera.+ Kodi pali aliyense amene akusangalala? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.+ 14 Kodi pali aliyense amene akudwala pakati panu? Aitane akulu+ a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka+ mafuta mʼdzina la Yehova.* 15 Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu amene akudwalayo* ndipo Yehova* adzamulimbitsa. Komanso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.

16 Choncho muululirane machimo anu poyera+ ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe. Pemphero lopembedzera la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.*+ 17 Eliya anali munthu ngati ife tomwe, komabe atapemphera kuchokera pansi pamtima kuti mvula isagwe, mvula sinagwedi mʼdzikolo kwa zaka zitatu ndi miyezi 6.+ 18 Kenako anapempheranso ndipo mvula inagwa kuchokera kumwamba moti nthaka inatulutsa zipatso zake.+

19 Abale anga, ngati wina pakati panu wasiya choonadi chifukwa chosocheretsedwa, ndiye munthu wina nʼkumubweza, 20 dziwani kuti amene wabweza wochimwayo panjira yake yoipa,+ wamupulumutsa ku imfa ndipo Mulungu adzakhululukira wochimwayo machimo ambiri.+

Kapena kuti, “amapereka popanda kupezera aliyense zifukwa.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzitamandire.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “chimamukopa ngati nyambo.”

Mabaibulo ena amati, “zoipa zambirimbiri.”

Kapena kuti, “ndi wopembedza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akupusitsa mtima wake.”

Kapena kuti, “Chipembedzo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasautso awo.”

Kapena kuti, “ndipo lamulo likukutsutsani.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chilamulo cha ufulu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ali maliseche.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “mpweya.”

Kapena kuti, “timalakwitsa zinthu.”

Kapena kuti, “limayatsa chilichonse chimene akuchita pa moyo wake.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “okoma.”

Mabaibulo ena amati, “ndi mtima wodzikonda.”

Mabaibulo ena amati, “mtima wodzikonda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwalo zanu.”

Kapena kuti, “Anthu osakhulupirika inu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “Musamangʼungʼudze za ena.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “osangalala.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mabaibulo ena amati, “amene watopayo.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “limakhala lamphamvu kwambiri pamene likugwira ntchito.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena